Mutu 6

1Komatu m’masiku amenewo, ophunzira pochulukana m’chiwerengero, panabuka chidandaulo cha Ahelene motsutsana ndi Aheberi chifukwa amasiye awo amasalidwa pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku. 2Ndipo khumi ndi awiriwo, podziitanira okha unyinji wa ophunzira, anati, Sikoyenera kuti ife, tisiye mau a Mulungu1, ndi kutumikira pa magome. 3Pamenepo tafufuzani, abale, pakati panu amuna asanu ndi awiri, a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu Woyera ndi nzeru, amene tiwakhazikitse pa ntchito imeneyi: 4komatu ifeyo tidzipereke tokha ku pemphero ndi utumiki wa mau. 5Ndipo kulankhulaku kunasangalatsa khamu lonse: ndipo iwo anasankha Stefano, munthu wodzala ndi chikhulupiliro komanso Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanora, ndi Timoni, ndi Parmena, ndi Nikolao, wopinduka waku Antiokeya, 6amene anawayika pamaso pa atumwi; ndipo, atapemphera, anayika manja pa iwo. 7Ndipo mau a Mulungu2 anachulukira; ndipo chiwerengero cha ophunzira m’Yerusalemu chinachuluka kwambiri, ndipo khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupilirocho.

8Ndipo Stefano, wodzala ndi chisomo ndi mphamvu, anachita zozizwa ndi zizindikiro zazikulu pakati pa anthu.

9Ndipo anauka ena a m’sunagoge odzitcha anthu omasulidwa, ndi aku Kurene, ndi aku Alesandriyo, ndi aku Kilikiya ndi Asiya, kutsutsana naye Stefano. 10Ndipo iwo sanakwanitse kutsutsana ndi nzeru komanso Mzimu amene iye amalankhula. 11Pamenepo iwo anamemeza anthu, nanena, Ife tamumva uyu akulankhula mau achipongwe kutsutsana ndi Mose komanso Mulungu3. 12Ndipo iwo anautsa anthu, ndi akulu, ndi alembi. Ndipo anabwera pa [iye[ namgwira ndi kumpititsa kubwalo la akulu. 13Ndipo iwo anakhazikitsa mboni zabodza, nanena, Munthu uyu sakusiya kulankhula motsutsana ndi malo oyera komanso chilamulo; 14pakuti ife tinamumva iye akunena, Yesu uyu Mnazarayo adzapasula malo awa, ndipo adzasintha miyambo imene Mose anatiphunzitsa ife. 15Ndipo onse amene anakhala pa bwalo la akulu, anamyang’anitsitsa iye, naona nkhope yake ikuoneka ngati ya mngelo.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu