Mutu 15
1Ndipo pomwepo m’mawa ansembe akulu, anapangana upo ndi akulu komanso alembi ndi akulu onse a milandu, nam’manga Yesu namtenga, ndi kumpereka [Iye] kwa Pilato. 2Ndipo Pilato anamfunsa Iye, Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda? Ndipo anayankha nati kwa iye, inutu mwatero. 3Ndipo ansembe akulu anam’nenera Iye zambiri. 4Ndipo Pilato anamfunsanso Iye, Kodi sukuyankha kathu? Taona zinthu zambiri zimene iwo akuchitira umboni otsutsana ndi Iwe. 5Komatu Yesu sanayankhebe kanthu kalikonse, kotero Pitalo anadabwa. 6Komatu nthawi ya phwando iye amawatulutsira iwo wandende m’modzi, amene iwo amapempha kuti atulutsidwe. 7Tsopano panali [munthu] wotchedwa Baraba amene anamangidwa ndi iwo amene anakonza mpanduko pamodzi naye, [ndiponso] kuti anapha munthu mu mpandukomo. 8Ndipo khamulo linayamba kufuula kupempha [kuti iye achite] kwa iwo monga momwe amachitira nthawi zonse. 9Koma Pilato anawayankha iwo nati, Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayuda? 10pakuti iye anadziwa kuti ansembe akulu anampereka Iye chifukwa cha njiru. 11Koma ansembe akulu anasonkhezera khamulo kuti iye awamasulire Baraba. 12Ndipo Pilato powayankha anatinso kwa iwo, Kodi ndichite chiyani [kwa Iye] amene mumamutchula kuti Mfumu ya Ayuda? 13Ndipo iwo anafuulanso, Mpachikeni Iye. 14Ndipo Pilato anati kwa iwo, Kodi Iyeyu wachita choipa chanji? Koma iwo anafuulirabe, Mpachikeni Iye. 15Ndipo Pilato, pofuna kulikhazikitsa khamulo, anawamasulira Baraba, ndipo anampereka Yesu, pamene iye anamkwapula, kuti akapachikidwe.
16Ndipo asilikali anamtsogolera Iye ku bwalo lamilandu limene [limatchedwa] Pretorio, ndipo anasonkhanitsa pamodzi gulu lawo lonse. 17Ndipo iwo anamuveka Iye chibakuwa, ndipo anamanga mozungulira mutu wake korona wa minga amene iwo anamuluka. 18Ndipo anayamba kumulankhula, Tikuoneni, Mfumu ya Ayuda! 19Ndipo anamkwapula m’mutu mwake ndi bango, namlavulira Iye, ndipo, popinda maondo awo, anamlambira. 20Ndipo pamene anamchitira chipongwe, anamvula chibakuwa, namveka zovala zake; ndipo iwo anamtsogolera kuti akampachike Iye. 21Ndipo iwo anamkakamiza munthu wina wodutsa panjira, Simoni, waku Kurene, amene amachokera kumunda, tate wawo wa Alesandere ndi Rufu, kuti anyamule mtanda Wake.
22Ndipo anafika naye ku malo [wotchedwa] Gologota, amene, atanthauza, ndiwo Malo a bade. 23Ndipo iwo anampatsa Iye vinyo [kuti amwe] wosakaniza ndi mure; koma Iye sanalandire. 24Ndipo atampachika Iye, anagawana zovala zake pakati [pawo], nachita maere pa iwo, chimene aliyense akuyenera kutenga. 25Ndipo inali ngati ola yachitatu, ndipo iwo anampachika Iye. 26Ndipo lembo la mlandu wake linalembedwa pamwamba: Mfumu ya Ayuda. 27Ndipo pamodzi naye anapachikidwa achifwamba awiri, wina kudzanja lake lamanja, ndi wina kudzanja lamanzere. 28[Ndipo lembo linakwaniritsidwa lakuti, Ndipo Iye anawerengedwa pamodzi ndi ochimwa.]
29Ndipo iwo akudutsa pamenepo anamchitira mwano, napukusa mitu yawo, ndi kunena, Ha! Iwe wakupasula kachisi ndi kumanga kwa masiku atatu, 30udzipulumutse wekha, ndi kutsika pa mtandapo. 31Momwemonso ansembe akulu, ndi alembi, anamchitira chipongwe, nanena wina ndi mzake, Anapulumutsa ena; koma akulephera kudzipulumutsa yekha. 32Lolani tsopano Khristu Mfumu ya Israyeli itsike tsopano pa mtanda, kuti ife tione ndi kukhulupilira. Ndipo iwo amene anapachikidwa naye pamodzi anamdzudzula Iye.
33Ndipo pamene linafika ola lachisanu ndi chimodzi, panagwa mdima padziko lonse kufikira ola lachisanu ndi chinayi; 34ndipo pa ola lachisanu ndi chinayi, Yesu anafuula ndi mau okweza, [nanena], Eloi, Eloi, lama sabakitani? Chimene chili, pa kutanthauzira, Mulungu1 wanga, mwandisiyiranji Ine? 35Ndipo ena mwa iwo akuimilira pamenepo, pamene anamva [ichi], anati, Taonani, akuitana Eliya. 36Ndipo wina, anathamanga nadzadza chinkhupule ndi vinyo wosasa, naika pa bango, napereka kwa Iye kuti amwe, nanena, Lekani, tiyeni tione ngati Eliya adzabwera kumutsitsa Iye.
37Ndipo Yesu, atafuula mokweza, anapereka mzimu wake. 38Ndipo nsalu ya mkachisi inang’ambika kuchokera kumwamba kufikira pansi. 39Ndipo kenturiyo amene anaimilira mopenyana ndi Iye, pamene anaona kuti anapereka mzimu wake anafuula, nati, Zoonadi munthu uyu anali Mwana wa Mulungu2. 40Ndipo analipo akazi amene amaonerera chapatali, ena mwa iwo anali Mariya wa Magadala, ndi Mariya mayi wake wa Yakobo wamng’ono ndi Yose, ndi Salome; 41amenenso, pamene anali mu Galileya, anamtsatira Iye ndi kumtumikira Iye; ndi ena ochuluka amene anabwera naye pamodzi ku Yerusalemu.
42Ndipo pamene kunali madzulo, pakuti inali nthawi yokonzekera, ndilo tsiku la sabata, 43Yosefe wa ku Arimateya, mkulu wa milandu wolemekezeka, amenenso amayembekezera ufumu wa Mulungu3, anabwera, nadzilimbitsa mtima yekha ndi kupita kwa Pilato napempha mtembo wa Yesu. 44Ndipo Pilato anadabwa ngati anali atafa kale; ndipo pamene anamuitanitsa kenturiyo, anamfunsa ngati anali atafa kale. 45Ndipo pamene anadziwa kuchokera kwa kenturiyo, iye anapereka thupilo kwa Yosefe. 46Ndipo anagula nsalu ya bafuta, [ndipo] anamutsitsa Iye, namkulunga mu nsalu ya bafuta, namuika m’manda wosema amene anasemedwa ku thanthwe, nakunkhuniza mwala pakhomo la mandawo. 47Ndipo Mariya wa Magadala ndi Mariya [mayi] wake wa Yose anaonapo pamene Iye anaikidwa.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu