Mutu 8
1Koma zokhudza zinthu zoperekedwa nsembe ku mafano, ife tidziwa, (pakuti ife tonse tili nacho chidziwitso: chidziwitso chimatukumula, koma chikondi chimangilira. 2Ngati wina ayesa kuti amadziwa kanthu, sadziwa kalikonse monga iye ayesa akudziwa. 3Koma ngati wina akonda Mulungu1, ameneyu adziwika mwa Iye): 4— pamenepo zokhudza kudya zinthu zoperekedwa ku mafano, ife tidziwa kuti fano lili chabe m’dziko lapansi, ndipo kuti palibe Mulungu2 wina kupatula m’modzi. 5Pakuti ngati ilipo ina yotchedwa milungu, kaya ndi kumwamba kapena padziko lapansi, (monga pali milungu yambiri, ndi ambuye ambiri,) 6komabe kwa ife [alipo] Mulungu3 m’modzi, Atate amene zinthu zonse, ndi ife tomwe tili ake; ndi Ambuye m’modzi, Yesu Khristu, amene mwa Iye ndi zinthu zonse, ndipo ifeyo tili mwa Iye. 7Komatu chidziwitso sichili mwa onse: koma ena, ndi chikumbumtima cha fano, kufikira pano amadyabe zinthu zoperekedwa nsembe ku mafano; ndipo chikumbumtima chawo, pokhala chofooka, ali odetsedwa. 8Komatu nyama simativomeredzetsa ife kwa Mulungu4; kapena ngati sitidya sitikhala operewera; mwinanso ngati tidya tili nako kupindula. 9Koma onetsetsani kuti ufulu wanu [wakudya] usakhale chokhumudwitsa kwa ofookawo. 10Pakuti ngati wina akuona iwe, amene uli ndi chidziwitso, utakhala pa gome mnyumba ya fano, kodi chikumbumtima chake, iye pokhala ofooka, sichidzalimbika kudya zinthu zoperekedwa kwa fano? 11ndipo wofookayo, m’bale amene Khristu anamufera, adzaonongeka kudzera mu chidziwitso chako. 12Tsopano, pamene muchimwira abalewo, ndi kuvulaza chikumbumtima chawo, muchimwiranso Khristu. 13Pamenepo ngati nyama ikhala msampha kwa m’bale wanga, sindidzadyanso nyama mpaka muyaya, kuti ndisakhale chokhumudwitsa kwa m’bale wanga.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu