Mutu 3

1Mauwa ali okhulupirika: ngati aliyense asilira kukhala woyang’anira, akhumba ntchito yabwino. 2Woyang’anira akhale wopanda banga, mwamuna wa mkazi m’modzi, wodziletsa, wanzeru, wolongosoka, wosamalira alendo, wokhoza kuphunzitsa; 3wosadzipereka kukuledzera vinyo, wopanda ndeu, koma wofatsa, osati wokonda mikangano, wosakondetsetsa chuma, 4woyang’anira bwino nyumba yake, kukhala nawo ana ake omvera ndi uzimu onse; 5(koma ngati wina sadziwa kuyang’anira bwino nyumba yake, adzayang’anira bwanji mpingo wa Mulungu1?) 6asakhale mwana mu uzimu, kuti asadzitukumule, nkugwa m’mayesero a mdierekezi. 7koma ndi kofunikira kutinso akhale ndi umboni wabwino kuchokera kwa akunja, kuti asakagwe m’manyazi ndi mumsampha wa mdierekezi. 8Atumiki, momwemonso, asamalitse, osanena pawiripawiri, asadzipereke kwambiri ku vinyo, asafune phindu mnjira yachabe, 9kusunga chinsinsi cha chikhulupiliro mu chikumbumtima changwiro. 10Ndipo amenewa avomerezedwe koyamba, kenako aloleni atumikire, pokhala alibe mlandu [wotsutsana nawo]. 11Akazi chimodzimodzinso asamalitse, asakhale amabodza, azisunge, akhulupirike mu zinthu zonse. 12Atumiki akhale amuna amene ali ndi mkazi m’modzi, oyang’anira bwino ana awo ndi nyumba zawo: 13kwa iwo amene adzatumikira bwino azadzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukulu m’chikhulupiliro chimene chili mwa Khristu Yesu. 14Zinthu izi ndilembera kwa iwe, pokhala ndili ndi chiyembekezo kuti ndibwera kwa iwe mwachangu; 15koma ngati ndichedwa, cholinga n’choti udziwe momwe munthu akuyenera kukhalira m’nyumba ya Mulungu2, omwe ndi mpingo wa Mulungu3 wa moyo, mzati ndi maziko a choonadi. 16 Ndipo povomereza chinsinsi cha ulemelero n’chachikulu. °Mulungu4 waonetsedwa mthupi, walungamitsidwa mu Mzimu, waonekera kwa angelo, walalikidwa pakati pa amitundu, wakhulupiridwa m’dziko lapansi, walandiridwa mu ulemelero.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu