Mutu 11
1Ndipo atumwi ndi abale amene anali mu Yudeya anamva kuti amitundunso alandira mau a Mulungu1; 2ndipo pamene Petro anakwera kupita ku Yerusalemu, iwo amene anali a mdulidwe anatsutsana ndi iye, 3nanena, Iwe unapita kwa anthu osadulidwa ndipo unadya nawo pamodzi. 4Koma Petro anayamba kufotokozera [nkhaniyo] kwa iwo mwatchutchutchu, nanena, 5Ine ndinali mu mzinda wa Yopa kupemphera, ndipo m’kukomoka ndinaona masomphenya, chotengera china chikutsika ngati nsalu yaikulu, chikutsitsidwa mbali zonse zinayi kuchokera kumwamba, ndipo chinafikira pa ine: 6chimenecho ndinachipenyetsetsa ndi maso anga, ndinalingalira, ndipo ndinaona nyama za miyendo inayi za padziko lapansi, ndi nyama za kuthengo, ndi zinthu zokwawa, ndi mbalame za mlengalenga. 7Ndipo ndinamva mau akunena kwa ine, Tauka Petro, uphe ndipo udye. 8Ndipo ine ndinati, nkosatheka, Ambuye, pakuti chawamba kapena chodetsedwa sichinaloweko m’kamwa mwanga. 9Ndipo mau anayankhulidwa kachiwiri kuchokera kumwamba, Chimene Mulungu2 wachiyeretsa, usachiyese iwe chawamba. 10Ndipo izi zinachitika katatu konse, ndipo zinatengedwanso zonse kupita kumwamba; 11ndipo taonani, nthawi yomweyo amuna atatu anabwera kunyumba kumene ine ndinali, otumizidwa kwa ine kuchokera ku Kaisareya. 12Ndipo Mzimu ananena kwa ine kuti ndipite nawo, ndisakayikire kalikonse. Ndipo anatsagana nane abalenso asanu ndi m’modzi awa, ndipo tinalowa mnyumba ya munthuyo, 13ndipo iye anatifotokozera ife m’mene anaonera mngelo mnyumba mwake, atayimilira ndi kuti [kwa iye], tumiza [amuna] ku Yopa ndi kukatenga Simoni, amene amatchulidwanso Petro, 14amene akalankhula mau kwa iwe amene udzapulumutsidwa nawo, iwe pamodzi ndi banja lako lonse. 15Ndipo pamene ine ndinayamba kulankhula, Mzimu woyera anagwa pa iwo komanso ngakhale pa ife monga anachitira poyamba paja. 16Ndipo ine ndinakumbukira mau a Ambuye, m’mene ananena, Yohane anabatiza ndi madzi, koma iwe udzabatizidwa ndi Mzimu Woyera. 17Ngati pamenepo Mulungu3 anawapatsa iwo mphatso yomweyo monganso kwa ife pamene tinakhulupilira pa Ambuye Yesu Khristu, nanga ndine ndani kuti ndikanize Mulungu4? 18Ndipo pamene anamva zinthu izi anakhala du!, nalemekeza Mulungu5, nati, Pamenepodi Mulungu6 anaperekanso kwa amitundu kulapa kupita ku moyo.
19Pamenepo iwo amene anamwazikana kupita kunja kudzera m’chisautso chimene chinachitika pa nthawi ya Stefano, anadutsira [m’dzikolo] kupita ku Foinike ndi Kupro ndi Antiokeya, osalankhula mau kwa wina aliyense koma kwa Ayuda okha. 20Koma panali ena a iwo, aku Kupro ndi Kurene, amene polowa mu Antiokeya analankhulanso kwa Ahelene, kulalikira uthenga wabwino wa Ambuye Yesu. 21Ndipo dzanja la Ambuye linali nawo, ndipo khamu lalikulu linakhulupilira ndipo linatembenukira kwa Ambuye. 22Ndipo mbiri yokhudza iwo inafika m’makutu a Mpingo umene unali mu Yerusalemu, ndipo anamutuma Barnaba apite kufikira ku Antiokeya: 23amene, pofika ndi kuona chisomo cha Mulungu7, anakondwera, ndipo anawadandaulira onse ndi cholinga choti mtima wao ukhalebe ndi Ambuye; 24pakuti iye anali munthu wabwino ndi wodzala ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiliro; ndipo khamu lalikulu [la anthu] linaonjezeka kwa Ambuye. 25Ndipo iye anapita ku Tariso kukafunafuna Saulo. 26Ndipo pamene anamupeza [iye], anam’bweretsa ku Antiokeya. Ndipo zinali kwa iwo kuti kwa chaka chathunthu anasonkhana pamodzi mu mpingo naphunzitsa khamu lalikulu: ndipo ophunzira anatchulidwa koyamba Akhristu ku Antiokeya.
27Tsopano m’masiku amenewa aneneri anatsikira kuchoka ku Yerusalemu kupita ku Antiokeya; 28ndipo m’modzi wa iwo, dzina lake Agabo, anayimilira natsimikizira mwa Mzimu kuti padzakhala chilala chachikulu padziko lonse lapansi lokhalamo anthu, zimene zinakwanitsidwa m’masiku a Klaudiyo. 29Ndipo iwo anatsimikizika, molingana ndi wina aliyense wa ophunzira monga anakhoza, aliyense wa iwo kuwatumiza kwa abale amene amakhala mu Yudeya, kutumikira [kwa iwo]; 30zimenenso iwo anachita, kutumiza kwa akulu padzanja la Barnaba ndi Saulo.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu