Mutu 22

1Ndipo Yesu pakuyankha analankhulanso kwa iwo m'mafanizo, nati, 2Ufumu wakumwamba wakhala ngati mfumu imene1 inakonza phwando la ukwati wa mwana wake wamwamuna, 3ndipo anatuma akapolo ake kuitana anthu onse amene anaitanidwa ku phwando la ukwati, ndipo iwo sanabwere. 4Anatumanso akapolo ena, nanena, Kauzeni anthu oitanidwa, Taonani, ndakonza phwando langa; ng'ombe zanga ndi nyama zonona za mthengo zaphedwa, ndipo zinthu zonse zakonzeka; bwerani ku phwando la ukwati. 5Koma iwo anapeputsa ichi2 ndipo anachokapo, wina anapita kumunda kwake ndi wina kumalonda ake. 6Ndipo otsalawo, anagwira akapolo ake, nawazunza ndi kuwapha [iwo]. 7Ndipo [pamene] mfumu [inamva za ichi, iyo] inakwiya3, ndipo inatumiza asilikali ake, nawononga anthu akupha aja ndi kuotcha mzinda wao. 8Pamenepo anati kwa akapolo ake, Phwando la ukwati lankonzedwa, komatu oitanidwa sanali oyenera; 9chotero pitani ku mphambano za misewu, ndipo aliyense amene mutamupeze muitaneni ku phwando la ukwati. 10Ndipo akapolo aja anapita mphambano za misewu, ndipo anasonkhanitsa anthu ochuluka amene anawapeza, oipa ndi abwino omwe; ndipo phwando la ukwati linadzadza ndi alendo. 11Ndipo mfumu, pakulowa kuti ikaone alendo, taonani panali munthu amene sanavale chovala cha ukwati. 12Ndipo anati kwa iye, Mzanga, zatheka bwanji iwe kulowa muno osavala chovala cha ukwati? Komatu iye anasowa choyankha. 13Pamenepo mfumu inalankhula kwa atumiki, M'mangeni miyendo ndi manja, ndipo mumtulutse iye, ndipo mumponye mu mdima wakunja: kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. 14Pakuti ambiri ndi oitanidwa, koma ochepa ndiwo osankhidwa. 15Pamenepo anapita Afarisi ndipo anakonza upo wakuti amkole Iye pakulankhula kwake. 16Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira awo pamodzi ndi Aherode, nanena, Mphunzitsi, ife timadziwa kuti ndinu woona ndipo mumaphunzitsa njira ya Mulungu4 m'choonadi, ndipo simusamala za wina aliyense, pakuti simuyang'anira kutchuka4 kwa munthu; 17choncho tatiuzeni zimene inu mukuganiza: Kodi ndi kololedwa kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena ayi? 18Koma Yesu podziwa kuipa mtima kwao, anati, Chifukwa chiyani mukundiyesa Ine, achinyengo inu? 19Tandionetseni Ine ndalama ya msonkho. Ndipo anampatsa Iye ndalama ya msonkho. 20Ndipo anati kwa iwo, Kodi chifanizo ichi ndi kulemba kwake ndi [za] ndani? 21Iwo anati kwa Iye, za Kaisara. Pamenepo Iye anati kwa iwo, Perekani chimene chili cha Kaisara kwa Kaisara, ndipo chimene chili cha Mulungu kwa Mulungu. 22Ndipo pamene anamumva [Iye], iwo anali odabwa, ndipo anamusiya Iye, nachokapo.

23Patsiku limenelo anabwera kwa Iye Asaduki, amene amati kulibe kuuka kwa akufa; ndipo iwo anamfunsa Iye, 24nanena, Mphunzitsi, Mose anati, Ngati munthu amwalira osakhala nawo ana, m'bale5 wake akwatire mkazi wake ndipo adzaukitse mbeu kwa m'bale wakeyo. 25Tsopano tinali nawo ife abale asanu ndi awiri; ndipo woyamba kukwatira anamwalira, ndipo sanakhale ndi mbeu, anasiyira mkazi wake m'bale wake. 26Chimodzimodzinso wachiwiri ndi wachitatu, kufikira wachisanu ndi chiwiri. 27Ndipo kumapeto kwake mkaziyu anamwaliranso. 28M'kuuka kwa akufa ndani mwa asanu ndi awiriwa adzakhala mwamuna wa mkaziyu, pakuti onsewa anakhala ndi iye? 29Ndipo Yesu pakuyankha anati kwa iwo, Inutu mukulakwitsa, osadziwa malembo kapena mphamvu ya Mulungu. 30M'kuuka kwa akufa sakwatira kapena kukwatiwa, koma amakhala ngati angelo a Mulungu a kumwamba. 31Koma zokhudza kuuka kwa akufa, kodi simunawerenge zimene zinalankhulidwa6 kwa inu ndi Mulungu, kunena kuti, 32Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo? Mulungu si Mulungu wa akufa, koma wa amoyo. 33Ndipo pamene makamu anamva [ichi] anali odabwa ndi chiphunzitso chake. 34Koma Afarisi, pakumva kuti iye anawakhalitsa Asaduki chete, anasonkhana pamodzi. 35Ndipo m'modzi wa iwo, wa chilamulo, anamfunsa, namuyesa iye, ndipo anati, 36Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu la m'chilamulo ndi liti? 37Ndipo anati kwa iye7, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse. 38Limeneli ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. 39Ndipo lachiwiri lifanana ndi ilo8, Uzikonda mzako monga iwe mwini. 40Pa malamulo awiri awa chilamulo chonse ndi aneneri zapachikidwa.

41Ndipo Afarisi pakusonkhana pamodzi, Yesu anawafunsa iwo, 42nanena, Kodi mukuganiza chiyani zokhudza Khristu? Kodi Iye ndi mwana wa ndani? Iwo anati kwa Iye, wa Davide. 43Iye ananena9 kwa iwo, Nanga bwanji Davide mu Mzimu anamutchula Iye Ambuye, nanena, 44Ambuye ananena kwa Ambuye wanga, Ukhale padzanja langa lamanja kufikira ndidzaika adani ako pansi pa mapazi ako? 45Ngati pamenepo Davide anamutchula Iye Ambuye, akhala bwanji mwana wake? 46 Ndipo palibe amene anakwanitsa kumuyankha Iye mau, kapenanso kumufunsa kanthu kuyambira tsiku limenelo.

1 'Imene kusonyeza chikhalidwe.' monga mutu 2.6 ndi mutu 7.24. 2 Onani Mfundo pa, Aheb. 2.3. 3 'Ndipo mfumu inapsa mtima,' kumeneku ndiye kuwerenga kolondola. 4 Kapena 'maonekedwe.' 5 Onani Gen. 38.8 ndi Deut. 25.5. 6 Eks. 3.6. 7 Deut. 6.5. 8 Lev. 19.18. 9 Mas. 110.1.