Mutu 3
1Koma dziwa ichi, kuti masiku otsiriza zizafika nthawi zowawitsa; 2pakuti anthu adzakhala ozikonda okha, okonda ndalama, odzikuza, amwano, olankhula moipa, osamvera makolo, osayamika, ochitira chipongwe zopatulika, 3osoweka chikondi cha chibadwidwe, osayanjanitsika, amijedu, okhala ndi zilakolako zoipa, ankhaza, osoweka chikondi pa zabwino, 4owukira, aliuma, amakani opanda pake, okonda zokondweretsa munthu osati kukonda Mulungu1; 5okhala nawo maonekedwe a chipembedzo koma mphamvu yake anayikana: ndipo kwa iwo udzipatule. 6Pakuti mwa iwowa amalowa m’nyumba, ndipo amagwira akazi opusa, olemedwa ndi machimo, otsogozedwa ndi zilakolako zosiyanasiyana, 7kuphunzira nthawi zonse, ndipo osakhoza kubwera ku chidziwitso cha choonadi. 8Tsopano momwemonso Yane ndi Yambre anatsutsana naye Mose, chomwecho awanso amatsutsana ndi choonadi; amuna oipa m’malingaliro, opezeka opanda phindu molingana ndi chikhulupiriro. 9Komatu iwo sadzapita chitsogolo; pakuti kupusa kwao kudzaonekera kwathunthu kwa onse, monganso kupusa kwa ena aja. 10Koma iwe waphunzitsika bwino lomwe ndi chiphunzitso changa, m’mayendedwe, cholinga, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, kupilira, 11mazunzo, zowawa: zowawa zimene zinandichitikira ine m’Atiokeya, m’Ikoniya, m’Lustro; mazunzo amene ine ndinapiliramo; ndipo Ambuye anandipulumutsa ine ku onsewa. 12Ndipodi onse amene akhumba kukhala opembedza mwa Khristu Yesu adzazunzidwa. 13koma anthu oipa ndi onyenga adzaipirabe, adzasocheretsa ndi kusocheretsedwa. 14Koma iwe, khalabe mu zinthu zimene waphunzira, ndi zimene iwe wakhulupirira kwathunthu, podziwa amene anakuphunzitsa; 15ndipo kuti kuchokera ukhanda wako unadziwa malembo opatulika, amene ali othekera kukupatsa nzeru ku chipulumutso, mwa chikhulupiriro chimene chili mwa Khristu Yesu. 16Lemba lililonse linauziridwa mwa umulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, pa kutsutsa, pa kukonza, pa kulangiza molungama; 17ku ti munthu wa Mulungu2 akhale waphumphu, wokonzeka kwathunthu kuchita ntchito iliyonse yabwino.
1Elohimu2Elohimu