Mutu 6

1Ndipo ndinaona pamene Mwanawankhosa anatsegula chimodzi mwa zizindikiro zisanu ndi ziwiri, ndipo ndinamva chimodzi mwa cholengedwa chamoyo chikulankhula, ngati mau a bingu, Bwera [ndipo udzaone]. 2Ndipo ndinapenya: ndipo taonani, kavalo woyera, ndipo wokhala pamenepo ali ndi uta; ndipo korona anaperekedwa kwa iye, ndipo anapita nagonjetsa ndi kuti akagonjetse.

3Ndipo pamene anatsegula chizindikiro chachiwiri, ndinamva cholengedwa chamoyo chachiwiri chikulankhula, Bwera [ndipo udzaone]. 4Ndipo kavalo wina wofiira, anatuluka; ndipo iye wakukhalapo, kwa iye kunapatsidwa mphamvu yakuchotsa mtendere padziko lapansi, ndi kuti iwo aphane wina ndi mnzake; ndipo kwa iye kunapatsidwa lupanga lalikulu.

5Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachitatu, ndinamva cholengedwa chamoyo chachitatu chikunena, Bwera [ndipo udzaone]. Ndipo ndinaona: ndipo taonani, kavalo wakuda, ndipo iye wakukhalapo wokhala pamenepo anali nawo mlingo mdzanja lake. 6Ndipo ndinamva mau mkatikati mwa zolengedwa zamoyo zinayizo zikunena, Mlingo wa tirigu wogulidwa ndi rupiya, ndi miyeso itatu ya barele yogulidwa ndi rupiya: ndipo usaononge mafuta ndi vinyo.

7Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachinayi, ndinamva mau a cholengedwa chamoyo chachinayi chikunena, Bwera [ndipo udzaone]. 8Ndipo ndinaona: ndipo taonani, kavalo wonyololoka, ndipo iye wakukhalapo, dzina lake linali Imfa, ndipo hade anamlondola iye; ndipo ulamuliro unaperekedwa kwa iye kudera lachinayi la dziko lapansi kuti akalikanthe ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi chilombo cha padziko lapansi.

9Ndipo pamene anatsegula chizindikiro chachisanu, ndinaona pansi pake guwa mizimu ya iwo amene anaphedwa chifukwa cha mau a Mulungu1, ndi umboni umene iwo anali nawo; 10ndipo iwo anafuula ndi mau akulu, nanena, Kufikira liti, Wolamulira inu wodziimira panokha, woyera ndi woona, muleka kuweruza ndi kubwezera mwazi wathu pa iwo amene akhala padziko lapansi? 11Ndipo kunapatsidwa kwa iwo, aliyense mwinjiro woyera; ndipo kunanenedwa kwa iwo kuti apumule pang’ono, kufikira akapolo amnzawo ndi abale awo atakwanira, amene adzaphedwanso monga iwo, kuti kukwanitsidwe.

12Ndipo ndinaona pamene chinatsegulidwa chizindikiro chachisanu ndi chimodzi, ndipo panali chivomezi chachikulu; ndipo dzuwa linada bii monga chiguduli cha ubweya, ndipo mwezi onse unakhala ngati magazi, 13ndipo nyenyezi zakumwamba zinagwa padziko lapansi, monga mtengo wa mkuyu, wogwedezeka ndi mphepo ya mkuntho, kugwetsa zipatso zake zosacha. 14Ndipo kumwamba kunachotsedwa monga mpukutu wa buku wopindidwa, ndipo phiri lililonse ndi chilumba zinachotsedwa pamalo pake. 15Ndipo mafumu adziko lapansi, ndi akulu, ndi akazembe, ndi achuma, ndi amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anazibisa okha m’mapanga ndi m’miyala ya m’mapiri; 16ndipo iwo anati kwa mapiri ndi kwa miyala, Mutigwere ife, ndipo mutibise ife ku nkhope ya iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi ku mkwiyo wa Mwanawankhosa; 17c chifukwa tsiku lalikulu la mkwiyo wake lafika, ndipo ndani amene akhoza kuima?

1Elohimu