Mutu 4

1Zitapita zinthu izi ndinaona, ndipo taonani, khomo lotseguka m’mwamba, ndipo mau oyamba omwe ndinamva anali ngati lipenga kulankhula ndi ine, nanena, Kwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa iwe zinthu zimene zidzachitike zitapita izi.

2Nthawi yomweyo ndinakhala mu Mzimu; ndipo taonani, mpando wachifumu unayima m’mwamba, ndipo pa mpandopo panakhala wina, 3ndipo iye wakukhalapo anaoneka ngati mwala wa jaspi ndi sardiyo, ndi utawaleza kuzungulira mpando wachifumu maonekedwe ngati emaraidi. 4Ndipo pozungulira mpando wachifumu panali mipando ya chifumu makumi awiri mphambu inayi, ndipo pa mipando ya chifumuyo panali akulu makumi awiri ndi mphambu anayi atakhalapo, atavala zovala zoyera; ndipo pa mitu pawo panali makorona a golide. 5Ndipo kutuluka pa mpando wa chifumu panali ziphaliwali, ndi mau, ndi mabingu; ndipo nyali zisanu ndi ziwiri za moto, zikuyaka pa mpando wa chifumuwo, ndiyo Mizimu ya Mulungu1 isanu ndi iwiri; 6ndipo pa mpandopo, pooneka monga nyanja ya mandala, monga kunyezimira. Ndipo mkatikati mwa mpandowo, ndi kuzungulirapo, zamoyo zinayi, zodzala ndi maso, kutsogolo ndi kumbuyo; 7ndipo cholengedwa choyamba chonga mkango, ndi chachiwiri chonga mwana wa ng’ombe, ndipo cholengedwa chamoyo chachitatu chokhala nayo nkhope monga munthu, ndipo cholengedwa chachinayi chonga nkhwazi yowuluka. 8Ndipo cholengedwa chamoyo chachinayi, chilichonse chokhala nawo mapiko asanu ndi limodzi; pozinga ponse ndi mkati zodzala ndi maso; ndipo zosatopa usana ndi usiku kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu2 Wamphamvu zonse, amene anali, ndipo ali, ndipo ali nkudza. 9Ndipo pamene zolengedwa za moyo zipereka ulemelero ndi ulemu ndi matamando kwa iye amene akhala pa mpando wachifumu, amene akhala ndi moyo ku nthawi za nthawi, 10akulu makumi awiri ndi mphambu anayi amagwa pamaso pa iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kumlambira iye amene akhalabe ku nthawi za nthawi; ndipo aponya pansi makorona awo pa mpando wachifumu, nanena, 11Mwayenera inu, Ambuye wathu ndi Mulungu3 [wathu], kulandira ulemelero ndi ulemu ndi mphamvu; pakuti inu munalenga zinthu zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhalapo, ndipo zinalengedwa izo.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu