Mutu 9
1Ine ndinena choonadi mwa Khristu, Sindikunama ayi, chikumbumtima changa chindichitira umboni mwa Mzimu Woyera, 2kuti ndili ndi chisoni chachikulu ndi kuwawidwa mtima kosatha mu mtima mwanga, 3pakuti ndafunitsitsa, mkati mwanga, kukhala themberero londichotsa kwa Khristu pa abale anga, a mtundu wanga, molingana ndi thupi; 4amene ali a Israyeli; amene wao ndi umwana, ndi ulemelero, ndi mapangano, ndi kupereka kwa lamulo, ndi kutumikira, ndi malonjezano; 5a iwo ali makolo awo; ndi aiwo, molingana ndi thupi, [ndiwo] Khristu, amene ali pamwamba pa zonse, Mulungu1 alemekezedwe kwa muyaya. Amen.
6Osati monga kuti mau a Mulungu2 alephera ayi; pakuti onse si Aisrayeli amene ali mu Israyeli; 7kapena chifukwa iwo ali mbeu ya Abrahamu ali onse ana: koma, mwa Isake mudzayitanidwa mbeu yako. 8Ndiko kuti, [iwo amene ali] ana a kuthupi, amenewa sali ana a Mulungu3; koma ana a lonjezano awerengedwa monga mbeu. 9Pakuti mau awa ali a lonjezano, molingana ndi nyengo imeneyi ndidzabwera, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wa mwamuna. 10Ndipo osati chokhachi, koma Rabeka pamene anali ndi pakati pa m’modzi ndiye Isake kholo lathu, 11[anawa] asanabadwe, kapena asanachite kalikonse kabwino kapena kopanda pake (kuti cholinga cha Mulungu4 molingana ndi osankhika chikakhazikike, osati mwa ntchito, koma mwa Iye woyitanayo), 12kunanenedwa kwa iye, Wamkulu adzatumikira wamng’ono: 13molingana ndi momwe kunalembedwera, Ine ndamukonda Yakobo, ndipo ndadana naye Esau.
14Kodi tidzanena chiyani pamenepo? [kodi pali] chosalungama ndi Mulungu5? Musaganize choncho. 15Pakuti Iye anati kwa Mose, Ndidzaonetsera chifundo kwa iye ofunika chifundo, ndipo ndidzamkomera mtima iye amene ndifuna kumukomera mtima. 16Chomwecho pamenepo sizitengera kufuna kwa munthu, kapena kuyetsetsa kwake, koma chifuniro cha Mulungu6 amene amaonetsera chifundo. 17Pakuti malemba anati kwa Farao, Pakuti pa chinthu chimenechi ndakukweza iwe pakati pa [anthu], kuti ndikaonetsere mwa iwe mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa libukitsidwe padziko lonse lapansi. 18Chomwecho pamenepo kwa iye amene afuna amuonetsera chifundo, ndi kwa iye amene amuumitsa mtima.
19Pamenepo mudzanena kwa Ine, Chifukwa chiyani Iye amatipeza olakwa? Kwa amene amakana cholinga chake? 20Koma iwe munthu, ndiwe ndani wakubwezera mau kwa Mulungu7? Kodi chinthu chopangidwa chilankhula kwa Iye wochipangayo, Chifukwa chiyani mwandipanga motere? 21Kapena woumba mbiya sali nawo ulamuliro pa dothi, kuchokera ku dongo lomwelo kuumba mbiya ya mtengo wapatali, ndi ina ya mtengo wotsika? 22Ndipo ngati Mulungu8, afuna kuonetsa mkwiyo wake ndi kuonetsera mphamvu zake, anapilira modekha mtima zopangidwa za mkwiyo zoyenera chionongeko; 23ndi kuti akadziwitse kulemera kwa chisomo chake pa zotengera za ulemelero, 24ife, amene Iye anatiitananso, osati kungoti pakati pa Ayuda okha, komanso pakati pa amitundu? 25Monganso Iye analankhula ku Hoseya, Sindidzawatchula anthu anga kukhala anthu anga; ndipo osakondedwa sindidzawatchula Okondedwa. 26Ndipo kudzakhala pamalo pamene pananenedwa kwa iwo, Inu sianthu anga, pomwepo adzatchedwa Ana a Mulungu9 wamoyo. 27Koma Yesaya anafuula zokhudza Israyeli, Ngakhale chiwerengero cha Israyeli chikhala ngati mchenga wa kunyanja, otsalawo adzapulumutsidwa: 28pakuti [Iye] nkhaniyi akufika nayo kumapeto, ndipo akuthana nawo mwachidule molungama; chifukwa chidule chake cha nkhaniyi Ambuye adzachikwaniritsa padziko lapansi. 29Ndipo molingana ndi Yesaya analankhula kale, Pokhapokha ngati Ambuye wa makamu adzatisiyira ife mbeu, tikanakhala ngati Sodomu, ndipo akanachitanso nafe ngati Gomora.
30Kodi tidzanena chiyani ife? Kuti iwo a mitundu, amene sanatsatire kulungama, anapeza kulungama, koma kulungama kumene kuli pa mfundo ya chikhulupiliro. 31Koma Israyeli, potsata lamulo la kulungama, sanathe kulipeza lamulo limenelo. 32Chifukwa chiyani? Chifukwa silinali pa mfundo ya chikhulupiliro, koma pa ntchito. Iwo anapunthwa pa mwala wopunthwitsa, 33monga kunalembedwa, Taonani, ndayika m’Ziyoni mwala wopunthwitsa ndi thanthwe limene limagwetsa anthu: ndipo iye amene akhulupilira pa Iye sadzachititsidwa manyazi.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu