Mutu 14
1Tsatani chikondi, ndipo funitsitsani mphatso za uzimu, koma maka kuti mukanenere. 2Pakuti iye amene alankhula malilime samalankhula kwa anthu koma kwa Mulungu1: pakuti palibe amene amamva; koma mwa mzimu alankhula zinsinsi. 3Koma iye amene amanenera amalankhula kwa anthu ku kumangilira, ndi kulimbikitsa, ndi kutonthoza. 4Iye amene amalankhula malilime azimangilira yekha; iye amene amanenera amamangilira mpingo. 5Tsopano ine ndifunitsitsa kuti nonse muzilankhula malilime, koma makamaka kuti inu munenere. Koma wamkulu ndi iye amene anenera kuposa amene amalankhula malilime, pokhapokha ngati amasulira, kuti mpingo umangilirike. 6Ndipo tsopano, abale, ngati ndibwera kwa inu ndi malilime, kodi ndidzakupindulani bwanji, pokhapokha ngati ndidzalankhula kwa inu mu vumbulutso, kapena chidziwitso, kapena uneneri, kapena mu chiphunzitso? 7Ngakhale zinthu zopanda moyo, zimapereka mau, kaya ndi chitoliro kapena zeze, ngati sizisiyanitsa malilidwe, kodi kuzadziwika bwanji mtundu wa chitoliro ndi zeze? 8Pakutinso, ngati lipenga lipereka mau osazindikirika, ndani amene azazikonzekeretsa yekha kupita ku nkhondo? 9Chomwechonso inu ndi malilime, pokhapokha ngati mupereka mau osamveka, chizadziwika bwanji chimene mwalankhula? Pakuti inu mudzakhala kuti mukulankhula ndi mphepo. 10Zikhoza kutheka, kuti ilipo mitundu yambiri ya ziyankhulo m’dziko lapansi, ndipo palibe kusiyana mau ake. 11Pamenepo ine ngati sindidziwa mphamvu ya mau, ndidzakhala mlendo kwa iye amene akulankhulayo, ndipo iye amene akulankhulayo adzakhala mlendo kwa ine. 12Momwemonso inu, pakuti mufunitsitsa za uzimu, funitsitsani kuti mukamangilirike pa kumangilira mpingo. 13Pamenepo iye emene alankhula ndi malilime apemphere kuti atanthauzire. 14Pakuti ngati ndilankhula malilime, mzimu wanga upemphera, koma chidziwitso changa nchosapindulitsa. 15Nanga chiyani pamenepo? Ine ndipemphera ndi mzimu, komanso ndipemphera ndi chidziwitso; ndiyimba ndi mzimu, komanso ndiyimba ndi chidziwitso. 16Pakuti ngati iwe udzadalitsa ndi mzimu, nanga iye wopezeka pa malopo m’khristu chabe adzanena bwanji Amen, pakuyamika kwako, pakuti iye sadziwa chimene adzalankhula? 17Pakuti iweyo udziwadi kuyamika bwino, koma winayo sakumangilirika. 18Ine ndiyamika Mulungu2 ndidziwa kuyankhula malilime kuposa inu nonse: 19koma mu mpingo ndimafunitsitsa kulankhula mau asanu ndi chidziwitso changa, chimenenso ndikhoza kulangiza nacho ena, [kusiyana] kulankhula mau ochuluka m’malilime. 20Abale musakhale ana m’malingaliro anu, koma m’choipa khalani makanda; koma m’malingaliro anu khalani anthu akuluakulu. 21Kunalembedwa m’chilamulo, Kudzera mwa anthu a zilankhula zina, ndi milomo ya chilendo, ndidzalankhula ndi anthu awa; ndipo mwina potero adzandimvera Ine, atero Ambuye. 22Choncho malilime ndi chizindikiro, osati kwa iwo okhulupilira, koma kwa osakhulupilira; koma uneneri, osati kwa osakhulupilira koma kwa iwo okhulupilira. 23Pamenepo ngati mpingo onse usonkhana pamodzi pamalo amodzi, ndipo onse alankhula m’malilime, ndipo munthu wamba alowa m’menemo, kapena osakhulupilira, kodi sadzanena kuti mwapenga? 24Koma ngati onse akanenera, ndipo ena osakhulupilira kapena munthu wamba alowa, adzatsutsidwa ndi onsewa, adzaweruzidwa ndi onsewa; 25zinsinsi za mtima wake ziwonekera; ndipo pamenepo, pogwetsa nkhope yake, adzapembedza Mulungu3, nadzalengeza kuti zoonadi Mulungu4 ali pakati panu.
26Pamenepo ndi chiyani abale? Pamene mubwera pamodzi, aliyense ali nayo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nawo malilime, ali nalo vumbulutso, ali nako kumasulira. Chitani zonse pakumangilira. 27Ngati wina alankhula malilime, [akhale] awiri, kapena atatu, ndipo alankhule mosiyana, ndiponso m’modzi atanthauzire; 28koma ngati palibe wotanthauzira, akhale chete mu mpingo, ndipo iye azilankhulire payekha ndi kwa Mulungu5. 29Ndipo aneneri awiri kapena atatu alankhule, ndipo enawo azindikire. 30Koma ngati pali vumbulutso kwa wina wokhala [pemenepo], woyambayo akhale chete. 31Pakuti nonse mukhoza kunenera m’modzi m’modzi, kuti nonse mukaphunzire ndi kulimbikikitsika. 32Ndipo mizimu ya aneneri imamvera ulamuliro wa aneneri. 33Pakuti Mulungu6 si [Mulungu7] wa chisokonezo koma wa mtendere, monga m’mipingo yonse ya oyera mtima.
34Akazi akhale chete mu mpingo, pakuti sikololedwa kwa iwo kulankhula; koma kukhala omvera, monganso lamulo linena. 35Koma iwo ngati afuna kuphunzira kalikonse, akafunse amuna awo kunyumba; pakuti ndi zochititsa manyazi mkazi kulankhula mu mpingo. 36Kodi mau a Mulungu8 anatuluka kwa inu, kapena anafikira kwa inu nokha? 37Ngati wina aziyesa yekha kukhala mneneri kapena wauzimu, alingalire zinthu zimene ndakulemberani inu, kuti limeneli ndi lamulo la Ambuye. 38Ngati wina akhala mbuli, akhale mbuli. 39Kotero kuti abale, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kulankhula malilime. 40Koma zinthu zonse zichitike moyenera ndi mwadongosolo.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu