Mutu 4
1Pamenepo, pokhala nawo utumiki umenewu, monga chifundo chaonetsedwa kwa ife, sitifooka konse. 2Koma takana zinthu zobisika za manyazi, osati kuyenda m’chinyengo, kapena kuchitira chinyengo mau a 1Mulungu, koma mwa maonekedwe a choonadi kudzivomereza tokha ku chikumbumtima chilichonse cha anthu pamaso pa 2Mulungu. 3Komanso ngati uthenga wathu wabwino waphimbika, uphimbika kwa iwo amene ali osochera; 4mwa iye 3mulungu wa dziko lapansi wachititsa khungu malingaliro a osakhulupilira, kotero kuti kuwala kwa uthenga wabwino wa ulemelero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha 4Mulungu, asawalire [kwa iwo]. 5Pakuti sitilalikira za ife eni, koma Khristu Yesu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu chifukwa cha Yesu. 6Chifukwa ali 5Mulungu amene analankhula kuchokera mu mdima kuunika kuwale amene wawala m’mitima mwathu kuwala kwa chidziwitso cha ulemelero wa 6Mulungu mu nkhope ya Yesu Khristu. 7Koma tili nacho chuma ichi mchotengera cha dothi, kuti ukulu woposa wa mphamvu ukhale wa 7Mulungu, osati wochokera kwa ife: 8kusautsika njira zonse, koma osapsinjika; osakhala kakasi, koma njira yathu yosatsekeka yonse; 9ozunzidwa, koma osasiyidwa; kugwetsedwa koma osaonongeka; 10nthawi zonse kusenza mthupi kufa kwa Yesu, kuti moyonso wa Yesu uwonekere m’thupi lathu; 11pakuti ife amene tikhala ndi moyo tapulumutsidwa mu imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyonso wa Yesu uwonekere m’thupi lathu la imfali; 12kotero kuti imfa ichite mwa ife, koma moyo mwa inu. 13Ndipo pokhala nawo mzimu womwewo wa chikhulupiliro, molingana ndi chimene chalembedwa, ndakhulupilira, pamenepo ine ndalankhula; ifenso takhulupilira, pameneponso ife talankhula; 14podziwa kuti iye amene anaukitsa Ambuye Yesu adzaukitsanso ife ndi Yesu, ndipo adzationetsera [ife] pamodzi ndi inu. 15Pakuti zinthu zonse nza kwainu, kuti chisomo chochulukira mwa ambiri chikadzetse chiyamiko kuchulukira ku ulemelero wa 8Mulungu. 16Pamenepo ife sitifooka; koma ngatidi munthu wathu wakunja avunda, komabe wamkati akonzedwa tsiku ndi tsiku. 17Pakuti kusakhalitsa kwa msautso wopepukawu kuchitira ubwino ifeyo pa mlingo wodutsa kulemera kwamuyaya kwa ulemelero; 18pamene ife tiyang’ana osati zinthu zimene zioneka ndi maso, koma ku zinthu zimene sizioneka ndi maso; pakuti zinthu zimene zioneka ndi maso ndi za kanthawi, koma zimene zili zosaoneka ndi maso ndi zamuyaya.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu