Mutu 1
1Paulo, kapolo wa Yesu Khristu, wotchedwa mtumwi, wopatulidwa ku Uthenga Wabwino wa Mulungu1, 2(umene Iye analonjezeratu mwa mneneri wake m’malembo woyera,) 3wokhudza Mwana wake (wotuluka m’mbewu ya Davide monga mwa thupi, 4wotsimikizika Mwana wa Mulungu2 mu mphamvu, molingana ndi Mzimu woyera, mwa kuuka kwa (akufa) Yesu Khristu Ambuye wathu; 5mwa ameneyu talandira chisomo ndi utumwi m’malo mwa dzina lake, pakumvera mwa chikhulupiliro pakati pa mitundu yonse, 6mwa amenewo muli inunso oyitanidwa a Yesu Khristu: 7kwa onse amene ali mu Roma, okondedwa a Mulungu3, otchedwa oyera mtima: Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu4 Atate wathu ndi Ambuye [wathu] Yesu Khristu. 8Poyamba, ndiyamika Mulungu5 wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, kuti chikhulupiliro chanu chadziwika padziko lonse lapansi. 9Pakuti Mulungu6 ndiye mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga mu Uthenga Wabwino wa Mwana wake, kuti kosalekeza sindinasiye kukutchulani inu, 10nthawi zonse m’mapemphero anga, mwanjira ina iliyonse tsopano ndikalemeretsedwe mwa chifuniro cha Mulungu7 ndikadze kwa inu. 11Pakuti ndifunitsitsa zedi kukuonani inu, kuti ndikayikize mwa inu mphatso zina za uzimu kukukhazikitsani inu; 12ndiko kuti, kukhala ndi chitonthozo chofanana pakati panu, aliyense monga mwa chikhulupiliro [chimene chili] mwa wina, cha inu ndi cha ine chomwe. 13Koma sindifuna kuti inu mukhale mbuli, abale, kuti kawirikawiri ndinakonza zobwera kwa inu, (ndipo ndakhala ndikuletsedwa kufikira nthawi yino,) kuti ndikaone zipatso zina pakatinso panu, ngakhale monganso pakati pa amitundu ena. 14Ine ndili wa mangawa kwa Ahelene ndi akunja omwe, kwa anzeru ndi opanda nzeru omwe: 15chomwecho, monga molingana ndi ine, ndili wokonzeka kulalikira Uthenga Wabwino kwa inunso amene muli m’Roma.
16Pakuti ine ndilibe manyazi ndi Uthenga Wabwino; pakuti mphamvu ya Mulungu8 ku chipulumutso, kwa aliyense amene akhulupilira, poyamba kwa Ayuda ndi Ahelene omwe: 17pakuti kulungama kwa Mulungu9 kwaonekera m’menemo, pa mfundo ya chikhulupiliro, kupita ku chikhulupiliro: molingana ndi m’mene kunalembedwera, Koma olungama adzakhala mwa chikhulupiliro.
18Pakuti wavumbulutsidwa mkwiyo wa Mulungu10 kuchoka kumwamba pa chisapembedzo chonse, ndi kusalungama kwa anthu opondereza choonadi mosalungama.
19Chifukwa chimene chidziwika cha Mulungu11 chaonekera pakati pawo, pakuti Mulungu12 wachionetsera kwa iwo, 20pakuti kuchokera ku chilengedwe cha dziko lapansi zinthu zosaoneka za Iye zaoneka, zazindikirika mwa malingaliro kudzera mu zinthu zimene zinapangidwa, mu mphamvu yake ya muyaya ndi umulungu, — monganso kuwaonetsera iwo kuti adzasowe chowiringula.
21Chifukwa, podziwa Mulungu13, iwo anamlemekeza [Iye] osati ngati Mulungu14, kapenanso kukhala oyamika; koma anakhala opanda pake m’malingaliro awo, ndipo mtima wawo posazindikira kuti mitima yawo inadetsedwa: 22poziyesa okha kukhala a nzeru, anakhala opusa, 23ndipo anasintha ulemerero wa Mulungu15 wopanda chivundi kukhala wofanana ndi chifanizo cha munthu wa chivundi ndi cha mbalame ndi cha nyama yoyendayenda ndi cha zokwawa. 24Pamenepo Mulungu16 anawaperekanso ku zilakolako za mitima yao ku zonyansa, kusalemekeza matupi awo pakati pawo: 25amene anasintha choonadi cha Mulungu17 kukhala chabodza, ndipo analemekeza ndi kutumikira cholengedwa kuposa Iye amene analenga [icho], amene ali wodalitsika nthawi zonse. Amen. 26Pa chifukwa chimenechi Mulungu18 anawapereka iwo ku zilakolako zamanyazi; pa akazi awo anasintha machitidwe a chibadwidwe m’kusemphana ndi chilengedwe; 27ndipo momwemonso amuna kuchita mwa manyazi, ndi kulandira mwa iwo okha mphoto ya kulakwa kwao imene inali yowayenera. 28Ndipo molingana iwo sanaganize kukhala ndi Mulungu19 m’chidziwitso [chao], Mulungu20 anawapereka iwo m’chidziwitso cha malingaliro awo kuchita zinthu zosayenera; 29podzala ndi kusalungama konse, zoipa, kusilira, dumbo, kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani, 30miseche, udani ndi Mulungu21, chipongwe, kunyada, kudzitukumula, oyambitsa zinthu zoipa, osamvera makolo, 31opanda nzeru, osakhulupilira, opanda chikondi cha chibadwidwe, opanda chifundo; 32amene ngakhale podziwa kuweruza kolungama kwa Mulungu22, kuti iwo ochita zinthu zimenezi akuyenera imfa, osati kungozichita kokha, koma avomerezana ndi iwo akuzichita.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu>6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu>11Elohimu12Elohimu13Elohimu14Elohimu15Elohimu>16Elohimu17Elohimu18Elohimu19Elohimu20Elohimu21Elohimu>22Elohimu