Mutu 4
1Pamenepo Yesu anatengedwa ndi Mzimu kupita kuchipululu kukayesedwa ndi mdierekezi: 2ndipo atasala kudya kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku, pambuyo pake Iye anamva njala. 3Ndipo woyesayo anadza kwa Iye nanena, Ngati iwe uli Mwana wa Mulungu, talankhula, kuti miyala iyi isanduke mikate. 4Koma Iye pakuyankha anati, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, komatu mau alionse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.
5Pamenepo mdierekezi anamutenga Iye napita naye ku mzinda woyera, ndipo anamuika pamwamba pa kachisi, 6ndipo anati kwa Iye, ngati uli Mwana wa Mulungu uzigwetse pansi; pakuti kwalembedwa, Iye adzalamulira angelo ake zokhudza Iwe, ndipo m’manja [mwao] adzakunyamula Iwe, kuti phazi lako lingakhudze mwala. 7Yesu anati kwa iye, kwalembedwanso, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.
8Pameneponso mdierekezi anamutengera Iye pamwamba pa phiri lalitali, ndipo anamuonetsa Iye maufumu onse a dziko lapansi ndi ulemelero wao, 9ndipo analankhula kwa Iye, Zinthu zonsezi ndidzakupatsa iwe ngati udzagwada pansi ndi kundilambira ine. 10Pamenepo Yesu anati kwa iye, Choka, Satana, pakuti kwalembedwa, Uzilambira Ambuye Mulungu wako, ndipo Iye yekha umtumikire.
11Pamenepo mdierekezi anamuleka Iye, ndipo taonani, angelo anabwera namutumikira Iye.
12Koma pakumva kuti Yohane anaperekedwa, Iye anachoka napita m’Galileya: 13ndipo atachoka ku Nazarete, Iye anapita ndi kukakhala ku Kapernao, kumene ndi m’mbali mwa nyanja ku malire a Zebuloni ndi Nafitali, 14kuti chikwaniritsidwe chimene chinalankhulidwa mwa Yesaya mneneri, kuti, 15Dziko la Zebuloni ndi dziko la Naftali, njira ya kunyanja kutsidya kwa Yordano, Galileya wa amitundu: 16anthu okhala mu mdima awona kuwala kwakukulu, ndipo kwa iwo akukhala m’dziko ndi mu mthunzi wa imfa, kuwala kwawatulukira. 17Kuyambira nthawi imeneyo Yesu anayamba kuphunzitsa nanena, Lapani, pakuti ufumu wakumwamba wayandikira.
18Ndipo pamene amayenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wotchedwa Petro, ndi Andreya m’bale wake, akuponya khoka lawo m’nyanja, pakuti iwo anali asodzi; 19ndipo Iye analankhula kwa iwo, nditsatireni, ndipo Ine ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu. 20Ndipo iwo pakusiya makoka awo, nthawi yomweyo anamutsatira Iye. 21Ndipo pakupitabe Iye anaonanso abale ena awiri, Yakobo [mwana] wa Zebedayo ndi Yohane m’bale wake, ali m’ngalawa pamodzi ndi atate wao Zebedayo akusoka makoka awo, ndipo Iye anawaitana iwo; 22ndipo iwo, pakusiya ngalawa ndi atate wao, nthawi yomweyo anamtsata Iye.
23Ndipo [Yesu] anayenda kuzungulira Galileya yense, kuphunzitsa m’masunagoge mwao, ndipo pakuphunzitsa uthenga wabwino wa ufumu, ndi kuchiritsa nthenda ina iliyonse komanso kufooka kwina kulikonse kwa mthupi pakati pa anthuwo. 24Ndipo kutchuka kwake kunafika ku dela lonse [la] Suriya, ndipo anabwera nawo kwa Iye onse amene anali kudwala, ovutika ndi nthenda zosiyanasiyana komanso ululu, ndi iwo ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa iwo. 25Ndipo khamu lalikulu linamutsatira Iye kuchokera ku Galileya, ndi Dekapole, ndi Yerusalemu, ndi Yudeya, ndi tsidya la Yordano.