Mutu 9
1Ndipo mngelo wachisanu anaomba lipenga [lake]: ndipo ndinaona nyenyezi ikuchoka kumwamba kugwera padziko lapansi; ndipo inapatsidwa chifungulo cha dzenje la phompho. 2Ndipo anatsegula dzenje la phompholo; ndipo panatuluka utsi kuchokera m’dzenjemo monga utsi wa ng’anjo yaikulu; ndipo dzuwa ndi mpweya zinadetsedwa ndi utsi ochokera m’dzenjemo. 3Ndipo kuchokera mu utsimo munatuluka dzombe padziko lapansi, ndipo mphamvu inapatsidwa kwa iwo monga zinkhanira padziko lapansi zili ndi mphamvu; 4ndipo analankhula kwa izo, kuti zisaononge udzu wadziko lapansi, kapena chilichonse chobiriwira, kapena mtengo uliwonse, koma anthu amene alibe chizindikiro cha Mulungu1 pa mphumi pawo: 5ndipo kunapatsidwa kwa iwo kuti asaziphe izo, koma kuti azunzidwe miyezi isanu; ndipo chizunzo chawo chinali chonga ululu wa chinkhanira chikaluma munthu. 6Ndipo masiku amenewo anthu adzafuna imfa, ndipo mwanjira iliyonse sadzaipeza; ndipo adzafunitsitsa kufa, ndipo imfa idzawathawa. 7Ndipo kufanana kwa dzombe [kunali] ngati akavalo kukonzekera ku nkhondo; ndipo pamutu pawo monga korona wa golide, ndipo nkhope zawo ngati nkhope za anthu; 8ndipo anali ndi tsitsi ngati tsitsi la mzimayi, ndipo mano awo anali a mikango, 9ndipo anali nazo zoteteza pachifuwa ngati za chitsulo, ndipo phokoso la mapiko awo linali ngati phokoso la magareta a akavalo kuthamangira ku nkhondo; 10ndipo anali nayo michira ngati ya zinkhanira, ndipo zimaluma; ndipo mphamvu yawo [inali] ku michira kwao kupweteka anthu miyezi isanu. 11Anali nayo mfumu ya kuwalamulira iwo, mngelo wa ku phompho: dzina la m’Chiheberi, Abadoni, ndipo m’Chihelene ali nalo dzina Apoliyoni.
12Tsoka loyamba lapita. Taonani, kukubwera matsoka ena awiri pakupita zinthu izi.
13Ndipo mngelo wachisanu ndi chimodzi anaomba lipenga [lake]: ndipo ndinamva mau kuchokera ku nyanga zinayi za guwa la golide limene lili pamaso pa Mulungu2, 14nanena kwa mngelo wa chisanu ndi chimodzi amene anali ndi lipenga, Umasule angelo anayi amene amangidwa ku mtsinje waukulu wa Firate. 15Ndipo angelo anayiwo anamasulidwa, amene ali okonzekera pa ola lake ndi tsiku ndi mwezi ndi chaka, kuti akaphe gawo lachitatu la anthu; 16ndipo chiwerengero cha ankhondo a pangamira [chinali] zikwi makumi awiri zochulukitsa zikwi khumi. Ndinamva chiwerengero chao.
17Ndipo pamenepo ndinaona akavalo m’masomphenya, ndipo iwo akukhala pa iwo, okhala ndi zoteteza pachifuwa za moto ndi huakinto ndi sulfure. 18Mwa milili itatu imeneyi panali gawo lachitatu la anthu amene anaphedwa, ndi moto ndi utsi ndi sulfure amene anatuluka m’kamwa mwao. 19Pakuti mphamvu ya akavalo ili mkamwa mwao ndi kumichira kwao: pakuti michira yawo ili ngati njoka, yokhala ndi mitu, ndipo ndi imeneyi anapwetekedwa. 20Ndipo anthu otsalawo amene sanaphedwe ndi milili imeneyi sanalape ku ntchito za manja awo, kuti asalambire ziwanda, komanso mafano a golide ndi a siliva ndi a mkuwa ndi a mwala ndi a mtengo, amene sangapenye kapena kuyenda. 21 Ndipo iwo sanalape ku kupha kwao, kapena ufiti wao, kapena chigololo chao, kapena kuba kwao.
1Elohimu2Elohimu