Mutu 15

1Pamenepo alembi ndi Afarisi ochokera ku Yerusalemu anabwera kwa Yesu, nanena, 2Chifukwa chiyani ophunzira anu amaphwanya lamulo limene linaikidwa ndi makolo akale? Pakuti iwo sasamba m’manja mwao pamene akudya mkate. 3Koma Iye poyankha anati kwa iwo, Chifukwa chiyaninso inu mumaphwanya lamulo la Mulungu1 potsata chiphunzitso cha miyambo yanu? 4Pakuti Mulungu2 analamulira nanena, Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo, iye wolankhulira atate wake ndi amake zoipa, aphedwe. 5Koma inu munena, Aliyense amene adzanena kwa atate wake kapena amake, Imeneyi ndi mphatso, chilichonse chimene [chizalandiridwa] kuchoka kwa Ine sichidzakupindulirani: 6ndipo mwanjira ina iliyonse salemekeza atate wake ndi amake; ndipo mwapeputsa lamulo la Mulungu3 potsata chiphunzitso cha miyambo yanu. 7Onyenga inu! Mneneri Yesaya analosera bwino lomwe zokhudza inu, ponena kuti, 8Anthu awa andilemekeza ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ili kutali ndi Ine; 9komatu andilambira Ine kwachabe, kuphunzitsa [monga] maphunzitso a malamulo a anthu. 10Ndipo anadziitanira [Iye] khamu, nanena nawo, Imvani ndipo mumvetsetse: 11Sikuti chimene chimalowa mkwamwa mwa munthu chimamuipitsa munthuyo; koma chimene chimatuluka mkamwa mwa munthu ndi chomwe chimamuipitsa.

12Pamenepo ophunzira ake, anabwera, nanena kwa Iye, Kodi simukudziwa kuti Afarisi, pakumva mau amenewa, akhumudwa nawo? 13Koma Iye poyankha anati, Mbewu iliyonse imene Atate wanga wakumwamba sanaidzale izadzulidwa. 14Alekeni choncho; iwowa ndi atsogoleri akhungu: koma ngati wakhungu atsogolera wakhungu, onsewa adzagwera m’mbuna. 15Ndipo Petro pakuyankha ananena kwa Iye, Titanthauzireni fanizo limeneli. 16Koma Iye anati, Kodi inunso muli opanda nzeru? 17Simudziwa kodi, kuti chilichonse cholowa mkamwa chimapita m’mimba, ndipo chimatayidwa kuthengo? 18Koma zinthu zonse zimene zimatuluka m’kamwa zimachokera mu mtima, ndipo zimenezi ndizo zimaipitsa munthu. 19Pakuti mu mtima mumachokera malingaliro oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, zochitira umboni wabodza, zamwano; 20zimenezi ndi zinthu zimene zimaipitsa munthu.

21Ndipo Yesu, pakupita kuchokera kumeneko, anapita mbali za ku Turo ndi Sidoni; 22ndipo taonani, mzimayi wa ku Kanani, akuchokera ku malire amenewo, anafuula [kwa iye] nanena, ndichitireni chifundo ine, Ambuye, Mwana wa Davide; mwana wanga wagwidwa koopsa ndi ziwanda. 23Komatu Iye sanamuyankhe kanthu mzimayiyu. Ndipo ophunzira ake anadza kwa [iye] namfunsa, nati, M’chotseni uyu, pakuti akulilira kumbuyo kwathu. 24Koma Iye pakuyankha anati, Inetu sindinatumidwe koma kudzapulumutsa nkhosa zosokera za m’nyumba ya Israyeli. 25Komatu iye anadza namlambira, nanena, Ambuye, ndithandizeni. 26Koma Iye poyankha anati, Sikoyenera kutenga mkate wa ana ndi kuponyera agalu. 27Koma iye anati, Indetu, Ambuye; pakuti ngakhale agalu amadya nyenyetswa zimene zikugwa kuchokera pa gome la mbuye wawo. 28Pamenepo Yesu poyankha ananena kwa iye, Mzimayi iwe, chikhulupiriro chako, [ndi] chachikulu. Zikhale momwemo kwa iwe monga ufuna. Ndipo mwana wake wa mkazi anachiritsidwa kuchokera nthawi yomweyo.

29Ndipo Yesu, pakuchoka kumeneko, anafika mbali ya kufupi ndi nyanja ya Galileya, ndipo anakwera ku phiri nakhala pansi kumeneko; 30ndipo makamu a anthu anabwera kwa Iye, ali nawo anthu olumala miyendo, osaona, osalankhula, opuwala ziwalo, ndi ena ambiri, ndipo anawaika pa mapazi ake, ndipo Iye anawachiritsa iwo: 31kotero makamu a anthu anali ozizwa poona osalankhula akulankhula, opuwala ziwalo akuchiritsidwa, olumala miyendo akuyenda, ndi osaona akuona; ndipo iwo analemekeza Mulungu4 wa Israyeli. 32Koma Yesu atadziyitanira ophunzira ake kwa [Iye], anati, Ine ndili ndi chifundo ndi khamuli, chifukwa akhala ali ndi Ine kwa masiku atatu tsopano ndipo alibe chakudya chili chonse kuti adye, ndipo sindingawachotse kuno iwo asanadye kuopa kuti angakomoke panjira. 33Ndipo ophunzira ake anati kwa Iye, Kodi tikapeza kuti mikate yochuluka muno m’chipululu imene ikhoza kukwanira khamu lalikulu lotere? 34Ndipo Yesu anati kwa iwo, Kodi muli ndi mikate ingati? Koma iwo anati, Isanu ndi iwiri, komanso nsomba zochepa. 35Ndipo Iye analamulira makamuwo kuti akhale pansi; 36ndipo atatenga mikate isanu ndi iwiri ndi nsombazo, anayamika, nainyema [iyo] ndipo anaipereka [iyo] kwa ophunzira ake, ndipo ophunzira anaipereka kwa khamulo. 37Ndipo onse anadya nakhuta; ndipo anasonkhanitsa makombo otsala ndipo anakwanira mitanga yodzadza isanu ndi iwiri; 38koma iwo amene anadya anali amuna zikwi zinayi, osaphatikizapo akazi ndi ana. 39Ndipo, atawachotsa makamu aja, Iye anakwera m’ngalawa ndipo anafika ku malire a Magadani.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu