Mutu 8
1Ndipo kunachitika kuti pambuyo pake Iye anayenda [m’dziko] mzinda ndi mzinda, komanso mudzi ndi mudzi, kulalikira ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu1; ndipo khumi ndi awiriwo [anali] naye pamodzi, 2ndipo akazi ena amene anachiritsidwa ku mizimu yoipa ndi nthenda zawo, Mariya amenenso anatchedwa Magadalene, mwa ameneyu ziwanda zisanu ndi ziwiri zinatulutsidwa, 3ndi Yohana, mkazi wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Susana, ndi ena ambiri, amene anamtumikira Iye ndi chuma chawo.
4Ndipo khamu lalikulu pobwera pamodzi, ndi iwo amene amabwera kwa Iye kuchokera ku mizinda yonse, Iye analankhula fanizo: 5Wofesa anatuluka kukafesa mbeu zake; ndipo pamene amafesa, zina zinagwera panjira, ndipo zinapondedwa, ndipo mbalame zakumwamba zinadya mbewuyo; 6ndipo zina zinagwa pa thanthwe, ndipo pakumera, zinafota chifukwa zinalibe chinyontho; 7ndipo zina zinagwera pakati pa minga, ndipo minga pomera inatsamwitsa mbewuyo; 8ndipo zina zinagwa mu nthaka yabwino, ndipo pomera zinabereka zipatso zana limodzi. Pamene Iye amalankhula zinthu izi anafuula nati, Amene ali ndi makutu akumva, amve. 9Ndipo ophunzira ake anamufunsa Iye [nanena], Kodi fanizo limeneli ndi lotani? 10Ndipo Iye anati, Kwa inu kwapatsidwa kudziwa zinsinsi za ufumu wa Mulungu2, koma kwa ena onse mafanizo, cholinga kuti pakuona asaonetsetse, ndi pakumva iwo asamvetsetse. 11Komatu fanizo ndi ili: Mbewu ndiwo mau a Mulungu3. 12Komatu iwo a m’mbali mwanjira ndiwo amene amamva; kenako amabwera mdierekezi nachotsa mau m’mitima mwao kuti asakhulupilire ndi kupulumutsidwa. 13Koma iwo a pa thanthwe, ali iwo amene pamene amva amalandira mau ndi chimwemwe; ndipo amenewa amakhala opanda mizu, amene amangokhulupilira kwa kanthawi, ndipo mu nthawi ya mayesero amagwa. 14Koma iwo amene anagwera pamene panali minga, ali iwo amene atamva mau anapita natsamwitsidwa pansi pa zosamalira ndi chuma ndi zosangalatsa za moyo, ndipo sanabereke zipatso zaphumphu. 15Koma iwo a mu nthaka yabwino, ali iwo mwa mtima woona ndi wabwino, atamva mau anawasunga, ndi kubereka chipatso ndi chipiliro. 16Ndipo palibe wakuyatsa nyali amaivundikira ndi chotengera chake kapena kuika pansi pa kama, komatu amaika pa choikapo nyale kuti iwo olowa awone kuwalako. 17Pakuti palibe kanthu kobisika kamene sikazavumbulutsidwa, kapena chinsinsi chimene sichizadziwika ndi kubwera poyera. 18Yang’anirani pamenepo momwe mumamvera; pakuti kwa iye amene ali nacho, kwa iye chizapatsidwa, ndipo iye amene alibe. Ngakhale chimene ayesa ali nacho chidzachotsedwa kwa iye.
19Ndipo mayi wake ndi abale ake anabwera kwa Iye, ndipo sanathe kufika pafupi ndi Iye chifukwa cha khamulo. 20Ndipo Iye anauzidwa ndi kuti, Mayi wanu ndi abale anu ayima panjapa, akufuna kukuonani. 21Komatu Iye poyankha anati kwa iwo, Mayi wanga ndi abale anga ali iwo amene amamva mau a Mulungu4 ndi kuwachita.
22Ndipo kunachitika kuti tsiku lina, Iye analowa m’ngalawa, Iye mwini pamodzi ndi ophunzira ake; ndipo anati kwa iwo, Tiyeni tiolokere tsidya lina la nyanja; ndipo iwo anayambapo kuchoka ku mtunda. 23Ndipo pamene iwo anakwera m’ngalawa, Iye anagona tulo; ndipo mwadzidzidzi mphepo ya mkuntho inaomba panyanjapo, ndipo iwo anadzala [ndi madzi], nakhala pa chiopsezo; 24ndipo pobwera kwa [Iye] iwo anamudzutsa nanena, Ambuye, Ambuye, tikuonongeka ife. Koma Iye, podzuka, anadzudzula mphepoyo ndi namondwe wa madziyo; ndipo izo zinaleka, ndipo panali bata. 25Ndipo Iye anati kwa iwo, Chikhulupiliro chanu chili kuti? Ndipo, pochita mantha, anali odabwa, nanena kwa wina ndi mzake, Kodi uyu ndi ndani, kuti akulamula ngakhale mphepo ndi madzi, ndipo izi zimvera Iye?
26Ndipo iwo anafika ku dziko la Agerasa, limene linali moyang’anana ndi Galileya. 27Ndipo pamene Iye anatuluka [m’ngalawa] kupita ku mtunda, munthu wina wa mumzindawo anakumana ndi Iye, amene adali ndi ziwanda kwa nthawi yaitali, ndipo samavala zovala, ndipo samakhala m’nyumba, koma amakhala kumanda. 28Koma pomuwona Yesu, iye anafuula, nagwa pamaso pake, ndipo ndi mau okweza anati, Kodi ndichite nanu chiyani inu, Yesu Mwana wa Mulungu5 Wamkulukulu? Ndikupemphani kuti musandizunze ine. 29Pakuti Iye analamula mzimu woipa kutuluka mwa munthuyo. Pakuti kawirikawiri umamugwira iye; ndipo amakhala womangidwa ndi maunyolo ndi matangadza; ndipo pomwetula zomangirazo iye amatsogozedwa ndi ziwanda kulowa m’chipululu. 30Ndipo Yesu anamufunsa iye nanena, Kodi dzina lako ndani? Ndipo iye anati, Legio: pakuti ziwanda zambiri zinalowa mwa iye. 31Ndipo izo zinamupempha Iye kuti asazilamulire kupita kuphompho. 32Ndipo pamenepo panali gulu la nkhumba zambiri zikudya ku mapiri, ndipo izo zinamupempha Iye kuti azilole kulowa mu nkhumbazo; ndipo Iye anazilola. 33Ndipo ziwandazo, potuluka mwa munthuyo, zinalowa mu nkhumba, ndipo gululo linatsika mwa liwiro potsetsereka ndi kulowa m’nyanja, ndipo zinatsamwa. 34Koma iwo amene amadzidyetsa [izo], poona zimene zinachitika, anathawa, nafotokozera [izi] ku mzinda ndi kudziko. 35Ndipo iwo ananyamuka kukaona zimene zinachitikazo, ndipo anabwera kwa Yesu, ndipo anampeza munthu amene anali ndi ziwanda zitatuluka mwa iye, wakukhala pansi, wovala ndi wanzeru zake, ali pa mapazi a Yesu. Ndipo iwo anali ndi mantha. 36Ndipo iwo amene anaona izi anawafotokozera momwe munthu wa ziwandayo anachiritsidwira. 37Ndipo anthu onse ochuluka ozungulira dziko la Agerasa anamupempha Iye kuti achoke kwa iwo, pakuti iwo anazadzidwa ndi mantha akulu; ndipo Iye, polowa m’ngalawa, anabwerera. 38Koma munthu amene anatulutsidwa ziwanda anapita ndi kumupempha kuti akhale naye. Koma Iye anamuuza apite, nanena, 39Bwerera kunyumba kwako ndi kufotokozera zazikulu zimene Mulungu6 wakuchitira. Ndipo iye anapita mu mzinda monse, nalengeza zinthu zazikulu zimene Yesu anamuchitira iye.
40Ndipo kunachitika kuti pamene Yesu anabwerera, khamu linamulandira mwa msangala, pakuti onse amayembekezera Iye. 41Ndipo taonani, munthu anafika, amene dzina lake anali Yairo, ndipo anali mkulu wa sunagoge, ndipo pakugwa pa mapazi a Yesu anamupempha Iye kubwera kunyumba kwake, 42chifukwa anali ndi mwana m’modzi yekhayo wa mkazi, amene anali ndi zaka khumi ndi ziwiri, ndipo anali nkufa. Ndipo pamene Iye amapita makamu a anthu anamkanikiza. 43Ndipo mkazi amene anali ndi nthenda ya kukha mwazi kwa zaka khumi ndi ziwiri, amene, anawononga zonse anali nazo kwa asing’anga, sanathe kuchiritsidwa ndi m’modzi wa iwo, 44pobwera kumbuyo, anakhudza mphonje ya chovala chake, ndipo pomwepo nthenda yake ya kukha mwazi inaleka. 45Ndipo Yesu anati, Ndani wandikhudza Ine? Komatu onse anakana, Petro ndi onse amene anali naye anati, Ambuye, makamu akuwandikirani ndipo akukukanikizani inu, ndipo inu mukuti, Ndani wandikhudza Ine? 46Ndipo Yesu anati, Wina wake wandikhudza Ine, pakuti ndazindikira kuti mphamvu yatuluka mwa Ine. 47Ndipo mkaziyo, powona kuti iye sanabisale, anabwera akunjenjemera, ndipo pakugwa pa mapazi ake analengeza kwa anthu onse cholinga chimene anamukhudzira Iye, komanso momwe anachiritsidwira nthawi yomweyo. 48Ndipo Yesu anati kwa iye, [Limba mtima,] mwana wanga; chikhulupiliro chako chakuchiritsa iwe; pita mu mtendere. 49Ali chilankhulire, anabwera munthu wina kuchokera kwa mkulu wa sunagoge, nanena kwa iye, Mwana wanu wamwalira; musamvutitse Mphunzitsi. 50Koma Yesu, pakumva ichi, anamuyankha iye nati, Usaope: ingokhulupilira kokha, ndipo iye adzachiritsidwa. 51Ndipo pamene anabwera kunyumba sanalola munthu wina aliyense alowe koma Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi bambo ake a mwana komanso mayi wake. 52Ndipo anthu onse anali kubuma ndi kumlira iye. Koma Iye anati, Musalire, pakuti iyeyu sanamwalire, koma akugona. 53Ndipo iwo anamnyodola Iye, podziwa kuti mtsikanayo anali atamwalira. 54Koma Iye, atatulutsa anthu onse panja nagwira dzanja la mtsikanayo, anafuula nati, Mwana iwe, tadzuka. 55Ndipo mzimu wake unabwerera, ndipo nthawi yomweyo anadzuka; ndipo Iye analamulira [kena kake] kakudya kaperekedwe kwa iye. 56Ndipo makolo ake anali ozizwa; koma Iye anawalamulira iwo kusauza munthu aliyense pa zimene zinachitikazo.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu