Mutu 7

1Ndipo zitatha izi Yesu anayenda m’Galileya, pakuti Iye sakanayenda m’Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye. 2Tsopano misasa, phwando la Ayuda linali pafupi. 3Pamenepo abale ake anati kwa Iye, Chokani kuno ndipo mupite m’Yudeya, kuti ophunzira anunso akaone ntchito zimene mukuchita; 4pakuti palibe munthu amene amachita zinthu mwa mseri ndipo iye mwini afuna [kudziwika] mu gulu. Ngati mumachita zinthu izi, zionetsereni nokha kudziko lapansi: 5pakuti ngakhale abale ake sanakhulupilire pa Iye. 6Yesu pamenepo anati kwa iwo, Nthawi yanga sinafike, komatu nthawi yanu inakonzedweratu. 7Dziko lapansi silingakudeni, koma Ine lindida, chifukwa ndimachitira umboni zokhudza ilo kuti ntchito zake zili zoipa. 8Inuyo, pitani ku phwandoko. Ine sindipitako, pakuti nthawi yanga sinakwaniritsidwe. 9Atanena zinthu zimenezi kwa iwo Iye anakhalabe m’Galileya.

10Koma pamene abale ake anapita ku phwandoko, pamenepo Iyenso anapitako, osati moonekera, koma mwachinsinsi. 11Pamenepo Ayuda anamufunafuna ku phwandoko, ndipo anati, Kodi Iyeyu ali kuti? 12Ndipo panali kung’ung’uza kwakukulu m’khamulo zokhudza Iye. Ena anati, Iye ndi [munthu] wabwino; enanso anati, Ayi; koma amasocheretsa khamu. 13Komabe. Palibe amalankhula poyera zokhudza Iye pakuopa Ayuda.

14Koma pamene panali pakati pa phwando, Yesu anapita m’kachisi naphunzitsa. 15Pamenepo Ayuda anadabwa, nanena, [Munthu] uyu adziwa bwanji malemba, wokhala kuti sanaphunzireko? 16Pamenepo Yesu anayankha ndi kuti, Chiphunzitso changa sichanga ayi, koma cha Iye amene anandituma Ine. 17Ngati wina afunitsitsa kuchita chifuniro chake, azadziwa zokhudza chiphunzitsochi, ngati chili cha Mulungu1, kapena [kuti] ndilankhula za Ine ndekha. 18Iye amene alankhula za iye yekha afuna ulemelero wa iye yekha; koma iye wofuna ulemelero wa Iye amene anamtuma, ali woona, ndipo chisalungamo sichili mwa iye. 19Kodi Mose sanakupatseni lamulo, ndipo palibe wa inu amatsata lamulolo? Chifukwa chiyani mufuna kundipha? 20Khamulo linayankha, [ndipo linati], Muli ndi chiwanda: ndani amene afuna kukuphani? 21Yesu anayankha nati kwa iwo, Ndachita ntchito imodzi, ndipo nonse mukudabwa. 22Pamenepo Mose anakupatsani mdulidwe (osati kuti mdulidwewo ndi wa Mose, koma wa makolo anu), ndipo inu mumadula munthu tsiku la sabata. 23Ngati munthu amalandira mdulidwe tsiku la sabata, kuti lamulo la Mose lisaphwanyidwe, kodi muli okwiya nane chifukwa ndachiritsa kwathunthu munthu pa sabata? 24Musamaweruze molingana ndi maonekedwe, koma weruzani ndi chiweruzo cholungama. 25Pamenepo ena aku Yerusalemu anati, Kodi uyu si uja akufuna kumuphayu? 26ndipo taonani, Iye amalankhula poyera ndipo sanalankhule kanthu kwa Iye. Kodi aulamuliro amzindikira kuti uyu ndi Khristu? 27Koma zokhudza munthu uyu ife tidziwa kumene akuchokera. Tsopano zokhudza Khristu, pamene adzabwera, palibe amene adzadziwa kumene akuchokera. 28Pamenepo Yesu anafuula m’kachisi, naphunzitsa ndipo anati, Inu nonse mundidziwa Ine ndi kumene ndichokera; ndipo Ine sindinabwere mwa Ine ndekha, koma Iye amene anandituma Ine ali woonadi, amene inu simumudziwa. 29Ine ndimdziwa Iye, chifukwa ndili wochokera kwa Iye, ndipo Iye wandituma Ine. 30Pamenepo iwo anafuna kumgwira Iye; ndipo palibe amene anayika dzanja lake pa Iye, chifukwa ola lake linali lisanafike. 31Koma ambiri mwa khamulo anakhulupilira pa Iye, ndipo anati, Kodi Khristu akadzabwera, adzachita zizindikiro zoposa izi zimene [munthu] uyu wachita? 32Afarisi anamva khamulo likung’ung’uza zinthu zimenezi zokhudza Iye, ndipo Afarisi ndi ansembe akulu anatuma asilikali kuti akamugwire Iye. 33Pamenepo Yesu anati, Kanthawi kochepa ndili ndi inu, ndipo Ine ndidzapita kwa Iye amene anandituma. 34Mudzandifunafuna koma simudzandipeza, ndipo kumene ndili simungathe kufikako. 35Pamenepo Ayuda analankhula kwa wina ndi mzake, Kodi akupita kuti kumene ife sitingathe kumupeza? Kodi akufuna kupita pakati pa Ahelene obalalikawo, ndi kuwaphunzitsa iwo? 36Kodi mau awa wanenawa ndi otani, Mudzandifunafuna koma simudzandipeza; ndipo kumene ndili simungathe kufikako?

37Tsiku lomaliza, lalikulu la phwando, Yesu anayimilira nafuula ndi kuti, Ngati wina amva ludzu, abwere kwa Ine ndipo adzamwa. 38Iye wokhulupilira pa Ine, monga malemba anena, Kuchoka mkati mwake mudzatuluka mitsinje ya madzi amoyo. 39Koma izi ananena zokhudza Mzimu, amene iwo okhulupilira pa Iye akuyembekedzera kulandira; pakuti Mzimu anali asanabwere, chifukwa Yesu anali asanalemekezedwe. 40Pamenepo [ena] mwa khamulo, pakumva mau amenewa, anati, Uyudi ndi mneneri. 41Ena anati, Uyu ndi Khristu. Enanso anati, Kodi Khristu adzatuluka m’Galileya? 42Kodi malemba sananene kuti Khristu achokera m’mbewu ya Davide, ndi kuchoka m’mudzi wa Beterehemu, kumene kunali Davide? 43Ndipo panali kugawikana pamenepo m’khamulo chifukwa cha Iye. 44Koma ena mwa iwo anafunitsitsa kumgwira, koma palibe anayika dzanja pa Iye. 45Pamenepo asilikali anabwera kwa ansembe akulu ndi Afarisi, ndipo anati kwa iwo, chifukwa chiyani simunamugwire Iye? 46Asilikaliwo anayankha, Palibe munthu analankhula motere, monga munthu uyu [alankhulira]. 47Pemenepo Afarisi anawayankha iwo, Kodi nanunso mwasokeretsedwa? 48Kodi wina wa olamulira anakhulupilira pa Iye, kapenanso Afarisi? 49Koma khamu ili, limene silidziwa lamulo, ndi lotembereredwa. 50Nikodemo anati kwa iwo (pokhala m’modzi wa iwo), 51Kodi lamulo lathu limaweruza munthu lisanamve kaye kwa iye mwini, ndi kudziwa chimene iye achita? 52Iwo anayankha nati kwa iye, Kodi nawenso ndi waku Galileya? Ufufuze ndi kuyang’ana, kuti palibe mneneri anauka ku Galileya.

53Ndipo aliyense anapita kunyumba kwake.

1Elohimu