Mutu 1

1Yakobo, kapolo wa Mulungu1 ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri amene ali m’chibalaliko, ndikulonjerani. 2Muchiyese chimwemwe chonse, abale anga, pamene mukugwa m’mayesero osiyanasiyana, 3podziwa kuti kutsimikizira kwa chikhulupiliro chanu kuchita chipiliro. 4Koma chipiliro chanu chikhale ndi ntchito yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi okwanira, osasowa kanthu. 5Koma ngati wina wa inu imsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu2, amene amapereka kwa onse kwaulere ndi kosatonza, ndipo kudzapatsidwa kwa iye: 6koma apemphe m’chikhulupiliro, osakayika konse. Pakuti iye amene akayika ali ngati funde la mnyanja lokankhidwa ndi mphepo ndi kugwedezeka kwambiri; 7pakuti asayese munthu kuti adzalandira kalikonse kwa Ambuye; 8[iye ali] munthu wolingalira pawiri, osakhazikika mnjira zake zonse.

9Koma m’bale wotsika azitamandire m’kukwezedwa kwake, 10ndipo wolemera m’manyazi ake, chifukwa monga duwa la udzu adzapita. Pakuti dzuwa latuluka ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu, ndipo duwa lake lagwa, ndipo maonekedwe akukongola kwake awonongeka: koteronso wachuma adzafota mkupita kwake. 12Wodala munthu amene apilira mayesero; pakuti, pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Iye analonjeza kwa iwo amene amkonda iye.

13Munthu poyesedwa, asanene, Ndikuyesedwa ndi Mulungu3. Pakuti Mulungu4 sangayesedwe ndi zinthu zoipa, ndipo iye mwini samayesa munthu. 14Koma aliyense amayesedwa, pokopeka, ndi kunyengeka ndi chilakolako chake chomwe; 15pamenepo chilakolako, chitayima, chimabereka tchimo; koma tchimo litamaliza kwathunthu limabweretsa imfa.

16Musapusitsidwe, abale anga okondedwa. 17Mphatso iliyonse yabwino ndi mphatso yonse yangwiro itsika kuchokera kumwamba, kuchokera kwa Atate wa kuunika, amene alibe kusiyana kapena mthunzi wa chitembenukiro. 18Kolingana ndi chifuniro chake anatibala ife ndi mau a choonadi, kuti tikhale chipatso choyamba cha zolengedwe zake.

19Kotero kuti, abale anga okondedwa, munthu aliyense akhale wakumva msanga, wochedwa kukwiya; 20pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu5. 21Mwa ichi, potaya zonyansa zonse ndi kuchuluka kwa zoipa, vomerezani ndi kufatsa mau owokedwawo, amene ali othekera kupulumutsa miyoyo yanu. 22Koma inu khalani akuchita mau ndipo osati akumva kokha, kudzinyenga nokha. 23Pakuti ngati munthu aliyense akhala wakumva mau ndi kusawachita, iye afanana ndi munthu wakudziyang’anira nkhope yake m’kalilole: 24pakuti wadziyang’anira yekha nachoka, ndipo nthawi yomweyo ayiwala m’mene amawonekera. 25Koma iye wakupenyerera pa lamulo langwiro, limene lili la ufulu, nakhazikika mu limenelo, posakhala wakumva woyiwala koma wakuchita ntchito, adzadalitsika m’kuchita kwake. 26Ngati wina adziyesa ali wopembedza, wosasamala lilime lake, koma kudzinyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyu nkopanda pake. 27 Kupembedza koyera ndi kosadetsedwa pamaso pa Mulungu6 ndi Atate ndi uku: kuyendera ana amasiye ndi akazi amasiye m’mavuto awo, kudzisunga wopanga banga kudziko lapansi.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu