Mutu 11

1Tsopano panali [munthu] wina wodwala, Lazaro wa ku Betaniya, wa kumudzi kwa Mariya ndi Marita m’bale wake. 2Ameneyu anali Mariya amene anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira bwino ndi kupukuta mapazi ake ndi tsitsi lake, amene mlongo wake amadwala. 3Pamenepo alongo ake anamtumizira Iye uthenga, nanena, Ambuye, taonani, iye amene mumkonda akudwala. 4Koma pamene Yesu anamva [ichi], anati, Kudwala uku sikomutengera ku imfa, koma kwa ulemelero wa Mulungu1, kuti Mwana wa Mulungu2 alemekezedwe nako. 5Tsopano Yesu anakonda Marita, ndi m’bale wake, ndi Lazaro. 6Kotero pamene Iye anamva, kuti akudwala, anakhala masiku awiri pamalo pamene Iye analipo. 7Kenako zitatha izi Iye anati kwa ophunzira ake, Tiyeni tipitenso ku Yudeya. 8Ophunzira anati kwa Iye, Rabi, [ngakhale kuti] tsopano Ayuda akufuna kukugendani, ndipo Inu mukufuna kupitanso? 9Yesu anayankha, Kodi sikuli maola khumi ndi awiri pa tsiku? Ngati munthu ayenda masana, sangapunthwe, chifukwa amawona kuwala kwa dziko lapansili; 10koma ngati munthu ayenda usiku, amapunthwa, chifukwa kuwala sikuli mwa iye. 11Zinthu izi analankhula Iye; ndipo zitapita izi anati kwa iwo, Lazaro, bwenzi lathu, wagona tulo, koma Ine ndipite kuti ndikam’dzutse ku tulo. 12Pamenepo ophunzira anati kwa Iye, Ambuye, ngati wagona tulo, iye apeza bwino. 13Koma Yesu amalankhula za imfa yake, koma iwo amaganiza za kugona kopumula. 14Pamenepo Yesu anati kwa iwo mwachindunji, Lazaro wamwalira. 15Ndipo ndikondwera chifukwa cha inu kuti Ine kunalibeko kumeneko, cholinga kuti inu mukhulupilire. Koma tiyeni tipite kwa iye. 16Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira amzake, Tiyeninso nafe tipite, kuti tikafere pamodzi ndi Iye.

17Pamenepo Yesu pofika anapeza kuti iye anakhala kale ali m’manda kwa masiku anayi. 18Tsopano Betaniya anali pafupi ndi Yerusalemu, pafupifupi mastadiya khumi ndi asanu, 19ndipo ambiri mwa Ayuda anabwera kwa Marita ndi Mariya, kuti akamutonthoze zokhudza mlongo wake. 20Kenako Marita, pamene anamva kuti Yesu akubwera, anapita kukakumana naye; koma Mariya anakhala mnyumba. 21Pamenepo Marita anati kwa Yesu, Ambuye, mukanakhala kuti munali kuno, mlongo wanga sakanamwalira; 22komabe kufikira pano ndikudziwa, kuti kalikonse kamene Inu mudzapempha kwa Mulungu3, Mulungu4 adzakupatsani Inu. 23Yesu anati kwa iye, Mlongo wako adzazukanso. 24Marita anati kwa Iye, Ndikudziwa kuti adzazukanso tsiku lomaliza la chiukitso. 25Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: iye wokhulupilira pa Ine, ngakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; 26ndipo aliyense wakukhala ndi moyo nakhulupilira pa Ine sadzamwalira konse. Kodi ukhulupilira zimenezi? 27Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; ndikhulupilira kuti ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu5, amene akudza m’dziko lapansi. 28Ndipo atalankhula izi, anachoka ndi kukayitana m’bale wake Mariya mwachinsinsi, nanena, Mphunzitsi wabwera ndipo akukuyitana. 29Pamene iye anamva [ichi], ananyamuka mwachangu napita kwa Iye. 30Tsopano Yesu anali asanafike m’mudzimo, koma anali pamalo pamene Marita anabwera kudzakumana naye. 31Pamenepo Ayuda amene anali naye mnyumba ndi kumtonthoza, powona kuti Mariya anauka mwachangu ndi kutuluka panja, anamtsatira iye, nanena, Akupita kumanda, kuti akalire kumeneko. 32Pamenepo Mariya, pamene anafika kumene kunali Yesu, pomuona Iye, anagwa pamapazi ake, nanena kwa Iye, Ambuye, mukanakhala kuti muli kuno, mlongo wanga sakanamwalira. 33Pamenepo Yesu, powona kuti iye akulira, ndi Ayuda amene anali naye amaliranso, anakhudzika kwambiri mu mzimu, ndipo anavutika, 34ndipo anati, Kodi mwamuyika kuti? Iwo anati kwa Iye, Ambuye, bwerani ndipo mudzaone. 35Yesu analira. 36Pamenepo Ayuda anati, Taonani m’mene amamkondera iye! 37Ndipo ena mwa iwo anati, Kodi [munthu] uyu, siamene anatsegula maso a [munthu] wakhungu, sakadapanganso kuti [munthu] uyu asamwalire? 38Pamenepo Yesu, pokhudzika kwambiri mwa Iye yekha, anabwera kumanda. Tsopano linali phanga, ndipo mwala unayikidwa pamenepo. 39Yesu anati, Chotsani mwala. Marita, mlongo wake wa womwalirayo, anati kwa Iye, Ambuye, wayamba kale kununkha, pakuti wakhala masiku anayi ali [m’menemo]. 40Yesu anati kwa iye, Kodi sindinanene kwa iwe, Kuti ngati ukhulupilira, udzaona ulemelero wa Mulungu6? 41Pamenepo iwo anachotsa mwala. Ndipo Yesu anakweza maso ake nati, Atate, ndikuyamikani kuti munandimva Ine; 42koma Ine ndinadziwa kuti Inu mumandimva Ine nthawi zonse; koma chifukwa cha khamu lakuimilira pozungulira ndanena [ichi], kuti akhulupilire kuti Inu munandituma Ine. 43Ndipo atalankhula izi, Iye anafuula ndi mau okweza, Lazaro, tuluka. 44Ndipo womwalirayo anatuluka, ali womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda, ndipo nkhope yake inali yokulungidwa ndi chitambaya. Yesu anati kwa iwo, M’masuleni ndipo mlekeni apite.

45Pamenepo ambiri mwa Ayuda anabwera kwa Mariya ndipo anaona zimene Iye anachita, nakhulupilira pa Iye; 46Koma ena mwa iwo anapita kwa Afarisi ndipo anawafotokozera iwo zimene Yesu anachita. 47Pamenepo ansembe akulu, ndi Afarisi anayitanitsa msonkhano wa akulu, ndipo anati, Kodi tichite chiyani? Pakuti munthu uyu akuchita zizindikiro zambiri. 48Ngati timlekerera, onse adzakhulupilira pa Iye, ndipo Aroma adzabwera ndi kutilanda malo athu ndi dziko lathu. 49Koma wina wa iwo, Kayafa, pokhala mkulu wa ansembe chaka chimenecho, anati kwa iwo, Palibe chimene mukudziwa 50kapena simuganiza kuti ndi kopindulitsa kwa inu kuti munthu m’modzi akafe chifukwa cha anthu, ndipo kuti mtundu wonse usaonongeke. 51Koma izi sanalankhule pa iye yekha; koma pokhala mkulu wa ansembe chaka chimenecho, ananenera kuti Yesu adzafa chifukwa cha mtunduwo; 52koma osati kwa mtundu okha, koma kutinso Iye akasonkhanitse pamodzi ana a Mulungu7 obalalitsidwawo. 53Pamenepo kuyambira tsiku limenelo anapangana kuti akamuphe Iye. 54Pamenepo Yesu sanayendenso poyera pakati pa Ayuda, koma anachokapo pamenepo nalowa m’dziko lowandikana ndi chipululu, ku mzinda wotchedwa Efraimu, ndipo kumeneko anayenda pamodzi ndi ophunzira.

55Koma Pasaka wa Ayuda anali pafupi, ndipo ambiri anapita ku Yerusalemu kuchokera ku miraga pasaka asanafike, kuti akadziyeretse okha. 56Pamenepo iwo anamufuna Yesu, ndipo anati mwa iwo okha, atayimilira m’kachisi, Mukuganiza bwanji? Kuti sabwera ku phwando? 57Tsopano ansembe akulu ndi Afarisi anapereka lamulo kuti ngati wina akudziwa kumene Iye ali, awadziwitse, kuti akamtenge Iye.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu