Mutu 24
1Ndipo atapita masiku asanu anatsika mkulu wa ansembe Hananiya, pamodzi ndi akulu, ndi munthu wina wodziwa kulankhula dzina lake Tertulo, ndipo anapereka mfundo zawo motsutsana ndi Paulo pamaso pa kazembeyo. 2Ndipo atayitanidwa iye, Tertulo anayamba kumneneza, nati, Popeza tili nawo mtendere waukulu mwa inu, ndipo mlingo wabwino umenewu uperekedwa ku mtundu uno mwa kulingaliratu kwanu, 3ife tilandira nthawi zonse komanso kulikonse mwa chiyamiko chonse, wolemekezeka kwambiri Felike. 4Koma kuti ndisakutayitseni nthawi, ndikupemphani kuti mutimvere ife mwachidule mwa chifundo chanu. 5Pomupeza munthu uyu kukhala mliri, ndi kuutsa mipanduko pakati pa Ayuda padziko lonse lapansi, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene; 6amenenso anayesera kuipsa kachisi; amenenso tinamugwira, [ndipo tikanamuweruza molingana ndi lamulo lathu; 7koma Lusiya, kapitao wamkulu, anabwera, namchotsa iye m’dzanja lathu ndi mphamvu yaikulu, 8Polamulira omtsutsa mlandu kubwera kwa inu;] ameneyo mwa inu nokha, pomufunsa [iye] mafunso, mwadziwa mwatchutchutchu zinthu zonse izi zimene tikum’tsutsa nazo iye. 9Ndipo Ayuda analowaponso kupereka nkhawa zawo motsutsana ndi [Paulo], ponena kuti zinthu izi zinali zoona. 10Koma kazembeyo, pamene anamkodola Paulo kuti alankhule, anayankha, Podziwa kuti kwa zaka zambiri mwakhala woweruza ku mtundu uwu, ine ndiyankha monga mwa zinthu zimene zikukhudza inu mwini. 11Monga inu mudziwa kuti sanathe masiku khumi ndi awiri pamene ine ndinapita kukapembedza ku Yerusalemu, 12ndipo ngakhale mkachisi sanandipeze ine ndi kutsutsana ndi wina aliyense, kapena kuyambitsa phokoso lililonse pa khamu losonkhana pamodzi, kapena m’sunagoge, kapenanso mu mzinda; 13kapenanso sangathe kukometsera zinthu zimene iwo tsopano akunditsutsa. 14Komatu ichi ndikutsimikizirani inu, kuti njira imene iwo akuitcha mpatuko, kotero ine nditumikira Mulungu1 wa makolo anga, kukhulupilira zinthu zonse zimene zinalembedwa m’chilamulo chonse, ndi aneneri; 15pokhala ndi chiyembekezo pa Mulungu2, chimene iwonso okha anachilandira, kuti chiukitso chilipo kwa olungama ndi osalungama omwe. 16Pachifukwa chimenechi inenso [pandekha] ndaphunzira mu zonse kukhala ndi chikumbumtima chopanda kutsutsika pa Mulungu3 ndi anthu. 17Ndipo pakutha pa zaka zambiri ine ndinafika, kubweretsa za chifundo ku mtundu wanga, ndi zopereka. 18Pamenepo iwo anandipeza ine woyeretsedwa m’kachisi, wopanda khamu la anthu kapena phokoso. Koma anali Ayuda ena aku Asiya, 19amene anafuna kubwera pamaso panu ndi kundineneza, ngati iwo ali nako kanthu kakundineneza ine; 20kapena aloleni iwo okha anene cholakwa chimene anachipeza mwa ine pamene ndinayima pabwalo, 21 [kupatula] mau awa amene ndinafuula pakuyimilira pakati pawo: Ine lero ndikuweruzidwa ndi inu pokhudza nkhani ya kuuka kwa akufa. 22Ndipo Felike, podziwa mwachindunji zinthu zokhudza njirayi, anawabwenza iwo, nanena, Pamene Lusiya kapitao wamkulu abwera ndidzaona bwino mlandu wanu; 23analamulira kenturiyo kuti amsunge, ndipo kuti akhale mwa ufulu, ndipo asalole aliyense wa abwenzi ake kuti amtumikire.
24Ndipo atapita masiku angapo, Felike anafika pamodzi ndi mkazi wake Drusila, amene anali Myuda wamkazi, anayitanitsa Paulo ndipo anamumva iye zokhudza chikhulupiliro mwa Khristu. 25Ndipo pamene iye anawafotokozera zokhudza kulungama ndi chiletso, ndi chiweruzo, Felike, anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita kaye pakali pano, ndipo ndikakhala ndi mpata ndikuyitananso; 26poyembekezera kuti nthawi yomweyo Paulo adzampatsa ndalama: pamenepo anamuyitananso pafupipafupi ndi kudya naye pamodzi. 27Koma pamene zaka ziwiri zinatha, Porkiyo Festo analowa m’malo mwa Felike; ndipo Felike, pofuna kukondweretsa Ayuda, anamsiya Paulo ali omangidwa.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu