Mutu 3

1Tsopano pa chaka cha khumi ndi chisanu cha ulamuliro wa Tiberiyo Kaisara, Pontiyo Pilato anali kazembe wa Yudeya, ndipo Herode anali chiwanga cha Galileya, ndi Filipo m’bale wake chiwanga cha Itureya ndi chigawo cha Trakoniti, ndi Lusaniyo anali chiwanga cha Abilene, 2mu ukulu wa nsembe wa Anasi ndi Kayafa, [mau a Mulungu1 anabwera kwa Yohane, mwana wa Zakariya, m’chipululu.] 3Ndipo iye anabwera m’madera onse ozungulira Yordano, kulalikira ubatizo wa kulapa pa chikhululukiro cha machimo, 4monga kunalembedwa m’buku la mau a Yesaya mneneri: Mau a wofuula m’chipululu: Konzani inu njira ya Ambuye, konzani khwalala lake likhale lowongoka. 5Chigwa chilichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lililonse ndi chikweza zidzachepetsedwa, ndipo [malo] aliwonse okhotakhota adzasanduka [njira] yowongoka, ndipo njira za zigolowondo zizasalala, 6ndipo thupi lililonse lidzaona chipulumutso cha Mulungu2. 7Pamenepo iye anati kwa makamuwo amene anatuluka kukabatizidwa ndi iye, Mbeu ya njoka inu, ndani amene anakuchenjezani kuthawa mkwiyo umene ukubwera? 8Chotero berekani zipatso zoyenera kulapa; ndipo musamanene mwa inu nokha, Tili naye Abrahamu ngati atate [wathu], Pakuti ine ndinena kwa inu kuti Mulungu3 akhoza kusandutsa miyala iyi kukhala ana a Abrahamu. 9Ndiponso nkhwangwa yaikidwa kale pa muzu wa mtengo; kotero kuti mtengo uliwonse umene subereka chipatso chabwino udulidwa ndi kuponyedwa m’moto. 10Ndipo makamuwo anamufunsa iye nati, Kodi tichite chiyani pamenepo? 11Ndipo iye poyankha anati kwa iwo, Iye amene ali nawo malaya awiri, apatseko iye amene alibe; ndipo amene ali nacho chakudya, achite chimodzimodzi. 12Ndipo anadza okhometsa msonkho kuti nawonso abatizidwe, ndipo iwo anati kwa iye, Mphunzitsi, kodi ifeyo tichite chiyani? 13Ndipo iye anati kwa iwo, Musamatolere [ndalama] yopitilira imene munauzidwa. 14Ndipo munthu wina amene anali msilikali anamufunsanso iye nati, Nanga ife tichite chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musamapondereze aliyense, kapena kunamizira munthu, ndiponso mudzikhutira ndi malipiro anu. 15Ndipo pamene anthu anali kuyembekezera, ndipo onse anali kulingalira m’mitima mwao zokhudza Yohane kuti ngati iye akhoza kukhala Khristu, 16Yohane anawayankha onse, nanena, Ineyo zoonadi ndikubatizani inu ndi madzi, komatu wamkulu kuposa ine akubwera, amene chingwe cha nkhwayira yake sindili woyenera kuchimasula; Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera komanso moto; 17amene chowuluzira mphepo chili m’manja mwake, ndipo adzayeretsa padwale pake, ndipo adzasonkhanitsa tirigu m’chiluri chake, koma madeya adzaotchedwa ndi moto osazimitsika. 18Powadandaulira pamenepo zinthu zina zambiri komanso iye analengeza uthenga [wake] wabwino kwa anthu. 19Koma Herode mfumuyo, pakudzudzulidwa ndi iye za Herodiya, mkazi wa m’bale wake, ndi zinthu zonse zoipa zimene Herodeyo anazichita, 20anaonjezera ichinso pa zonse [zotsala], kuti akamutsekere Yohane m’ndende.

21Ndipo kunachitika kuti, anthu onse pamene anabatizidwa ndi kupemphera, kumwamba kunatseguka, 22ndipo Mzimu Woyera anatsika pa Iye mthupi ngati nkhunda; ndipo mau anachokera kumwamba, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndapeza kukondwera kwanga.

23Ndipo Yesu mwini anayamba kukwanitsa zaka makumi atatu; nakhala monga anayenera kukhala mwana wa Yosefe; mwana wa Eli, 24mwana wa Matati, mwana wa Levi, mwana wa Melki, mwana wa Yana, mwana wa Yosefe, 25mwana wa Matatiyo, mwana wa Amosi, mwana wa Naumi, mwana wa Esli, mwana wa Nagai, 26mwana wa Maati, mwana wa Matatiyo, mwana wa Semeini, mwana wa Yosefe, mwana wa Yoda, 27mwana wa Yoanani, mwana wa Resa, mwana wa Zerubabeli, mwana wa Salatieli, mwana wa Neri, 28mwana wa Melki, mwana wa Adi, mwana wa Kosamu, mwana wa Elmadama, mwana wa Ere, 29mwana wa Jose, mwana wa Eliezere, mwana wa Yorimu, mwana wa Matati, mwana wa Levi, 30mwana wa Simeoni, mwana wa Yuda, mwana wa Yosefe, mwana wa Yonamu, mwana wa Eliyakimu, 31mwana wa Melea, mwana wa Mena, mwana wa Matata, mwana wa Natani, mwana wa Davide, 32mwana wa Jese, mwana wa Obedi, mwana wa Boazi, mwana wa Salimoni, mwana wa Naasoni, 33mwana wa Aminadabu, mwana wa Aramu, mwana wa Ezromu, mwana wa Faresi, mwana wa Yuda, 34mwana wa Yakobo, mwana wa Isake, mwana wa Abrahamu, mwana wa Tera, mwana wa Nakoro, 35mwana wa Seruki, mwana wa Ragau, mwana wa Faleki, mwana wa Ebere, mwana wa Sala, 36mwana wa Kainani, mwana wa Arfaksadi, mwana wa Semu, mwana wa Nowa, mwana wa Lameki, 37mwana wa Metusala, mwana wa Enoki, mwana wa Yaredi, mwana wa Malaleeli, mwana wa Kainane, 38mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu4.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu