Mutu 10

1Koma munthu wina wa m’Kaisareya, — dzina lake Korneliyo, kenturiyo wa gulu lotchedwa Italiya, 2wopembedza, ndi woopa Mulungu1 pamodzi ndi banja lake lonse, amapereka zachifundo kwa anthu, ndi kupembedza Mulungu2 kosalekeza, 3— anaona chindunji m’masomphenya, pafupifupi ola lachisanu ndi chinayi la tsiku, mngelo wa Mulungu3 akubwera kwa iye, ndipo anati kwa iye, Korneliyo. 4Koma iye, polunjikitsa maso ake pa iye, ndi kukhala ndi mantha kwathunthu, anati, Kodi ndi chiyani, Ambuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zafika ngati chikumbutso pamaso pa Mulungu4. 5Ndipo tsopano tumiza anthu ku Yopa akatenge Simoni, wotchedwanso Petro. 6Iye akukhala ndi Simoni wina, wofufuta zikopa, amene nyumba yake ili mphepete mwa nyanja. 7Ndipo pamene mngelo amene amalankhula kwa iye anachoka, anayitana awiri a antchito ake komanso msilikali wopembedza amene amakhala ndi iye nthawi zonse, 8ndipo iye anafotokoza zinthu zonse kwa iwo, ndipo anawatumiza ku Yopa. 9Ndipo m’mawa mwake, pamene awa amapita ndi powandikira mzindawo, Petro anakwera pa chindwi panyumba kukapemphera, pafupifupi ola lachisanu ndi chimodzi. 10Ndipo iye anamva njala nafuna kudya. Koma m’mene amakonzekera chakudya kunamgwera ngati kukomoka: 11ndipo iye anaona kumwamba kutatseguka, ndipo chotengera china chinali kutsika, monga nsalu yayikulu, [yomangidwa] mbali zonse zinayi ikutsitsidwa padziko lapansi; 12m’menemo munali nyama za miyendo inayi ndi zinthu zokwawa za dziko lapansi, ndi mbalame za mlengalenga. 13Ndipo panali mau kwa iye, Tauka, Petro, uphe ndipo udye. 14Ndipo Petro anati, nkosatheka, Ambuye; pakuti sindinadyeko kalikonse ka wamba kapena kodetsedwa. 15Ndipo [panali] mau onenedwanso kachiwiri kwa iye, chimene Mulungu5 wachiyeretsa, usachiyese iwe chinthu wamba. 16Ndipo zimenezi zinachitika katatu konse, ndipo chotengeracho nthawi yomweyo chinatengedwa kupita kumwamba. 17Ndipo pamene Petro anakayika payekha kuti masomphenya awa akutanthauza chiyani, taonaninso amuna aja anatumidwa ndi Korneriyo, atafunsira nyumba ya Simoni, anayima pa chipata, 18ndipo atayitana [munthu wina], iwo anafunsira ngati Simoni amenenso anatchedwa Petro amakhalira kumeneko. 19Koma pamene Petro amalingalirabe za masomphenya, Mzimu anati kwa iye, Taona, amuna atatu akukufuna iwe; 20koma nyamuka, tsika, ndipo upite nawo, usakayike kalikonse, chifukwa Ine ndawatumiza iwo. 21Ndipo Petro potsikira kwa amunawo anati, Taonani, ndine amene mukumufunayo: chimene mwabwerera ndi chiyani? 22Ndipo iwo anati, Korneriyo, kenturiyo, munthu wolungama, ndi woopa Mulungu6, ndipo achitiridwa umboni ndi fuko lonse la Ayuda, walangizidwa mwa umulungu ndi mngelo woyera kuti mupite kunyumba kwake, ndipo akamve kuchokera kwa inu. 23Pamenepo atawalowetsa iwo mnyumba, anakhala ndi iwo. Ndipo m’mawa mwake, anauka napita nawo pamodzi, ndipo ena mwa abale aku Yopa anapita naye. 24Ndipo m’mawa mwake anafika ku Kaisareya. Koma Korneliyo anali kuwadikira iwo, atayitanitsa abale ake ndi abwenzi [ake] a pamtima. 25Ndipo pamene Petro amalowa mnyumba, Korneliyo anamulonjera iye, ndipo anagwada pansi namlambira. 26oma Petro anamdzutsa iye, nanena, Tayimilira: Inenso ndine munthu. 27Ndipo iye analowa mnyumbamo, akulankhula naye, ndipo anapeza anthu ambiri atasonkhana pamodzi. 28Ndipo iye anati kwa iwo, Inu mukudziwa kuti sikololedwa kwa Myuda kuphatikana kapena kubwera kwa munthu wa mtundu wachilendo, ndipo kwa ine Mulungu7 wandionetsera kuti ndisatchule munthu wina aliyense wa wamba kapena wodetsedwa. 29Pameneponso, potumidwa, ndabwera mosatsutsana ndi ichi. Chomwecho ndikufuna kudziwa chifukwa chimene wandiyitanira ine. 30Ndipo Korneliyo anati, Masiku anayi apitawa ndakhala ndikusala kudya kufikira ola lino, ndipo ola lachisanu ndi chinayi [ndinali] kupemphera mnyumba mwanga, ndipo taonani, munthu anayima pamaso panga wovala zovala zonyezimira, 31ndipo anati, Korneliyo, pemphero lako lamveka, ndipo zachifundo zako zafika ngati chikumbutso pamaso pa Mulungu8. 32Pamenepo tumiza ku Yopa ndi kuyitana Simoni, wotchedwanso Petro; amene akukhala mnyumba ya Simoni, wofufuta zikopa, mphepete mwa nyanja [ameneyo akabwera adzalankhula kwa iwe]. 33Pamenepo nthawi yomweyo ndinayitanitsa iwe, ndipo iwe wachita bwino kuti wabwera. Pamenepo tsopano tonse tili pamaso pa Mulungu9 kumva zinthu zonse zimene wakulamulira Mulungu10. 34Ndipo Petro potsegula pakamwa pake anati, Zoonadi ndakhulupilira kuti Mulungu11 salemekeza munthu, 35koma m’mitundu yonse amene amuopa Iye ndi kugwira ntchito molungama amalandilidwa kwa Iye. 36Mau amene Iye anatumiza kwa ana a Israyeli, kulalikira mtendere mwa Yesu Khristu, ( Iye ndi Ambuye wa zinthu zonse,) 37inu mukudziwa; umboni umene unafalikira mu Yudeya yense, kuyambira ku Galileya atalengeza za ubatizo umene Yohane anaulalikira — 38Yesu amene [anali] waku Nazarete: m’mene Mulungu12 anamudzodzera Iye mwa Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anayenda [m’madera onse] kuchita zabwino, ndi kuchiritsa onse amene anali pansi pa mphamvu ya mdierekezi, chifukwa Mulungu13 anali naye. 39Ifenso ndife mboni ya zinthu zonse zimene Iye anazichita m’dziko la Ayuda ndi mu Yerusalemu; amenenso iwo anamupha, nampachika Iye pa mtanda. 40[Munthu] ameneyu Mulungu14 anamuukitsa tsiku lachitatu ndi kumpereka kuti awonedwe poyera, 41osati kwa anthu onse, koma kwa mboni zimene zinasankhidwa pamaso pa Mulungu15, ifeyo amene tinadya ndi kumwa pamodzi naye pamene anaukitsidwa pakati pa akufa. 42Ndipo anatilamulira ife kulalikira kwa anthu, ndi kuchitira umboni kuti Iye ali amene anasankhidwa mwa Mulungu16 [kukhala] woweruza wa anthu amoyo ndi akufa. 43Kwa Iye aneneri onse anachitira umboni kuti aliyense wokhulupilira pa Iye alandire m’dzina lake chikhululukiro cha machimo.

44Petro adakali chilankhulure mau amenewa Mzimu Woyera anagwa pa onse amene amamvera mauwa. 45Ndipo okhulupilira a kumdulidwe anali odabwa, ambiri a iwo amene anabwera ndi Petro, mwakuti pa amitundunso mphatso ya Mzimu Woyera inathiridwa: 46pakuti iwo anawamva akulankhula ndi malilime ndi kukweza Mulungu17. Pamenepo Petro anayankha, 47Kodi wina akhoza kukaniza madzi kuti awa abatizidwe, amene alandira Mzimu Woyera monga ifenso tinalandira? 48Ndipo iye anawalamulira iwo kuti abatizidwe mdzina la Ambuye. Pamenepo iwo anampempha iye kukhala masiku ena.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu13Elohimu14Elohimu15Elohimu16Elohimu17Elohimu