Mutu 2
1Ndipo pamene tsiku la Pentekoste linafika, iwo anali onse pamodzi malo amodzi. 2Ndipo pamenepo mwadzidzidzi panafika mau ochokera kumwamba monga mphepo yoomba mwa mphamvu, ndipo inadzadza nyumba yonse imene iwo anakhalamo. 3Ndipo pamenepo panaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, monga a moto, ndipo unakhala pa iwo aliyense payekha payekha. 4Ndipo iwo onse anadzadzidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo anayamba kulankhula ndi malilime ena monga Mzimu anaperekera kwa iwo kulankhula.
5Tsopano kumeneko anakhalako Ayuda ku Yerusalemu, amuna opembedza, kuchokera ku mtundu uliwonse wa pansi pa thambo. 6Komatu mphekesera ya izi itawanda, khamulo linabwera pamodzi ndipo linasokonezedwa, chifukwa aliyense anawamva akulankhula m’chilankhulo chake. 7Ndipo iwo onse anali odzidzimuka ndi odabwa, nanena, Taonani, kodi onse amene akulankhulawa si Agalileya? 8ndipo zitheka bwanji ife tikuwamva [iwo] aliyense m’chilankhulo chathu monga mwa chilankhulo chathu chimene tinabadwa nacho, 9Aparti, ndi Amedi, ndi Aelami, ndi iwo akukhala m’Mesopotamiya, ndi m’Yudeya, ndi m’Kapadokiya, m’Ponto ndi Asiya, 10m’Frugiya ndi Pamfuliya, m’Aigupto, ndi mbali za Libiya zimene zimalumikizitsa Kurene, ndi alendo ochokera ku Roma, Ayuda ndiponso opinduka, 11Akrete ndi a Arabu, tiwamva iwo akulankhula m’chilankhulo chathu zinthu zazikulu za Mulungu? 1 12Ndipo iwo onse anali odabwa ndipo pothedwa nzeru, anati kwa wina ndi mzake, Kodi zimenezi zitanthauza chiyani? 13Koma ena mwachipongwe anati, Awa akhuta vinyo wa lero.
14Koma Petro, poyimilira pamodzi ndi khumi ndi m’modziwo, anakweza mau ake ndipo analankhula kwa iwo, Amuna aku Yudeya, ndi inu nonse okhala mu Yerusalemu, izi zidziwike kwa inu, ndipo imvani mau anga: 15pakuti awa sanakhute vinyo, monga inu mukuganizira, pakuti lidakali ola lachitatu la tsiku; 16koma izi ndi zomwe zinalankhulidwa mwa mneneri Yoweli, 17Ndipo kudzatero m’masiku otsiriza, atero Mulungu2, [kuti] ndidzatsanulira cha Mzimu wanga pathupi lililonse; ndipo ana anu amuna ndi ana anu akazi adzanenera, ndipo achinyamata anu adzaona masomphenya, ndipo akuluakulu anu adzalota maloto; 18zoonadi, ngakhale pa akapolo amuna ndi akapolo akazi m’masiku amenewo ndidzatsanulira cha Mzimu wanga, ndipo iwo adzanenera. 19Ndipo Ine ndidzapereka zodabwitsa m’mwamba ndi zizindikiro padziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi mthunzi wa utsi: 20Dzuwa lidzasinthidwa kukhala mdima ndi mwezi kukhala magazi, lisanafike tsiku lalikulu la Ambuye. 21Ndipo kudzatero kuti aliyense wakuyitanira pa Ambuye adzapulumuka. 22Amuna inu a Israyeli, imvani mau awa: Yesu Mnazarayo, munthu wochitiridwa umboni mwa Mulungu2 kwa inu mwa ntchito za mphamvu ndi zodabwitsa ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye, mwa dzanja la [anthu] ochimwa, anampachika Iye ndi kumupha. 223— ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woyikika ndi kudziwiratu kwa Mulungu4, inuyo, mwa dzanja la [anthu] osaweruzika, munampachika ndi kumupha. 224Amene Mulungu5 anamuukitsa, atamasula ululu wa imfa, ngakhale kuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe ndi mphamvu yake; 25pakuti Davide anati za Iye, Ndinaona Ambuye pamaso panga nthawi zonse, chifukwa Iye ali kudzanja langa lamanja kuti ndisasunthike. 26Pamenepo mtima wanga ukondwera ndi lilime langa lisangalala; kuonjezera apo, thupi langanso lidzakhala m’chiyembekezo, 27pakuti simudzasiya moyo wanga mu hade, kapena kupereka wachisomo wanu ku chionongeko. 28Mwandidziwitsa ine njira za moyo, mwandidzadza ine ndi chimwemwe komanso chilimbikitso chanu. 29Abale inu, tiyeni kuloledwe kulankhula ndi ufulu kwa inu zokhudza kholo Davide, kuti anamwalira ndi kuikidwa m’manda, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero. 30Pamenepo pokhala mneneri, ndi kudziwa kuti Mulungu6 anapangana kwa iye ndi lumbiro, la chipatso cha mchiuno mwake kukhala pa mpando wake wa chifumu; 31iye, poona [ichi] kale, analankhula zokhudza kuuka kwa Khristu, kuti sanaponyedwe m’hade kapena thupi lake kuona chivundi. 32Yesu ameneyu Mulungu7 anamuukitsa, pamenepo tonsefe ndife mboni. 33Pamenepo atakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu8, ndipo atalandira mwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, Iye anasanulira ichi chimene inu muchiona ndi kuchimva. 34Pakuti Davide sanakwere kupita kumwamba, koma iye mwini anati, Ambuye anati kwa Mbuye wanga, Khala kudzanja langa lamanja 35kufikira ndikaike adani ako [kukhala] chopondapo mapazi ako. 36Pamenepo nyumba yonse ya Israyeli ikadziwedi kuti Mulungu9 wampanga Iye, Yesuyu amene inu munampachika, kukhala Ambuye ndi Khristu.
37Ndipo pakumva [ichi] analaswa mu mtima, ndipo anati kwa Petro ndi ophunzira ena aja, Tichite chiyani ife, abale inu? 38Ndipo Petro anati kwa iwo, Lapani, ndi kubatizidwa, aliyense wa inu, m’dzina la Yesu Khristu, pa kukhululukidwa kwa machimo, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. 39Pakuti kwa inu kuli lonjezano ndi kwa ana inu, ndi kwa ena onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu10 wathu angawaitane. 40Ndipo ndi mau ochuluka iye anachitira umboni nawadandaulira iwo, nanena, Pulumutsidwani ku m’badwo uwu wokhotakhota. 41Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaphatikizidwa m’tsiku limenelo miyoyo pafupifupi zikwi zitatu.
42Ndipo iwo anakhalabe m’chiphunzitso ndi m’chiyanjano cha atumwi, m’kunyema mkate ndi mapemphero. 43Ndipo mantha anagwira moyo uliwonse, ndipo zodabwitsa ndi zizindikiro zambiri zinachitika mwa atumwi. 44Ndipo onse amene anakhulupilira anali pamodzi, ndipo anakhala nazo zonse zofanana, 45ndipo anagulitsa katundu wawo ndi zina, ndipo anazigawa izo kwa iwo onse, molingana ndi kusowa kwa aliyense. 46Ndipo tsiku lililonse, pakukhala pamodzi m’kachisi ndi cholinga chimodzi, ndi kunyema mkate m’myumba, iwo analandira chakudya chawo ndi chisangalalo ndi mtima wodzichepetsa, 47kutamanda Mulungu11, ndi kukhala nako kukonderedwa ndi anthu onse; ndipo Ambuye anaonjezera [ku mpingo] tsiku ndi tsiku iwo amene amapulumutsidwa.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12