Mutu 5
1Koma munthu wina, dzina lake Hananiya, ndi Safira mkazi wake, anagulitsa munda, 2ndipo anadzipatulira yekha gawo lina la mtengo, mkazi [wake] anadziwanso ichi; ndipo atabweretsa gawo lina, analiyika pamapazi pa atumwi. 3Koma Petro anati, Hananiya, Chifukwa chiyani Satana wadzadza mtima wako kuti unamize Mzimu Woyera, ndipo wadzipatulira wekha gawo lina la mtengo wa munda? 4Pamene unali nawo sunali wako kodi? Ndipo utagulitsa, sunali mu mphamvu yako kodi? Chifukwa chiyani iwe walowetsa chinthu ichi mu mtima mwako? Iwetu sunanamize anthu, koma Mulungu1. 5Ndipo Hananiya, pakumva mau awa, anagwa pansi ndi kumwalira. Ndipo mantha akulu anagwira iwo onse amene anamva [ichi]. 6Ndipo anyamata, ananyamuka, namkulunga kuti akayikidwe m’manda, ndipo atamunyamula iye, anakayikidwa m’manda.
7Ndipo kunachitika kuti atatha pafupifupi maola atatu, kuti mkazi wake, posadziwa chimene chinachitika, analowa. 8Ndipo Petro ananena naye, Tandiuza ngati munagulitsa mundawo pa mtengo wakuti? Ndipo iye anati, Inde, pa mtengo wakuti. 9Ndipo Petro anati kwa iye, Chifukwa chiyani mwagwirizana kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi a iwo amene ayika mwamuna wako m’manda ali pakhomo, ndipo adzakutenga iwe. 10Ndipo nthawi yomweyo anagwa pansi pamapazi pake namwalira. Ndipo pamene anyamata analowa anampeza iye atamwalira; ndipo, anamtengera iye panja, namuyika pafupi ndi mwamuna wake.
11Ndipo mantha anadza pa mpingo wonse, ndi onse amene anamva zinthu izi. 12Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zinachitika pakati pa anthu; (ndipo iwo onse anali ndi mtima umodzi m’khumbi la Solomo, 13koma palibe m’modzi wa otsalawo analimba mtima kuphatikana nawo, koma anthu anawakweza iwo; 14ndipo okhulupilira anawonjezeka kwa Ambuye kuposa kale, khamu la amuna ndi akazi omwe;) 15kotero kuti anabweretsa odwala m’misewu ndipo anawayika [iwo] pa makama ndi pa mphasa, kuti chithunzi chokha cha Petro, podutsa, chiphimbe m’modzi wa iwo. 16Ndiponso khamu lalikulu la mu mzindamo ndi lozungulira linabwera ku Yerusalemu, linabweretsa anthu odwala komanso anthu ogwidwa ndi mizimu yoipa, amene onse anachiritsidwa.
17Ndipo poyimilira mkulu wa ansembe, ndi onse amene anali naye pamodzi, ndiwo a chipatuko cha Asaduki, anadzala ndi mkwiyo, 18ndipo anawagwira atumwiwo nawatsekera m’ndende ya anthu wamba. 19Koma mngelo wa Ambuye usiku anatsegula zitseko za ndendeyo, nawatulutsa onse, nanena, 20Pitani ndipo mukayimilire ndi kulankhula m’kachisi kwa anthu mau a moyo uwu. 21Ndipo pamene iwo anamva ichi, analowa m’kachisi m’bandakucha naphunzitsa. Ndipo pamene wamkulu wa ansembe anabwera, ndi iwo amene anali naye, anawasonkhanitsa pamodzi abwalo la akulu ndi akulu onse a ana a Israyeli, nawatuma ku ndende kuti akawatenge iwo. 22Ndipo pamene asilikali anabwera, sanawapeze iwo m’ndende; ndipo anabwerera kukanena 23nati, Tapeza ndende yotseka ndi chitetezo chonse, ndipo alonda atayima pa makomo onse; koma pamene tinatsegula, mkatimo sitinapeze aliyense. 24Ndipo pamene anamva mau amenewa, wansembe pamodzi ndi mdindo wa m’kachisi komanso asembe akulu anathedwa nzeru ndi iwowa, kuti chimenechi chiwabweretsera chiyani. 25Ndipo wina anabwera nanena kwa iwo, Taonani, anthu amene munawatsekera m’ndende ali m’kachisi, kuyimilira ndi kuphunzitsa anthu. 26Pamenepo mtsogoleri wao, atapita ndi asilikali, anawabweretsa, osati mwa mavuvu, pakuti amaopa anthu, mwina angawagende. 27Ndipo anabwera nawo nawayika pa bwalo la akulu. Ndipo mkulu wa ansembe anawafunsa iwo, 28nanena, Tinakulamulirani mwamphamvu kuti musaphunzitse mu dzina ili: ndipo taonani, mwadzala Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndi cholinga chotibweretsera ife mwazi wa munthu uyu. 29Koma Petro poyankha, ndi atumwi aja, anati, Tikuyenera kumvera Mulungu2 kusiyana ndi anthu. 30Mulungu3 wa atate wathu anamdzutsa Yesu, amene inu munamupha, mutampachika pa mtanda. 31Ameneyo Mulungu4 anamkweza ndi dzanja lake lamanja monga Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kupereka kulapa kwa Israyeli ndi chikhululukiro cha machimo. 32Ndipo ife ndife mboni zake za zinthu zimenezi, ndi Mzimu Woyera yemwe, amene Mulungu5 anampereka kwa iwo akumvera Iye. 33Koma iwo pamene anamva [zinthu izi], anasweka mtima, ndipo anafuna uphungu wa kuwaphera iwo. 34Koma [munthu] wina, Mfalisi, wotchedwa Gamaliyeli, mphunzitsi wa chilamulo, wochitiridwa ulemu ndi anthu onse, anayimilira pa uphungupo, ndipo analamulira kuwatulutsa panja anthuwo pang’ono, 35ndipo anati kwa iwo, Amuna inu a Israyeli, muchenjere nokha zokhudza anthu awa zimene mukufuna kuchita; 36pakuti asanafike masiku awa Teuda anauka, nadziyesa yekha kuti ali kanthu, kwa amene anthu ena, pafupifupi mazana anayi anaphatikana naye; amene anaphedwa, ndipo onse, amene anamumvera iye, anamwazikana nasanduka chabe. 37Atapita iye panaukanso Yuda m’Galileya m’masiku a kalembera, ndipo anadzitengera yekha anthu ena; ndipo iye anaonongeka, ndi onse, amene anamtsatira iye, anabalalitsidwa. 38Ndipo tsopano ndinena kwa inu, Asiyeni anthu awa ndipo aloleni azipita, pakuti ngati uphungu uwu kapena ntchito iyi ndi yochokera kwa anthu, idzaonongeka; 39koma ngati ili yochokera kwa Mulungu6, simungakwanitse kuwakhazika pansi, kuti inunso mungapezeke mukulimbana ndi Mulungu7. 40Ndipo iwo anamvera upangiri wake; ndipo atawayitana atumwiwo, anawakwapula, ndi kuwalamulira iwo kuti asalankhulenso m’dzina la Yesu, ndipo anawamasula iwo. 41Pamenepo iwo anachoka pakati pa bwalo la akulu, osangalala kuti anayesedwa oyenera kuzunzidwa chifukwa cha dzinalo. 42Ndipo tsiku lililonse, m’kachisi ndi mnyumba mwao, sanasiye kuphunzitsa ndi kulalikira uthenga wabwino kuti Yesu [anali] Khristu.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu