Mutu 21
1Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu anafika ku Betefage, pa phiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumiza ophunzira awiri, 2nanena kwa iwo, Pitani m’mudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo mukapeza bulu womangidwa, ndi mwana wake ali naye; m’masuleni [iye] ndipo atsogolereni [iwo] kwa Ine. 3Ndipo ngati munthu aliyense akanena kanthu kwa inu, munene, Ambuye awafuna awa, ndipo nthawi yomweyo adzawatumiza. 4Komatu zonse izi zinachitika, kuti chikakwaniritsidwe chimene chinalankhulidwa kudzera mwa mneneri, kunena kuti, 5Nenani kwa mwana wa mkazi wa Ziyoni, Taonani mfumu yanu idza kwa inu, wofatsa, wokwera pa msana pa bulu, ndi katundu woikidwa pamwamba pa mwana wa bulu. 6Koma ophunzira, atapita ndi kuchita zomwe Yesu anawalamulira iwo, 7anabweretsa bulu ndi mwana wake ndipo anaika zovala pa msana pawo, ndipo anakhala Iye pamenepo. 8Koma makamu akulu a anthu anayala zovala zawo mu msewu, ndipo ena anadulabe nthambi za mitengo naziyala mu msewu. 9Ndipo makamu amene amayenda patsogolo pake ndi iwo amene amatsatira pambuyo anafuula, nanena, Hosana kwa Mwana wa Davide; wodala [akhale] iye wakudza m’dzina la Ambuye; Hosana m’mwambamwamba. 10Ndipo pamene amalowa m’Yerusalemu, mzinda wonse unagwedezeka, nanena, Kodi uyu ndi ndani? 11Ndipo makamu anati, Ameneyu ndi Yesu mneneri wochokera ku Nazarete wa Galileya.
12Ndipo Yesu analowa m’kachisi [wa Mulungu1], ndipo anatulutsa onse amene amagulitsa ndi kugula m’kachisimo, ndipo Iye anagubuduza magome a anthu osintha ndalama komanso mipando ya iwo amene amagulitsa nkhunda. 13Ndipo Iye ananena kwa iwo, Kwalembedwa, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba ya pemphero, koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba. 14Ndipo akhungu ndi opunduka miyendo anadza kwa Iye m’kachisimo, ndipo Iye anawachiritsa iwo. 15Ndipo pamene ansembe akulu ndi alembi anaona zozizwa zimene Iye anachita, ndi ana pa kufuula m’kachisi ndi kunena, Hosana Mwana wa Davide, anali aukali, 16ndipo anati kwa Iye, Kodi mukumva zimene awa akunena? Ndipo Yesu anati kwa iwo, Inde; kodi inu simunawerengepo, Mkamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera bwino malemekezo? 17Ndipo pakuwasiya iwo anatuluka mu mzindawo kupita ku Betaniya, ndipo kumeneko Iye anakhalako usiku onse.
18Komatu mamawa kwambiri, pamene amabwerera mu mzinda muja, Iye anamva njala. 19Ndipo pakuona umodzi wa mtengo wa mkuyu panjira, Iye anafika pa mtengopo ndipo anapeza kuti palibe zipatso koma masamba okha. Ndipo Iye analankhula kwa mtengowo, Sudzaberekanso chipatso chochuluka kwamuyaya. Ndipo nthawi yomweyo mtengo wa mkuyuwo unafota. 20Ndipo pamene ophunzira anaona [ichi], anali odabwa, nati, Zakhala bwanji kuti mtengo wa mkuyuwu ufote mwachangu! 21Ndipo Yesu pakuyankha anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, ngati inu mukhala ndi chikhulupiliro, ndipo osakaika konse, osati muzangochita zimene [zachitikazi] ku mtengo wa mkuyu, komatu ngakhale mudzanena ku phiri ili, Uchotsedwe apa ndipo ukadziponye m’nyanja, ndipo izi zidzachitika. 22Ndipo zinthu zonse zimene inu mudzapempha mu pemphero, m’kukhulupilira, mudzalandira.
23Ndipo pamene analowa m’kachisi, ansembe akulu ndi akuluakulu a anthu anabwera kwa Iye [pamene anali] kuphunzitsa, nanena, Kodi mumachita izi pa ulamuliro wotani? Ndipo ndi ndani amene anakupatsani ulamuliro umenewu? 24Ndipo Yesu pakuyankha anati kwa iwo, Inenso ndikufunsani inu chinthu chimodzi, chimene inu mukandiuza, Inenso ndikuuzani ulamuliro umene ndimapangira zinthu zimenezi: 25Ubatizo wa Yohane, unachokera kuti? Kumwamba kapena kwa anthu? Ndipo anakambirana pa iwo okha, nanena, Ngati tinena kuti, Kumwamba, Iye adzanena kwa ife, Chifukwa chiyani nanga simunakhulupirire iye? 26komanso tikanena, kwa anthu, ife tikuopa khamu la anthu, pakuti onse anamuyesa Yohane mneneri. 27Ndipo pakumuyankha Yesu iwo anati, Sitikudziwa ife. Iyenso anati iwo, lnenso sindikuuzani ulamuliro umene ndimapangira zinthu izi. 28Koma inu mukuganiza bwanji? Munthu wina anali ndi ana awiri, ndipo kwa woyamba iye anati, Mwanawe, pita lero, ukagwire ntchito m’munda [wanga] wa mpesa. 29Ndipo iye pakuyankha anati, Ayi sindipita; koma kenako atalapa mwa iye yekha anapita. 30Ndipo kwa wachiwiri iye analankhula chimodzimodzi; ndipo iye pakuyankha anati, Ine [ndipita], mbuye, ndipo sanapite. 31Kodi mwa awiriwa ndi ndani amene anachita chifuniro cha atate? Iwo anati [kwa iye], woyambayo. Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu kuti okhometsa msonkho ndi akazi achiwerewere amatsogolera inu kulowa mu ufumu wa Mulungu2. 32Pakuti Yohane anabwera kwa inu munjira ya chilungamo, ndipo inu simunamkhulupirire iye; komatu okhometsa msonkho ndi akazi achiwerewere anamkhulupirira iye; koma inu pamene munachiona [ichi] simunalape nokha pambuyo pake kumkhulupirira iye.
33Mverani fanizo lina: Panali mwini nyumba amene anadzala m’munda wa mpesa, ndipo anamanga linga kuzungulira mundawo, ndipo anakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, ndipo anaubwereketsa kwa olima m’munda, ndipo anachoka m’dzikomo. 34Koma pamene nyengo ya zipatso inawandikira, anatumiza akapolo ake kwa olima m’munda uja kuti akalandire zipatso zake. 35Ndipo olima m’munda aja anagwira akapolo ake, ndipo anawamenya, namupha wina, ndipo wina anamugenda miyala. 36Anatumanso akapolo ena oposa oyamba aja, ndipo anachita nawonso chimodzimodzi. 37Ndipo pamapeto pake anatumiza kwa iwo mwana wake, nanena, Iwo akachitira ulemu mwana wanga. 38Koma olima m’munda pakumuona mwana uja, ananena mwa iwo okha, Uyu ndiye wolowa; bwerani, timuphe iye ndi kutenga cholowa chake. 39Ndipo anamtenga iye, namponya kunja kwa munda wa mpesa, ndipo anamupha iye. 40Pamene mbuye wa munda wa mpesa abwera, kodi adzachita chiyani kwa olima m’munda aja? 41Iwo ananena kwa Iye, Adzawaononga iye koopsya [anthu] oipa amenewo, ndipo adzaubwereketsa mundawo kwa olima m’munda ena, amene adzam’bwezera iye zipatso mu nyengo yake. 42Yesu anati kwa iwo, Kodi simunawerenge m’malembo, Mwala umene m’misiri womanga nyumba anaukana, umenewu wasanduka mwala wa pa ngodya: chimenechi ndi [cha] Ambuye, ndipo ndi chodabwitsa m’maso mwathu? 43Chotero ndinena kwa inu, kuti ufumu wa Mulungu3 udzachotsedwa kwa inu ndipo udzaperekedwa kwa mtundu umene udzabereka zipatso zake. 44Ndipo iye amene adzagwera pa mwala umenewu adzathyoka, koma iye amene udzamgwera, udzamupera iye ngati ufa. 45Ndipo ansembe akulu ndi Afarisi, pakumva mafanizo ake, anadziwa kuti amanena zokhudza iwo. 46Ndipo anafunitsitsa kumgwira Iye, koma iwo anachita mantha ndi makamu a anthu, pakuti anamuyesa Iye mneneri.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu