Mutu 22

1Ndipo anandionetsa ine mtsinje wa madzi amoyo, wonyezimira ngati krustalo, kuchokera ku mpando wachifumu wa Mulungu1 ndi Mwanawankhosa. 2Pakati pa msewu wake, ndi pa mtsinje, mbali yakuno ndi mbali inayo, panali mtengo wamoyo, wakubereka zipatso khumi ndi ziwiri, mwezi uliwonse kubereka chipatso chake; ndipo masamba a mtengowo kuchiritsira amitundu. 3Ndipo thembelero silidzakhalakonso; ndipo mpando wachifumu wa Mulungu2 ndi wa Mwanawankhosa udzakhala m’menemo; ndipo atumiki ake adzamtumikira iye, 4ndipo iwo adzaona nkhope yake; ndipo dzina lake lili pa mphumi pawo. 5Ndipo usiku sudzakhalakonso, ndipo nyale sidzafunika, ndi kuwala kwa dzuwa; pakuti Ambuye Mulungu3 adzawalira pa iwo, ndipo adzalamulira kwa nthawi za nthawi.

6Ndipo iye anati kwa ine, Mau awa ndi okhulupirika ndi oona; ndipo Ambuye Mulungu4 wa mizimu ya aneneri watumiza angelo ake kuonetsa akapolo ake zinthu zimene zikuyenera kuchitika posachedwa. 7Ndipo taonani, ndidza msanga. Wodala [ali] iye wakusunga mau a uneneri wa buku ili.

8Ndipo ine, Yohane, [ndinali] amene ndinamva ndikuona zinthu zimenezi. Ndipo pamene ndinamva ndi kuona, ndinagwa pansi ndi kulambira pamapazi a mngelo amene anandionetsa zinthu izi. 9Ndipo anati kwa ine, Taona usachite ichi. Ndine kapolo mzako, ndi [kapolo mnzawo] wa abale ako aneneri, ndi iwo akusunga mau a buku ili. Ulambire Mulungu5.

10Ndipo iye anati kwa ine, Usayike chizindikiro mau a uneneri a buku ili, Nthawi yawandikira. 11Iye wakuchita chosalungama achitebe chosalungama; ndipo iye wakuchita zonyasa achitebe zonyasa; ndipo iye wakuchita cholungama achitebe cholungama; ndi iye amene ali woyera, akhalebe woyeretsedwa. 12Taonani, ndidza msanga, ndipo mphoto imene ndiIi nayo, kupereka kwa aliyense monga mwa ntchito zake. 13Ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi mathero.

14Odala [ali] iwo amene anachapa mikanjo yawo, kuti akakhale ndi ufulu wa kumtengo wamoyo, ndi kuti akalowe pa zipata mu mzindawo. 15Kunja kuli agalu, ndi amatsenga, ndi achigololo, ndi akupha, ndi opembedza mafano, ndi aliyense wakukonda ndi kuchita bodza.

16Ine Yesu ndatumiza angelo anga kuchitira umboni zinthu zimenezi kwa inu ndi ku mipingo. Ndine muzu ndi mbeu ya Davide, nyenyezi yowala ya ku m’bandakucha. 17Ndipo Mzimu ndi mkwatiyo anati, Bwerani. Ndipo iye wakumva ludzu abwere; iye wakufuna, atenge madzi a moyo kwaulere.

18Ine ndichitira umboni kwa aliyense wakumva mau a uneneri a buku ili, ngati wina adzaonjezera ku zinthu zimenezi, Mulungu6 adzaonjezera kwa iye milili imene yalembedwa m’buku ili. 19Ndipo ngati wina akachotsa mau a buku la uneneri uwu, Mulungu7 adzamchotsera gawo lake ku mtengo wamoyo, ndi kuchotsedwa mu mzinda woyera, amene alembedwa m’buku ili.

20Iye wakuchitira umboni zinthu zimenezi anena, Inde, ndidza msanga. Amen; bwerani, Ambuye Yesu.

212Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi oyera mtima onse.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu