Mutu-2

1Ana anga, zinthu izi ndikulemberani cholinga kuti musachimwe; ndipo ngati wina achimwa, tili naye woyang’anira ndi Atate, Yesu Khristu wolungamayo; 2ndipo iye ndi chotetezera ku machimo athu; koma osati athu okha, komanso adziko lonse lapansi.

3Ndipo pamenepo ife tazindikira kuti timdziwa iye, ngati tisunga malamulo ake. 4Iye amene anena kuti, Ndimdziwa iye, ndipo sasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo choonadi mwa iye mulibe; 5koma aliyense amene asunga mau ake, mwa iye zoonadi chikondi cha Mulungu1 chamalizidwa. M’menemo ife tizindikira kuti tili mwa iye. 6Iye amene anena kuti akhala mwa iye akuyenera, kuyenda monga anayendanso iye mwini.

7Okondedwa, sindikulemberani lamulo latsopano kwa inu, koma lamulo lakale lomwe, limene munakhala nalo kuyambira pachiyambi. Lamulo lakale ndi mau amene inu munawamva. 8NdikuIemberaninso lamulo latsopano kwa inu, chinthu chimene chili choona mwa iye ndi mwa inu, chifukwa mdima ukuchoka ndipo kuunika kwenikweni kwawala kale. 9Iye amene anena kuti ali kuunika, ndipo adana naye m’bale wake, ali mu mdima kufikira tsopano. 10Iye amene akonda m’bale wake akhala m’kuunika, ndipo palibe kanthu kokhumudwitsa mwa iye. 11Koma iye amene adana naye m’bale wake ali mu mdima, ndipo ayenda mu mdima, ndipo sadziwa kumene iye akupita, chifukwa m’dima watseka m’maso mwake.

12NdikuIemberani inu, ana, chifukwa machimo anu akhululukidwa chifukwa cha dzina lake.

13Ndikulemberani inu, atate, chifukwa mwam’dziwa iye kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani inu, anyamata, chifukwa mwamlaka woipayo. NdikuIemberani inu, ana, chifukwa mwam’dziwa Atate.

14Ndikulemberani inu, atate, chifukwa mwam’dziwa iye kuyambira pachiyambi.

NdikuIemberani inu, anyamata, chifukwa muli ndi mphamvu, ndipo mau a Mulungu2 akhala mwa inu, ndipo inu mwamlaka woipayo. 15Musakonde dziko lapansi, kapena zinthu zopezeka m’menemo. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye; 16chifukwa zonse zimene zili m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi, ndi chilakolako cha maso, ndi matamandidwe a moyo, sizili za Atate, koma za dziko lapansi. 17Ndipo dziko lapansi likupita, ndi zilakolako zake, koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu3 akhala kwa muyaya.

18Ana inu, ndi nthawi yotsiriza iyi, ndipo, molingana ndi momwe munamvera kuti wokana Khristu akubwera, ngakhale tsopano pabwera wokana Khristu ambiri, pamenepo ife tizindikira kuti ndi nthawi yotsiriza. 19Iwo anatuluka pakati pathu, koma sanali a ife ayi; pakuti akanakhala a ife, akanakhalabe ndi ife, koma kuti akaonekere kuti iwo sali a ife. 20Ndipo inu muli nako kudzodza kochokera kwa Woyerayo, ndipo inu mudziwa zinthu zonse. 21Sindinalembere kwa inu pachifukwa chakuti simudziwa choonadi, koma chifukwa chakuti mudziwa choonadi, ndipo kuti palibe bodza limene limachokera ku choonadi. 22Ndani amene ali wabodza koma iye amene amakana kuti Yesu ndi Khristu? Iyeyu ndi wokana Khristu amene amakana Atate ndi Mwana. 23Aliyense amene amakana Mwana alibenso Mwana; iye amene avomereza Mwana alinso ndi Atate. 24Koma kwa inu chimene munachimva kuyambira pachiyambi chikhale mwa inu: ngati chimene munachimva kuyambira pachiyambi chikhala mwa inu, inunso mudzakhala mwa Mwana ndi mwa Atate. 25Ndipo limeneli ndilo lonjezano limene iye anatilonjeza ife, moyo wosatha. 26Zinthu zimenezi ndakulemberani inu zokhudza iwo amene angakusocheretseni: 27ndipo inu eni, kudzodza kumene munalandira kuchokera kwa iye kukhala mwa inu, ndipo simufunikira kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzodza komweko kukuphunzitsani inu monga kwa zinthu zonse, ndipo kuli choonadi osati bodza, ndipo ngakhale kwaphunzitsidwa kwa inu, mukhazikika mwa iye.

28Ndipo tsopano, ana inu, khalani mwa iye, kuti ngati adzaonetsedwa tidzakhale nako kulimbika, ndi kuti tisachititsidwe manyazi kwa iye pakubwera kwake.

29Ngati inu mudziwa kuti iye ali wolungama, dziwani kuti aliyense amene amachita chilungamo anabadwa mwa iye.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu