Mutu 3

1Ndipo ine, abale, sindinathe kukulankhulani za uzimu koma za kuthupi, monga makanda mwa Khristu. 2Ine ndakupatsani mkaka kuti mumwe, osati nyama, pakuti simunali okonzeka kulandira, ngakhalenso pano simuli okonzeka; 3pakuti mudakali a kuthupi. Pakuti pali kaduka ndi kulimbana pakati panu, kodi si inu akuthupi, ndipo muyenda molingana ndi umunthu? 4Pakuti wina anena, ndine wa Paulo, ndi wina, ndine wa Apolo, kodi si inu anthu? 5Kodi Apolo ndi ndani, ndipo Paulo ndi ndani? Atumiki otumikira, amene inu munawakhulupilira, ndipo monga Ambuye anaperekera kwa aliyense. 6Ine ndinadzala; Apolo anathilira; koma Mulungu1 wachulukitsa. 7Kotero kuti wodzala ali chabe, chomwechonso wothilira; koma Mulungu2 wochulukitsayo. 8Komatu wodzala ndi wothilira ali amodzi; koma aliyense adzalandira dipo lake molingana ndi ntchito yake. 9Pakuti ndife antchito amzake a Mulungu3; inu ndi zolimidwa za Mulungu4, chomangidwa cha Mulungu5. 10Molingana ndi chisomo cha Mulungu6 chimene chapatsidwa kwa ine, monga m’misiri womanga waluso, ine ndamanga maziko, ndipo wina wamanga pamenepo. Koma aliyense ayang’anire m’mene akumangira pamenepo. 11Pakuti palibe maziko ena munthu akhoza kuyika kupatula maziko amene anayikidwa, amene ndi Yesu Khristu. 12Tsopano ngati munthu amanga pa maziko amenewa, golide, siliva, miyala ya mtengo wapatali, mitengo, udzu, tsekera, 13ntchito ya aliyense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa lidzaonetsedwa m’moto; ndipo motowo udzayesa ntchito ya aliyense chimene ili. 14Ngati ntchito ya aliyense imene iye anamanga pa maziko idzakhala, iye adzalandira mphoto. 15Ngati ntchito ya aliyense idzatenthedwa, adzataya zake, koma iye adzapulumuka, komatu monga kudutsa pa moto. 16Kodi inu simudziwa kuti ndinu kachisi wa Mulungu7, ndi [kuti] Mzimu wa Mulungu8 akhalira mwa inu? 17Ngati wina aliyense awononga kachisi wa Mulungu9, ameneyo Mulungu10 adzamuononga; pakuti kachisi wa Mulungu11 ndi woyera, ndipo chomwechonso muli inu. 18Aliyense asadzinamize yekha: ngati wina aliyense aganiza mwa iye yekha kukhala wa nzeru pakati panu m’dziko lapansili, ameneyo akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru. 19Pakuti nzeru ya dziko lapansili ndi yopusa ndi Mulungu12; pakuti kwalembedwa, Iye anakola anzeru m’kuchenjera kwao. 20Ndiponso, Ambuye amadziwa maganizidwe a wanzeru kuti ndi opanda pake. 21Chomwecho munthu asadzitamandire mwa anthu; pakuti zinthu zonse ndi zanu. 22Kaya Paulo, kapena Apolo, kapena Kefa, kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena zinthu za nthawi yino, kapena zinthu zili nkudza, zonsezi ndi zanu; 23ndipo ndinu wa Khristu, ndipo Khristu ndiye wa Mulungu13.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu13Elohimu