Mutu 21
1Ndipo pamene, tinachoka kwa iwo, tinakwera ngalawa, tinafika chindunji moyang’anana ndi Ko, ndipo m’mawa mwake ku Rode, ndipo kuchoka kumeneko ku Patara. 2Ndipo tinapeza ngalawa yodutsira m’Foinike, tinakwera imeneyo ndi kunyamuka; 3ndipo tinaona mzinda wa Kupro ndipo tinaudutsa kudzanja lamanzere, tinapitilira kupita ku Suriya, ndipo tinakocheza ku Turo, pakuti kumeneko ngalawa imatsitsa katundu wake. 4Ndipo m’mene tinapeza ophunzira, tinakhala kumeneko masiku asanu ndi awiri; amene analankhula kwa Paulo mwa Mzimu kuti asapite ku Yerusalemu. 5Koma titamaliza masikuwo, tinakonzeka ndi kunyamuka ulendo wathu, onse mwa iwo anatiperekeza ife, pamodzi ndi akazi awo ndi ana, kufikira tinatuluka mu mzindawo. Ndipo tinagwada mphepete mwa nyanja ndi kupemphera. 6Ndipo titalawirana wina ndi mzake, tinakwera m’ngalawamo, ndipo iwo anabwerera kunyumba. 7Ndipo ife, titatsiriza ulendowo, tinafika ku Ptolemayi kuchokera ku Turo, ndipo titawalonjera abale, tinakhala nawo tsiku limodzi. 8Ndipo titanyamuka m’mawa mwake, tinafika ku Kaisareya; ndipo tinalowa mnyumba mwa Filipo mlalikiyo, amene anali m’modzi wa asanu ndi awiriwo, tinakhala naye. 9Tsopano munthu ameneyu anali ndi ana akazi anayi anamwali amene ananenera. 10Ndipo pamene ife tinakhala kumeneko masiku ambiri, munthu wina dzina lake Agabo, mneneri, anabwera kuchokera ku Yudeya, 11ndipo pobwera kwa ife anatenga lamba wa Paulo, ndipo anazimanga manja ake ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, mwini wake wa lamba uyu adzamangidwa ndi Ayuda m’Yerusalemu, ndipo adzampereka m’manja mawa Amitundu. 12Ndipo pamene ife tinamva zinthu izi, tonse amene tinali pamenepo tinamdandaulira [iye] kuti asapite ku Yerusalemu. 13Koma Paulo anayankha, Chifukwa chiyani, mukulira ndi kundiswera mtima? pakuti ine ndili wokonzeka osati kumangidwa kokha, komanso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu. 14Ndipo pamene iye sakanakopekanso, tinakhala chete, ndi kuti, Chifukiro cha Ambuye chichitike. 15Ndipo atapita masiku amenewa, tinakonza a katundu athu, tinapita ku Yerusalemu. 16Ndipo [ena] mwa ophunzira aku Kaisareya anapita nafe, nabwera naye Mnaso waku Kupro, ophunzira wakalekale, amene tinakhala naye pamodzi. 17Ndipo pamene tinafika ku Yerusalemu abale anatilandira ife mwamsangala. 18Ndipo m’mawa mwake Paulo anapita nafe kwa Yakobo, ndipo akulu onse anafika kumeneko. 19Ndipo powalonjera iwo, iye anawafotokozera chimodzichimodzi cha zinthu zimene Mulungu1 anachita pakati pa amitundu mwa utumiki wake. 20Ndipo iwo pakumva [izi] analemekeza Mulungu2, ndipo anati kwa iye, Waona, m’bale, kuti ambirimbiri a Ayuda akhulupilira, ndipo onse ali ndi changu cha pa lamulo. 21Ndipo iwo adziwitsidwa zokhudza iwe, kuti waphunzitsa Ayuda onse pakati pa amitundu apatukane ndi Mose, kuwauza kuti asawadule ana awo, kapena kuyenda mu miyambo. 22Kodi chimenechi ndi chiyani? Ochuluka akuyenera kubwera pamodzi, pakuti adzamva kuti iwe wafika. 23Pamenepo tinena izi kwa iwe: tili nawo amuna anayi amene anachita chowinda pa iwo; 24uwatenge amenewa ndipo uyeretsedwe nawo pamodzi, ndi kuwalipilira, kuti mitu yawo ikhoza kumetedwa; ndipo onse akadziwe kuti [mwa zinthu zimenezo] zimene anadziwitsidwa za iwe palibe chimene chili [choona]; komanso kuti iwe mwini ukayendenso molunjika, posunga lamulo. 25Koma zokhudza [iwo mwa] amitundu amene akhulupilira, talemba ife, kulingalira kuti iwo [asasamale zinthu zimenezo, koma kuti] azipatule okha ku zinthu zoperekedwa kwa mafano, ndi mwazi, ndi zinthu zimene zapotoledwa, ndi chigololo. 26Pamenepo Paulo, anawatenga amunawo, tsiku lotsatiralo, atayeretsedwa, ndipo analowa nawo mkachisi, kusonyeza nthawi ya masiku akudziyeretsa kuti akwaniritsidwa, kufikira chopereka chinaperekedwa pa aliyense wa iwo. 27Ndipo pamene masiku asanu ndi awiri anatsala pang’ono, Ayuda ochokera ku Asiya, pamene anamuona iye m’kachisi, anautsa khamu lonse la anthu m’chisokonezo, ndipo anamgwira iye, 28nafuula, Aisrayeli, tithandizeni! Uyu ndi munthu amene amaphunzitsa onse paliponse motsutsana ndi anthu, ndi chilamulo, ndi malo ano, ndipo wabweretsanso amitundu mkachisi, ndi kudetsa malo awa oyera. 29Pakuti iwo adamuona kale Trofino m’Efeso ali naye pamodzi mu mzinda, amene iwo anayesa kuti Paulo anam’bweretsa m’kachisi. 30Ndipo mzinda onse unasokonezeka, ndipo panali chipwirikiti pa anthuwo; ndipo pamene anam’gwira Paulo anamtulutsa mkachisi, ndipo nthawi yomweyo zitseko zinatsekedwa. 31Ndipo pamene iwo anafuna kumupha, kunabwera nthumwi kwa mkulu wa guluyo kunena kuti Yerusalemu yense anali mu chipwirikiti; 32ameneyo, nthawi yomweyo anatengana ndi asilikali ndi akenturiyo, nawathamangira kwa iwo. Koma iwo, poona mkulu wa guluyo ndi asilikali, anasiya kumumenya Paulo. 33Mkulu wa guluyo anabwera ndi kumugwira iye, nalamulira kuti [iye] amangidwe ndi maunyolo awiri, ndipo anamfunsa kuti iyeyo ndi ndani, ndipo wachita chiyani. 34Ndipo wina anafuula zina ndi winanso zina m’khamulo. Koma iye, posadziwa chenicheni choyambitsa phokosolo anamlamulira kuti adze naye mu linga. 35Koma pamene iye anafika pa makwerero kunachitika kuti anamnyamula asilikali chifukwa cha chiwawa cha khamulo. 36Pakuti khamu lalikulu linamtsatira, likufuula, mchotseni iye. 37Komatu pamene iye amati amtengere ku linga, Paulo anati kwa kapitawo wamkulu, Kodi ndi kololedwa ine kulankhula kanthu kena kwa inu? Ndipo iye anati, Kodi iwe umadziwa chihelene? 38Kodi sindiwe m’Aigupto amene asanafike masiku awa unachita mipanduko ndipo unatsogolera ku chipululu amuna zikwi zinayi akuphawo? 39Koma Paulo anati, Ine ndi Myuda waku Tariso, mzika ya mumzinda wotchuka wa Kilikiya, ndipo ndikupemphani inu, ndiloleni ine ndilankhule ndi anthuwa. 40Ndipo pamene anamlola iye, Paulo, poyima pa makwerero, anawakhazika chete anthuwo ndi dzanja lake; ndipo bata lalikulu litachitika, nawalankhula iwo m’chihelene, nati,
1Elohimu2Elohimu