Mutu 19
1Pamenepo Pilato anamtenga Yesu ndi kumkwapula [Iye]. 2Ndipo asilikali pamene analuka chisoti cha ufumu chaminga anachiveka pamutu pake, ndiponso anamveka mwinjiro wa chibakuwa, 3ndipo anabwera kwa Iye nati, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda! Ndipo anam’menya Iye zibakera ku nkhope. 4Ndipo Pilato anatulukanso nati kwa iwo, Taonani, ndim’bweretsa Iye kwa inu, kuti mudziwe sindinapeze cholakwa china chilichonse mwa Iye. 5(Pamenepo Yesu anatuluka panja, atavekedwa chisoti cha chifumu chaminga, ndi mwinjiro wa chibakuwa.) Ndipo iye anati kwa iwo, Taonani munthuyu! 6Pamene ansembe akulu ndi asilikali anamuona Iye anafuula nati, Mpachikeni, mpachikeni [Iye]. Pilato anati kwa iwo, Mtengeni inuyo ndipo mpachikeni [Iye], pakuti sindikupeza cholakwa chilichonse mwa Iye. 7Ayuda anamuyankha iye, Ife tili nalo lamulo, ndipo molingana ndi lamulo [lathu] akuyenera kufa, chifukwa anaziyesa yekha Mwana wa Mulungu1.
8Pamene Pilato anamva mau awa, anachita mantha, 9ndipo analowanso m’bwalo la milandu nanena kwa Yesu, Kodi ukuchokera kuti? Koma Yesu sanamuyankhe kanthu. 10Pamenepo Pilato anati kwa Iye, Kodi sukulankhula kanthu kwa ine? Kodi sukudziwa kuti ine ndili nawo ulamuliro wokumasula Iwe ndiponso ulamuliro wokupachika Iwe? 11Yesu anayankha, Inu simukanakhala nawo ulamuliro uliwonse pa Ine pakanakhala kuti sunaperekedwe kwa inu kuchokera kumwamba. Pachifukwa ichi amene wandipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo lalikulu. 12Kuyambira nthawi imeneyo Pilato anafuna kum’masula Iye; koma Ayuda anafuula nati, Ngati mungam’masule [munthu] uyu ndiye kuti sindinu bwenzi la Kaisara. 13Pamenepo Pilato, atamva mau amenewa, anatuluka naye Yesu ndipo anakhala pa mpando wa chiweruzo, pamalo otchedwa Bwalo la Miyala, koma m’Chiheberi Gabata; 14(tsopano kunali chikonzero cha Pasaka; ndipo linali ngati ola lachisanu ndi chimodzi;) ndipo iye anati kwa Ayuda, Taonani mfumu yanu! 15Koma iwo anafuula, Mchotseni [Iye], mchotseni [Iye], mpachikeni. Pilato anati kwa iwo, Kodi ndipachike mfumu yanu? Ansembe akulu anayankha, Tilibe mfumu yina koma Kaisara. 16Pamenepo anampereka Iye kwa iwo, kuti apachikidwe; ndipo iwo anamtenga Iye.
17Ndipo Iye anatuluka, atasenza mtanda wake, napita kumalo otchedwa [malo] a bade, amene m’Chiheberi amatchedwa, Gologota; 18kumene anampachika Iye, ndipo pamodzi naye anapachikanso ena awiri, [m’modzi] mbali ina, ndi [wina] mbali inayo, ndipo Yesu anapachikidwa pakati. 19Ndipo Pilato analembanso lemba ndipo analiyika pa mtandapo. Komatu panalembedwa pamenepo: Yesu Mnazarayo, Mfumu ya Ayuda. 20Pamenepo lemba limeneli Ayuda ambiri analiwerenga, pakuti malo a mzinda pamene Yesu anapachikidwapo anali powandikira; ndipo analembedwa m’Chiheberi, m’Chiherene, ndi m’Chiroma. 21Pamenepo ansembe akulu a Ayuda anati kwa Pilato, Musalembe kuti, Mfumu ya Ayuda, koma kuti Iye anati, Ndine Mfumu ya Ayuda. 22Pilato anayankha, Chimene ndalemba, ndalemba. 23Pamenepo asilikali, pamene anampachika Yesu, anatenga zovala zake, ndipo anazidula magawo anayi, msilikali aliyense anatenga gawo lake, ndi malaya; koma malayawo anali wopanda msoko, wosokedwa onse kuchokera kumwamba mpaka pansi. 24Pamenepo iwo anati kwa wina ndi mzake, Tiyeni tisawang’ambe, koma tichite mayere pa iwo, kuti adzakhala a ndani; kuti lemba likwaniritsidwe limene likuti, Anang’amba zovala zanga pakati pawo, ndipo pa malaya anga anachita mayere. Pamenepo asilikali anachita zinthu zonse izi.
25Ndipo pafupi ndi mtanda wa Yesu panayima mayi wake, ndi m’bale wa mayi wake, Mariya [mkazi] wa Kleopa, ndi Mariya wa Magadala. 26Pamenepo Yesu, poona mayi wake, ndi ophunzira atayima pambali pake, amene Iye anamkonda, anati kwa mayi wake, Mkazi, taona mwana wako. 27Pamenepo Iye anati kwa wophunzirayo, Taona mayi wako. Ndipo kuyambira ola limenelo wophunzira uja anawatengera mayi wake kunyumba kwake. 28Zitapita izi, Yesu, podziwa kuti zinthu zonse zatha tsopano, kuti lemba likwaniritsidwe, anati, Ndikumva ludzu. 29Panali chotengera pamenepo chodzadza ndi vinyo wosasa, ndipo ataviika chinkhupule chodzala ndi vinyo wosasa, ndi kuyika pa phesi la hisope, anayika pakamwa pake. 30Pamene Yesu analandira vinyo wosasayo, anati, Kwatha; ndipo ataweramitsa mutu wake, anapereka mzimu wake.
31Pamenepo Ayuda, kuti thupi lisakhalebe pa mtanda pa tsiku la sabata, pakuti linali tsiku lokonzekera sabata, (pakuti tsiku la sabata linali [tsiku] lalikulu,) anapempha kwa Pilato kuti miyendo yawo ithyoledwe, ndipo achotsedwe. 32Pamenepo asilikali anabwera ndi kuthyola poyamba miyendo ya iwo amene anakhomedwa pamodzi ndi Iye; 33koma pakufika kwa Yesu, pamene iwo anaona kuti anali atafa kale sanathyole miyendo yake, 34koma m’modzi wa asilikali anam’baya ndi mkondo mu nthiti mwake, ndipo nthawi yomweyo munatuluka mwazi ndi madzi. 35Ndipo iye amene anaona ichi achitira umboni, ndipo umboni wake ndi owona, ndipo iye akudziwa kuti akunena zoona kuti inuyo mukakhulupilire. 36Pakuti zinthu zimenezi zinachitika kuti lemba likakwaniritsidwe, Fupa lake silinathyoledwe. 37Ndiponso lemba lina linena, Iwo adzayang’ana pa Iye amene anam’baya.
38Ndipo zitapita izi Yosefe waku Arimateya, amene anali wophunzira wa Yesu, koma mwa chinsinsi poopa Ayuda, anamupempha Pilato kuti atenge thupi la Yesu: ndipo Pilato anavomera ichi. Pamenepo iye anabwera ndi kutenga thupi la Yesu. 39Ndipo Nikodemonso, amene anabwera poyamba kwa Yesu usiku, anabwera, atatenga mure wosakaniza ndi aloe, pafupifupi miyeso zana [kulemera kwake]. 40Pamenepo iwo anatenga thupi la Yesu ndipo analikulunga mu nsalu ya bafuta ndi zonunkhira, monga chili chikhalidwe cha Ayuda pokonzekera kuyika maliro. 41Komatu panali munda pamalo pamene Iye anapachikidwapo, ndipo m’munda m’menemu munali manda atsopano amene simunayikidwemo munthu wina aliyense. 42Pamenepo, pa chifukwa cha chikonzero cha Ayuda, pakuti manda anali pafupi, iwo anamuyika Yesu.
1Elohimu