Mutu 18

1Zitapita zinthu izi ndinaona mngelo wina akutsika kuchoka kumwamba, wokhala nawo ulamuliro: ndipo dziko lapansi linawalitsidwa ndi ulemelero wake. 2Ndipo anafuula ndi mau akulu, nanena, Babulo wamkulu wagwa, wagwa, ndipo wasanduka mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yoipa, ndi mosungiramo chidetso chonse ndi mbalame zodedwa; 3chifukwa mafuko onse aledzera ndi vinyo wa ukali wa chigololo chake; ndipo mafumu adziko lapansi achita chigololo ndi iye, ndipo ochita malonda adziko lapansi azilemeretsa kudzera mu mphamvu ya m’moyo wake wapamwamba.

4Ndipo ndinamva mau ena kuchoka kumwamba nanena, Tulukani mwa iye, anthu anga, kuti musachite naye chiyanjano m’machimo ake, ndi kuti musalandire nawo milili yake: 5pakuti machimo ake aunjikana pa lina ndi limzake kufikira kumwamba, ndipo Mulungu1 wakumbukira kusalungama kwake. 6Mum’bwezere iye monganso iye wabwezera; ndi kuwirikiza kawiri [kwa iye] kuwirikiza kawiri, molingana ndi ntchito zake. Mu chikho chimene iye wasakanizamo, sakanizani kwa iye kuwirikiza kawiri. 7Monga momwe wadzipatsa yekha ulemelero nakhala moyo wapamwamba, chizunzo chachikulu ndi chisoni ziperekedwe kwa iye. Chifukwa amanena mu mtima mwake, Ndikhala ine mfumukazi, ndipo siine wamasiye; ndipo sindidzaona konse chisoni: 8pachifukwa chimenechi tsiku lina milili yake idzafika, imfa ndi chisoni ndi chilala, ndipo iye adzatenthedwa ndi moto; pakuti ali wamphamvu Ambuye Mulungu2 amene wam’weruza iye. 9Ndi mafumu adziko lapansi, amene anachita naye chigololo, ndi kukhala naye moyo wapamwamba, adzamlilira ndi kum’bumira iye, pamene adzaona utsi wa kupsa kwake, 10atayima patali, mwa mantha a kuzunzika kwake, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukulu, Babulo, mzinda wolimba! Pakuti mwa ola imodzi chiweruzo chafika. 11Ndipo ochita malonda apadziko lapansi adzamlilira ndi kum’bumira iye, chifukwa palibenso amene adzagula malonda awo; 12malonda a golide, ndi a siliva, ndi a miyala ya mtengo wapatali, ndi a ngale, ndi a nsalu yabwino yopyapyala, ndi a chibakuwa, ndi a zonyezimira, ndi a mlangali, ndi a mitengo yonse yonunkhira, ndi zinthu zonse za m’nyanga ya njovu, ndi zinthu zonse za mtengo wamtengo wapatali, ndi mu chamkuwa, ndi mu chachitsulo, ndi mu chansangalabwi, 13ndi kinamomo, ndi amomo, ndi zofukiza, ndi zodzoladzola, ndi zonunkhira, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wopera bwino, ndi tirigu ndi ng’ombe, ndi nkhosa, ndi za akavalo, ndi za magareta, ndi za matupi, ndi miyoyo ya anthu. 14Ndi zipatso zakupsa zimene zili zilakolako za moyo wao zinachoka pamaso pako, ndi zinthu zonse zabwino ndi zokongola zaonongeka pamaso pa iwe, ndipo iwo sadzazipezanso konse. 15Ochita malonda a zinthu zimenezi, amene anadzilemeretsa kudzera mwa iye, adzayima patali mwa mantha a kudzunzidwa kwake, kulira ndi kubuma, 16nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukulu, umene unavekedwa ndi nsalu yabwino yoyera, ndi bafuta ndi chibakuwa, ndipo anali nazo zonunkhira za golide ndi miyala ya mtengo wapatali ndi ngale! 17pakuti mu ola imodzi chuma chambiri chonchi chasanduka bwinja. Ndipo watsigiro aliyense, ndi woyendetsa chombo aliyense kupita kulikonse, ndi oyenda panyanja, ndi onse amene achita maitanidwe awo panyanja, anaima patali, 18ndipo analira, poona utsi wakupsa kwake, nanena, ndi [mzinda] uti ufanana ndi mzinda waukulu? 19ndipo anathira fumbi pamitu pawo, nafuula, nalira ndi kubuma, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukulu, m’mene onse amene anali ndi zombo m’nyanja analemeretsedwa kudzera mwa kulemera kwake! Pakuti mu ola limodzi iye anasandulika bwinja.

20Kondwera pa iye, m’mwamba, ndi oyera [inu] nonse ndi atumwi ndi aneneri; pakuti Mulungu3 waweruza chiweruzo chako pa iye.

21Ndipo mngelo wolimba watenga mwala, wonga mphero yayikulu, ndi kuuponyera m’nyanja, nanena, Chomwecho ndi Babulo mzinda waukulu waponyedwa pansi, ndipo sudzapezekanso konse; 22ndipo mau a iwo oyimba azeze ndi a oyimba ndi oyimba zitoliro ndi malipenga sadzamvekanso konse mwa iwe, ndipo palibe m’misiri wa luso lililonse adzapezeke konse mwa iwe, ndi mau a mphero sadzamvekanso konse mwa iwe, 23ndipo kuwala kwa nyale sikudzawalanso konse mwa iwe; pakuti amalonda ako anali otchuka padziko lapansi; pakuti matsenga ako mitundu yonse yanyengeka nawo. 24 Ndipo mwa iye munapezeka mwazi wa aneneri ndi wa oyera mtima, ndi onse ophedwa padziko lonse lapansi.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu