Mutu 7

1Koma pokhudza zinthu zimene munandilembera ine: Ndikwabwino kuti mwamuna asakhudze mkazi; 2koma chifukwa cha madama, aliyense wa inu akhale ndi mkazi wa iye yekha, ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wa iye yekha. 3Mwamuna akwaniritse udindo wake kwa mkazi wake, chimodzimodzinso mkazi kwa mwamuna wake. 4Mkazi alibe ulamuliro pa thupi lake, koma mwamuna wake: chimodzimodzinso mwamuna alibe ulamuliro pa thupi lake, koma mkazi ndiye. 5Musakanizane wina ndi mzake, pokhapokha, mutagwirizana mwa kanthawi kuti mudzipereke nokha ku pemphero, ndipo mukhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni chifukwa cha kusadziletsa kwanu. 6Koma ichi ndinena, mokupemphani, osati mokulamulani. 7Tsopano ndifuna amuna onse akhale ngati ine mwini: komatu aliyense ali nayo mphatso yake ya Mulungu1: wina iyi, ndi wina iyo. 8Koma ndinena kwa iwo osakwatira ndi akazi amasiye, ndi kwabwino kwa iwo kuti akhale monga ine ndili. 9Komatu ngati sangakwanitse kudzisunga, akwatire; pakuti ndi kwabwino kukwatira kusiyana ndi kutentha thupi. 10Koma kwa okwatira ndikulamulirani, osati ine, koma Ambuye, mkazi asalekane ndi mwamuna wake; 11(koma ngatinso adzalekanitsidwa, akhale choncho osakwatiwa, kapena ayanjanitsidwe kwa mwamuna wake;) ndipo mwamuna asasiye mkazi wake. 12Koma kwa ena nonse, ndinena, osati Ambuye, Ngati m’bale wina ali naye mkazi wosakhulupilira, ndipo watsimikizika kukhala naye, asamusiye ameneyo. 13Ndipo mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupilira, ndipo watsimikizika kukhala naye, anamusiye mwamuna ameneyo. 14Pakuti mwamuna wosakhulupilirayo wayeretsedwa mwa mkaziyo, ndipo mkazi wosakhulupilirayo wayeretsedwa mwa m’baleyo; pakutidi kuyambira pamenepo ana anu anakhala osayeretsedwa, koma tsopano ali oyera. 15Koma ngati osakhulupilira achoka, aloleni achoke; m’bale kapena mlongo sali womangika mu nyengo zoterezi, koma Mulungu2 watiyitanira ife mu mtendere. 16Pakuti udziwa bwanji, mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamuna wako? Kapena udziwa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi wako? 17Komabe, monga Ambuye anagawira kwa aliyense, monga Mulungu3 anayitanira aliyense, akayende chomwecho; ndipo pamenepo ndiyikiza m’mipingo yonse. 18Kodi wina anayitanidwa ali wodulidwa? Ameneyo asakhale osadulidwa: kodi wina anayitanidwa ali wosadulidwa? Ameneyo asakhale wodulidwa. 19Mdulidwe uli chabe, ndipo kusadulidwa kuli chabe; komatu kusunga malamulo a Mulungu4. 20Aliyense akhazikike m’mayitanidwe amene iye anayitanidwira. 21Kodi munayitanidwa mudakali kapolo, chimenechi chisakukhudzeni; koma ngati mwapeza mwayi kukhala mfulu, gwiritsani tchito mwayiwo. 22Pakuti kapolo amene wayitanidwa mwa Ambuye ndi mfulu wa Ambuye; chimodzimodzinso mfulu woyitanidwa ali kapolo wa Khristu. 23Inutu munagulidwa ndi mtengo wake; musakhale akapolo a anthu. 24Aliyense m’mene anayitanidwira, abale, akhelebe m’menemo ndi Mulungu5.

25Koma zokhudza anamwali, ndilibe lamulo la Ambuye; koma ine ndipereka maganizo anga, monga wolandira chifundo cha Ambuye kukhala wokhulupirika.

26Pamenepo ndiganiza ine kuti ndi kwabwino, potengera ndi zokhumba za nyengo yino, kuti kwabwino munthu akhale monga alili. 27Kodi mwamangika kwa mkazi? Musamasulidwe; kodi mwamasulidwa kwa mkazi? Musafunefune mkazi. 28Komabe ngati mufunanso kwatirani, simunachimwe; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanachimwe: koma woterewa adzakhala nacho chizunzo m’thupi; koma ine ndikulewetsani inu. 29Koma ichi ndinena, abale, nthawi yatha. Pakuti kwa onse, amene ali ndi akazi, akhale ngati alibe: 30ndipo iwo amene akulira, akhale ngati sakulira; ndipo iwo amene akusangalala, akhale ngati sakusangalala; ndipo iwo amene akugula, akhale ngati alibe kanthu; 31ndipo iwo amene akugwiritsa dziko lapansi, akhale ngati sakuligwiritsa ngati lawo; pakuti zooneka za dziko lapansili zidzapita. 32Komatu ine ndifuna kuti musazitengere. Wosakwatira amasamala zinthu za Mulungu, m’mene angamkondweretsere Ambuye; 33koma iye amene anakwatira amasamala zinthu za dziko lapansi, m’mene angamusangalatsire mkazi wake. 34Palitu kusiyana pakati pa mkazi ndi namwali. Wosakwatiwa amasamala zinthu za Ambuye, kuti akakhale woyera m’thupi komanso mu mzimu; koma iye amene ali wokwatiwa amasamala pa zinthu za dziko lapansi, momwe angasangalatsire mwamuna wake. 35Komatu ine ndilankhula izi pa ubwino wanu womwe; osati kuti ndikakutchereni inu msampha, koma kuti chimene chioneke, ndicho kudikira Ambuye popanda chosokoneza. 36Koma ngati wina aganiza kuti akuchita molakwika pa namwali wake wopalana naye ubwenzi, ngati iye chilakolako chake chiposa msinkhu wake, ndipo kukhale chomwecho, kuti achite chifuniro chake, kuti asachimwe: aloleni akwatirane. 37Koma iye amene ayimikikabe mu mtima mwake, wopanda chosowa, koma ali nawo ulamuliro wa chifuniro chake, ndipo anakhazikitsa ichi mkati mwake kuti adzasunga unamwali wake, ameneyu achita bwino. 38Kotero iye amene akwatira achita bwino; ndipo iye amene sakwatira achita bwino koposa. 39Mkazi amakhala womangika pa nthawi iliyonse imene mwamuna wake ali moyo; koma ngati mwamuna wake amwalira, amakhala womasuka kukwatirana ndi amene iye akufuna, mwa Ambuye mokha. 40Koma amakhala wosangalala akakhala wosakwatiwanso, molingana ndi kuona kwanga; koma ndikuganiza kuti inenso ndili ndi Mzimu wa Mulungu6.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu