Mutu 2
1Ndipo patsiku lachitatu panali ukwati mu Kana wa Galileya, ndipo mayi wake wa Yesu anali komweko. 2Ndiponso Yesu, ndi ophunzira ake, anaitanidwa ku ukwatiko. 3Ndipo atatha vinyo, mayi wake wa Yesu anati kwa Iye, Alibe vinyo. 4Yesu anati kwa iye, Ndili ndi chiyani ndi inu, mkazi? Ola langa silinafike. 5Mayi wake anati kwa otumikira, Chilichonse chimene atanene ndi inu, chitani. 6Tsopano panayimilira pamenepo mitsuko ya miyala isanu ndi umodzi, molingana ndi mayeretsedwe a Ayuda, yokhala ndi milingo iwiri kapena itatu mtsuko uliwonse. 7Yesu anati kwa iwo, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Ndipo anadzaza mitsukoyo mpaka pamwamba. 8Ndipo Iye anati kwa iwo, Tungani tsopano, ndipo kaperekeni kwa mkulu wa phwando. Ndipo iwo anatunga madziwo. 9Koma pamene mkulu wa phwando analawa madziwo amene anapangidwa kukhala vinyo (ndipo sanadziwe kumene anachokera, komatu atumiki amene anatunga madziwo), mkulu wa phwando anayitanitsa mkwati, 10ndipo anati kwa iye, Munthu aliyense amayika koyamba vinyo wokoma, ndipo pamene anthu amwa bwino, pamenepo amabweretsa wosakoma; iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano. 11Chiyambi cha zizindikiro Yesu anachita mu Kana wa Galileya, ndipo anaonetsera ulemelero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupilira pa Iye.
12Zitapita izi anatsikira ku Karpenao, Iye ndi mayi wake ndi abale ake ndi ophunzira ake; ndipo kumeneko iwo anakhalako masiku ochepa.
13Ndipo paskha wa Ayuda anali pafupi, ndipo Yesu anakwera kupita ku Yerusalemu. 14Ndipo Iye anapeza mkachisi ogulitsa ng’ombe ndi nkhosa ndi nkhunda, ndi osintha ndalama atakhala pansi; 15ndipo, anakonza chikwapu cha zingwe, nawatulutsira [iwo] kunja kwa kachisi, nkhosa ndi ng’ombe zomwe; ndipo Iye anakhuthula ndalama za osintha ndalamawo, nagubuduza magome, 16ndipo anati kwa ogulitsa nkhunda, Chotsani izi; musasandutse nyumba ya Atate wanga kukhala nyumba ya malonda. 17[Ndipo] ophunzira ake anakumbukira zimene zinalembedwa, Changu cha panyumba panu chandidya ine. 18Ayuda pamenepo anayankha nati kwa Iye, Kodi mutionetsa chizindikiro chanji, kuti mukuchita zinthu izi? 19Yesu anayankha nati kwa iwo, Pasulani kachisi uyu, ndipo m’masiku atatu ndizamudzutsanso. 20Ayuda pamenepo anati, kwa zaka makumi anayi ndi zisanu ndi chimodzi kachisi uyu anamangidwa, ndipo ukuti udzamudzutsa m’masiku atatu? 21Koma Iye amalankhula za kachisi wa thupi lake. 22Pamene Iye anaukitsidwa pakati pa akufa, ophunzira ake anakumbukira kuti Iye analankhula zimenezi, ndipo anakhulupilira malemba ndi mau amene Yesu analankhula.
23Ndipo pamene Iye anali m’Yerusalemu, ku paskha, pa phwando, ambiri anakhulupilira padzina lake, pakuona zizindikiro zake zimene Iye anazichita. 24Koma Yesu mwini sanawakhulupilire iwo kuti akhale nawo, pakuti Iye anawadziwa [anthu] onse, 25ndipo kuti sanafune kuti aliyense achitire umboni za munthu, pakuti Iye mwini amadziwa zimene zinali mwa munthu.