Mutu 13
1Moyo ulionse umvere aulamuliro amene ali patsogolo pake. Pakuti palibe ulamuliro koma wochokera kwa Mulungu1; ndipo iwo amene akupezeka anayikidwa ndi Mulungu2. 2Kotero kuti iye amene atsutsana ndi ulamulirowu atsutsana ndi chokhazikitsidwa ndi Mulungu3; ndipo iye amene atsutsana nawo adzibweretsera yekha chiweruziro cha kutsutsika. 3Pakuti oweruza sichiopsezo pa ntchito yabwino, koma pa tchito yoipa. Pamenepo kodi udzakhumba kuchita mantha pa aulamuliro? chita [chimene chili] chabwino, ndipo iwe udzatamandidwa ku chimenecho; 4pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu4 kuchitira chabwino kwa iwe. Koma ngati uchita choipa, chita mantha; pakuti sagwira lupanga pachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu5, wobwezera mkwiyo kwa iwo ochita choipa. 5Pamenepo ndi kofunika kukhala omvera, osati chifukwa choopa mkwiyo, komanso chifukwa cha chikumbumtima. 6Pachifukwa chimenechi mumaperekanso msonkho; pakuti iwowa ali atumiki a Mulungu6, kuchita chinthu chimenechi nthawi zonse. 7Perekani kwa onse ngongole zawo: ngongole kwa eni ake ngongole, msonkho kwa eni ake msonkho; kwa iye woyenera kumuopa, timuope; kwa iye woyenera ulemu, tipereke ulemu. 8Musakhale ndi ngongole kwa munthu, pokhapokha ngati chili chikondi kwa wina ndi mzake: pakuti iye amene akonda mzake akwaniritsa lamulo. 9Pakuti, Usachite chigololo, usaphe, usabe, usasilire; ndipo ngati pali lamulo lina, lamangilirika m’mau amenewa, ndiko kuti, Uzikonda mzako monga uzikonda iwe mwini. 10Chikondi sichichitira mzake choipa; kotero chikondi ndilo lamulo lathunthu.
11Chitaninso ichi, podziwa nthawi, kuti yakwana kale kuti tidzuke kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu chawandikira kusiyana ndi momwe ife tinayambira kukhulupilira. 12Usiku watsala pang’ono kutha, ndipo usana wayandikira; tiyeni chomwecho titaye ntchito za mumdima, ndipo tiyeni tivale zida za kuunika. 13Monga usana, tiyeni tiyende moyenera; osati mu chiwawa ndi kuledzera, osati m’madama, osati m’zinyanso, osati m’magawano ndi nsanje. 14Koma valani Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kukwaniritsa zokhumba zake.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu