Mutu 5
1Musamdzudzule munthu wamkulu momchititsa manyazi, komatu mdandaulireni iye monga tate, anyamata monga abale, 2achikulire akazi monga amayi, atsikana monga alongo, ndi chiyero chonse. 3Lemekeza amasiye amene alidi amasiye; 4koma ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, koyamba aphunzire kulemekeza monganso a mnyumba mwao, ndi kubwezera kumbali yawo akuwabala; pakuti chimenechi ndi chovomerezeka pamaso pa Mulungu1. 5Tsopano iye amene alidi wamasiye, ndipo wasiyidwa yekha, ayike chiyembekezo chake mwa Mulungu2, ndi kupitiriza m’mapembedzero komanso m’mapemphero usiku ndi usana. 6koma iye amene akhala m’makhalidwe a zilakolako zake ndi wakufa adakali wamoyo. 7Ndipo zinthu izi ulangize, kuti akakhale opanda banga. 8Koma ngati wina alephera kuzisamalira yekha, ndipo makamaka kusamalira nyumba yake, ameneyu wakana chikhulupiriro, ndipo ndi munthu woipa kuposa wosakhulupirira. 9Wamasiye asawerengedwe, akakhala kuti sanafike zaka makumi asanu ndi limodzi, amene anakhalako mkazi wa mwamuna m’modzi, 10wonyamula umboni wa ntchito zabwino, ngati walera ana, ngati wacherezako alendo, ngati anasambitsako mapazi a atumwi, ngati anabweretsako mpumulo kwa osautsika, ngati mokhulupirika anatsatira ntchito yabwino. 11Koma amasiye achichepere uwakane; pakuti pamene achitira chipongwe Khristu, amakhumba kukwatiwa, 12potsutsika, chifukwa anataya chikhulupiriro chawo choyamba. 13Ndipo, nthawi yomweyo, iwo amaphunziranso kumangokhala, kupita kunyumba za anthu; ndipo osati kumangokhala kokha, komanso kukhala amiseche ndi olowerera za ena, olankhula zinthu zosayenera. 14Ndikufunitsitsa ine kuti achichepere akwatiwe, abereke ana, alamulire nyumba, osapereka mpata kwa mdani poIemekeza cha manyazi. 15Pakuti ena atembenukira kale kwa Satana. 16Ngati mwamuna kapena mkazi aliyense wokhulupirira ali nawo a amasiye, aloleni ayikize chitonthozo kwa iwo, ndipo musalole kuti mpingo ulemetsedwe, kuti ukayike chitonthozo kwa iwo amene ali amasiyedi.
17Akulu amene akutsogolera bwino [pakati pa oyera mtima] alemekezedwe mowirikiza ndi kuthandizidwa, makamaka iwo amene akuchititsa m’mau ndi chiphunzitso; 18pakuti malembo anena, Usapunamiza ng’ombe yopuntha tirigu, ndipo, Wogwira ntchito ayenera kulipira kwake. 19Pa mkulu usalandire chomnenera pokhapokha pamene pali mboni ziwiri kapena zitatu. 20Iwo amene achimwa uwadzudzule pamaso pa onse, kuti enawonso akhale ndi mantha. 21Ndichitira umboni pamaso pa Mulungu3 ndi Khristu Yesu ndi angelo osankhika, kuti usunge zinthu izi popanda kukhala ndi mbali, kupanga chinthu mokondera.
22Usafulumire kuyika manja pa munthu wina aliyense, kapena kutenga nawo gawo pa machimo. Zisunge wekha kukhala woyera. 23Usangomwa madzi okha, koma gwiritsa ntchito vinyo pang’ono chifukwa cha m’mimba mwako ndi kudwaladwala kwako. 24Za anthu ena machimo awonekera kale, kupita motsogola ku chiweruzo, ndipo ena amatsatira pambuyo. 25 Chimodzimodzinso ntchito zabwino zinaonekera kale, ndipo zimene sizinaonekere sizingabisike.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu