Mutu 6
1Mwa ichi, kusiya mau a chiyambi cha Khristu, tipitirize [ku zimene zipezeka] m’kukula kwathunthu, osayalanso maziko a kulapa kuchoka ku ntchito zakufa ndi chikhulupiriro mwa Mulungu1, 2za chiphunzitso cha ubatizo, ndi kusanjika kwa manja, ndi za kuuka kwa akufa, ndi za chiweruzo cha muyaya; 3ndipo ichi tizachita ngati Mulungu2 alola. 4Pakuti nzosatheka kuwakonzanso ku kulapa iwo amene poyamba anali mkuunika, ndipo analawako mphatso yakumwamba, ndipo anatenga nawo gawo la Mzimu Woyera, 5ndipo analawa ubwino wa mau a Mulungu3, ndi ntchito za mphamvu za nyengo imene ilinkudza, 6ndipo anagwa, nadzipachika okha [monga iwo achitira] Mwana wa Mulungu4, ndi kumchititsa manyazi [iye]. 7Pakuti nthaka imene imamwa mvula yobwera kawirikawiri pa nthakapo, ndi kuphukitsa zomera zoyenera iwonso amene anayitipula, itenga nawo gawo la mdalitso ochokera kwa Mulungu5; 8koma ikulitsa minga ndi mitungwi, zimene zipezeka zopanda phindu ndi zowandikira ku themberero, zimene chitsiriziro chake ndicho kuotchedwa. 9Koma ife takopeka ndi inu, wokondedwa, zinthu zabwino, ndi kulumikizika nacho chipulumutso, ngakhale ife tilankhula choncho. 10Pakuti Mulungu6 sali wosalungama kuiwalira ntchito yanu, ndi chikondi chimene mwaonetsera ku dzina lake, potumikira kwa oyera mtima, ndi kutumikirabe. 11Koma tili nacho chikhumbokhumbo chachikulu kuti aliyense wa inu awonetse changu ku chitsimikizo chathunthu cha chiyembekezo kufika kumapeto; 12kuti musakhale aulesi, koma akutsanza a iwo amene mwa chikhulupiriro ndi chipiriro anakhala olowa a malonjezano.
13Pakuti Mulungu7, atamulonjeza Abrahamu, popeza analibe wamkulu womlumbirira, analumbira pa iye yekha, 14nanena, Zoonadi mdalitso ndidzakudalitsa iwe, ndipo kuchulukitsa ndidzachulukitsa iwe; 15ndipo pamenepo, pokhala nacho chipiriro choposa, iye analandira lonjezano. 16Pakuti anthu amalumbiradi kwakukulu, ndipo mwa iwo lumbiroli ndilo chitsimikizo chonse, kutsindika zinthuzo kukhala zoona. 17Momwemo Mulungu8, afunitsitsa kusonyezera zochuluka kwa iwo olowa mu lonjezano kusasinthika kwa cholinga chake, kulowerera mwa lumbiro, 18kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, zimene kunali kovuta kwa Mulungu9 kuti anene bodza, ife tikhale nacho chilimbikitso cha mphamvu, amene tinathawira kupeza mpumulo pa chiyembekezo chimene chinayikidwa kwa ife, 19chimene tili nacho ngati cholimbitsira moyo, chotetezeka ndi chokhazikika, ndi kulowa m’menemo mwa chophimba, 206 kumene Yesu akulowa monga wotitsogolera wathu, kukhala nthawi zonse wamkulu wansembe molingana ndi dongosolo la Melikizedeke.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu