Mutu 7

1Kodi ndinu mbuli, abale, (pakuti ine ndikulankhula kwa iwo odziwa lamulo,) kuti lamulo limalamulira pa munthu pokhapokha munthuyo ali moyo?2Pakuti mkazi wokwatiwa amangika mu lamulo la kwa mwamuna wake pokhapokha mwamunayo ali ndi moyo; koma ngati mwamunayo amwalira, iye wamasuka ku lamulo la mwamuna wakeyo:3Chomwecho pamenepo, mwamunayo pokhala ndi moyo, iye adzatchedwa wachigololo ngati akwatiwa kwa mwamuna wina; koma ngati mwamunayo amwalira, ali womasuka ku lamulo, sakhalanso wachigololo, ngakhale wakwatiwa ndi mwamuna wina.4Kotero kuti, abale anga, inunso mwayesedwa akufa ku lamulo mwa thupi la Khristu, kuti mukakhale a wina, amene waukitsidwa pakati pa akufa, cholinga kuti tikabereke chipatso kwa Mulungu1.

5Pakuti pamene tinali mthupi zilakolako za machimo, zimene zinali mwa lamulo, zinalamulira thupi lathu kubereka chipatso ku imfa;6koma tsopano tili omasuka ku lamulo, kufa ku chimene chinkatimanga, kuti tikatumikire mu mzimu watsopano, osati mu chilembo chakale.

7Kodi tidzalankhula chiyani pamenepo? Kodi lamulo [ndi] tchimo? Musaganize choncho. Koma ine sindikanadziwa tchimo, pokhapokha mwa lamulo: pakuti sindinakhale nako kutsutsikanso kwa chikhumbokhumbo chonyansa pokhapokha lamulo litanena, usasilire;8koma tchimo, linapeza mpata wakunditsutsa mwa lamulo, kulamulira mwa ine chikhumbokhumbo chilichonse; pakuti popanda lamulo tchimo [linali] lakufa.9koma ndinali wakufa nthawi yina popanda lamulo; koma lamulo litabwera, tchimo linatsitsimuka, koma ine ndinali wakufa.10Ndipo lamulo, limene [linali] la moyo, linapezeka [monga] kwa ine [kukhala] la kuimfa:11pakuti tchimo, linapeza mpata wakutsutsidwa ndi lamulo, kundinamiza ine, ndipo ndinaphedwa nalo.12Kotero kuti lamulo lilidi loyera, ndipo chilamulo chili choyera, ndi cholungama, ndi chabwino.13Kodi pamenepo chimene chinali chabwino chasanduka imfa kwa ine? Musaganize choncho. Koma tchimo, kuti likaoneke ngati tchimo, kukhala imfa kwa ine pa chimene chili chabwino; cholinga kuti tchimo mwa lamulo likhale lopyoza m’machimwidwe.14Pakuti tidziwa kuti lamulo ndi lauzimu: koma ine mwathupi, ndinagulitsidwa pansi pa tchimo.15Pakuti pa chimene ine ndichita, sichikhala cha ine: pakuti chimene sindifuna, chimenechi ndimachichita; koma chimene ndidana nacho, chimenechi ndimachichita.16Koma ngati chimene sindifuna chimenechi ndichichita, ndivomereza ku lamulo kuti ndi labwino.17Tsopano pamenepo sindinenso amene ndichita ichi, koma tchimo lopezeka mwa ine.18Pakuti ndidziwa kuti mwa ine, kunena kuti, m’thupi mwanga, chabwino sichikhalamo: pakuti kufunitsitsa kulipo mwa ine, koma kuchita cholondola ndimalephera.19Pakuti ine sindichita chabwino chimene ndikuyenera kuchichita; koma choipa chimene sindikuyenera kuchita, chimenecho ndichichita.20Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, sindinenso amene ndikuchita, koma tchimo limene lokhala mwa ine.21Pamenepo ndimapeza lamulo pa ine amene ndikuyenera kuchita chabwino, kuti mwa ine choipa chili pamenepo.22Pakuti ine ndimakondwera mu lamulo la Mulungu2 molingana ndi munthu wa mkati:23koma ndimaona lamulo lina mkati mwanga, likuchita nkhondo motsutsana ndi lamulo la m’malingaliro mwanga, ndi kundibweretsa ine mu ukapolo wa lamulo la tchimo limene limapezeka mkati mwanga.24Munthu wosauka ine! Ndani adzandilanditsa ine ku thupi la imfa ili?25Ndiyamika Mulungu3, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Kotero pamenepo ine mwini ndi malingaliro anga kutumikira lamulo la Mulungu4; koma ndi thupi kutumikira lamulo la tchimo.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu