Mutu 2
1Ndipo ine, pamene ndinabwera kwa inu, abale, sindinabwere ndi mau opambana, kapena anzeru, kulengeza kwa inu umboni wa Mulungu1. 2Pakuti sindinatsimikizike kudziwa kanthu kena kalikonse pakati panu kupatula Yesu Khristu, Iye wopachikidwayo. 3Ndipo ine ndinali nanu m’chifooko ndi m’mantha ndi kunjenjemera kwakukulu; 4ndipo mau anga ndi ulaliki wanga, sizinali mau okopa a nzeru, komatu mu chionetsero cha Mzimu ndi mphamvu; 5kuti chikhulupiliro chanu chisayimikike mu nzeru za anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu2.
6Komatu ife timalankhula nzeru pakati pa anthu angwiro; koma osati nzeru ya dziko lapansi, kapena olamulira a dziko lapansili, amene ali chabe. 7Koma ife tilankhula nzeru ya Mulungu3 mwachinsinsi, nzeru yobisika imene Mulungu4 anayikhazikitsiratu pasanakhale nyengo ya pansi pano pa ulemelero wathu: 8imene palibe mwa akalonga a nthawi yino angayidziwe, (pakuti iwo akanadziwa, sakanamupachika Ambuye wa ulemelero;) 9koma molinga ndi momwe kunalembedwera, Zimene maso sanathe kuona, ndi makutu sanathe kumva, ndipo zimene sizinafike mumtima wa munthu, zimene Mulungu5 anawakonzera iwo amene amkonda Iye, 10komatu Mulungu6 wativumbulutsira ife mwa Mzimu wake; pakuti Mzimu amasanthula zinthu zonse, ngakhale zakuya za Mulungu7. 11Pakuti ndani wa anthu amene wadziwa zinthu za munthu kupatula mzimu wa munthu umene uli mwa iye? Chomwechonso zinthu za Mulungu8 palibe amene azidziwa kupatula Mzimu wa Mulungu9. 12Koma ife talandira, osati mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu umene uli wa Mulungu10, kuti tikadziwe zinthu zimene zapatsidwa kwa ife mwa Mulungu11: 13umenenso ife tilankhula, osati mwa mau ophunzitsidwa ndi nzeru ya munthu, koma kuphunzitsidwa mwa Mzimu wa Mulungu12, kulumikidzitsa zinthu za uzimu mwanjira ya uzimu; 14koma munthu wa kuthupi sakhoza kulandira zinthu za Mzimu wa Mulungu13 pakuti zili zopusa kwa iye; ndipo iye sangazizindikire [izo] pakuti zimazindikirika mwa uzimu; 15komatu iye wa uzimu amazindikira zinthu zonse, ndipo iye sazindikiridwa ndi wina aliyense. 16Pakuti ndani amene wadziwa lingaliro la Ambuye, ndani amene adzamulangiza iye? Koma ife tili nalo lingaliro la Khristu.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu