Mutu 3
1Chotsalira, abale, tipempherereni ife, kuti mau a Ambuye athamange ndi kulemekezedwa, monganso ndi inu; 2ndi kuti tilanditsidwe kwa anthu osayenera ndi oipa, pakuti chikhulupiliro sicholowa cha tonse. 3Koma Ambuye ali wokhulupirika, amene adzakukhazikitsani inu nakutetezani ku choipa. 4Komatu ife timakhulupilira mwa Ambuye monganso kwa inu, kuti zinthu zimene tikulamulirani, kuti inu nonse muchita komanso mudzachita. 5Komatu Ambuye atsogolera mitima yanu m’chikondi cha Mulungu1, ndi m’chipiliro cha Khristu.
6Tsopano ife tikulamulirani inu, abale, m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti mutalikirane ndi m’bale aliyense woyenda mosayenera ndi kuyenda osati monga mwa langizo limene analandira kwa ife. 7Pakuti mudziwa inu nokha m’mene muyenera kukhalira otsanza ife, chifukwa ife sitinayende kosayenera pakati panu; 8kapenanso kudya mkate wa ulere kwa aliyense; komatu movutikira ndi mopsinjika kugwira ntchito usiku ndi usana kuti tisalemetse wina aliyense wa inu: 9osati kuti tilibe ufulu, koma kuti tikapereke tokha chitsanzo kwa inu, cholinga kuti mukatitsanze ife. 10pakutinso pamene ife tinali ndi inu tinakulamulirani inu ichi, kuti ngati munthu safuna kugwira ntchito. Musamulole kuti adye. 11Pakuti tikumva kuti alipo ena amene akuyenda kosayenera pakati panu, sagwira konse ntchito, koma kusokoneza ena. 12Tsopano kwa otere ife tikukulamulirani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu Khristu, kuti iwowa agwire ntchito mwa chete ndi kudya mkate waowao. 13Koma inu, abale, musaleme pakuchita zabwino. 14Koma ngati wina samvera mau athu m’kalatayu, myang’anireni ameneyo, ndipo musayanjane naye, kuti achite manyazi iye mwini; 15ndipo musamtenge iye ngati mdani, koma mchenjezeni iye monga m’bale. 16Komatu Ambuye wa mtendere iye mwini akupatseni inu mtendere wopitilira mwanjira ina iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.
17Malonje mwa dzanja langa ine, Paulo, amene ndimayika mu kalata ina iliyonse; chomwecho ndikulemberani. 18 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.
1Elohimu