Mutu 11

1Pamenepo ndinena, Kodi Mulungu1 wataya anthu ake? Musaganize choncho. Pakuti inenso ndine m’Israyeli, wa mbeu ya Abrahamu, wa mtundu wa Benjamini.1 Mulungu2 sanataye anthu ake amene anawadziwiratu. Kodi simukudziwa zimene malemba anena mu [mbiri ya] Eliya, m’mene anachonderera kwa Mulungu3 zokhudza Israyeli?3Ambuye, iwowa anapha aneneri anu, anakumba maguwa anu; ndipo ine ndatsala ndekha, ndipo akusakasaka moyo wanga.4Koma yankho la kumwamba linali lotani kwa iye? Ndazisungira ndekha anthu zikwi zisanu ndi ziwiri, amene sanagwadire kwa Baala.5Pamenepo, mu nthawi inonso alipo otsala molingana ndi kusankhidwa mwa chisomo.6Koma ngati mwa chisomo, osatinso mwa ntchito: pakuti [ngati sikutero] chisomo si chisomonso.7Nanga chiyani pamenepo? Chimene Israyeli anafunafuna, chimene sanachipeze, koma osankhikawo anachipeza, ndipo ena onse anachititsidwa khungu,8molingana ndi m’mene kunalembedwera, Mulungu4 anawapatsa iwo mzimu watulo, kukhala ndi maso koma osaona, ndi makutu koma osamva, kufikira lerolino.9Ndipo Davide anati, gome lawo likhale msampha, ndi ngati diwa, ndi monga chopunthwitsa, ndi chowabwezera chilango kwa iwo:10maso awo adetsedwe kuti asaone, ndi kukhotetsa misana yawo.

11Pamenepo ine ndinena, Kodi anakhumudwa kuti agwe? Musaganize choncho: komatu m’kugwa kwao muli chipulumutso kwa amitundu kuwachititsa iwo nsanje.12Koma ngati kugwa kwao kuli chuma cha dziko lapansi, ndipo kulephera kwao chuma cha amitundu, nanga koposa kotani kudzadza kwao?13Pakuti ine ndilankhula kwa inu, amitundu, monga ine mtumwi wa amitundu, ndimalemekeza utumiki wanga;14ngati mwanjira ina iliyonse ndidzawatsogolera kuchita nsanje [iwo amene ali] a thupi langa, ndi kupulumutsa ena pakati pawo.15Pakuti ngati kuwataya kwao kuli kuyanjanitsidwa kwa dziko lapansi, nanga kulandiridwa kwao kudzatani, koma ngati moyo pakati pa anthu akufa?

16Tsopano ngati chipatso choyamba chikhala choyera, chomwechonso mtanda; ndipo ngati muzu ukhala woyera chomwechonso nthambi zake.17Tsopano ngati nthambi zathyoledwa, ndipo inu, okhala mtengo wa kuthengo wa mafuta, mwalumikizidwa pakati pawo, ndipo mwakhala wotenga gawo wa muzu ndi kunenepa kwa mtengo wa mafuta,18usadzitame wekha pa nthambipo; koma ngati udzitame, si iwe amene unyamula muzu, koma muzu unyamula iwe.19Pamenepo iwe unena, Nthambi zathyoledwa cholinga kuti ndikalumikizidwe mwa iwo.20Chabwino: iwo athyoledwa kudzera mu kusakhulupilira, ndipo mwayimikika mwa chikhulupiliro. Musakhale ozitukumula, koma amantha:21Ngatidi Mulungu5 sanatimane nthambi za chilengedwe; sazakulekanso iwe.

22Taonani pamenepo ubwino ndi ukali wa Mulungu6: pa iwo amene anagwa, ukali; pa iwe ubwino wa Mulungu7, ngati iwe udzakhala mu ubwino, koma ngati sochoncho iwenso udzadulidwa.23Ndipo iwonso, ngati akhala m’kusakhulupilira, adzalumikizidwa; pakuti Mulungu8 ali nako kuthekera kowalumikizanso iwo.24Pakuti ngati inu mwadulidwa ku mtengo wa mthengo wa mafuta mwa chilengedwe, ndipo mosemphana ndi chilengedwe, mwalumikizidwa mu mtengo wabwino wa mafuta, nanga koposa kotani iwo molingana ndi chilengedwe analumikizidwa ku mtengo wawowawo wa mafuta?25Pakuti ine sindifuna kuti mukhale mbuli, abale, za chinsinsi chimenechi, kuti musaziyese nokha a nzeru, kuti khungu linachitika mu gawo lina kwa Israyeli, kufikira uphumphu wa mafuko ukadza;26ndipo pamenepo Israyeli yense akapulumutsidwa. Molingana ndi m’mene kunalembedwera, Mpulumutsi adzatuluka kuchoka mu Ziyoni; Iye adzachotsa choipa kuchoka mwa Yakobo.27Ndipo limeneli ndi pangano langa lochokera kwa ine kupita kwa iwo, pamene ndidzachotsa machimo awo.28Molingana ndi uthenga wabwino, iwo ali adani chifukwa cha inu; koma molingana ndi kusankhidwa, ali okondeka chifukwa cha makolo.29Pakuti mphatso komanso maitanidwe a Mulungu9 sizitengera ku kulapa.30Pakuti mongadi inunso kale simunakhulupilire mwa Mulungu10, koma tsopano mwakhala zida za chifundo kudzera m’kusamvera kwa awa;31tsopano awanso sanakhulupilire mu chifundo chanu, cholinga kuti iwonso akakhale zida za chifundo.32Pakuti Mulungu11 watsekera onse pamodzi m’kusakhulupilira, cholinga kuti akaonetse chifundo kwa onse.33Ha Kuya kwa kulemera mu nzeru ndi chidziwitso cha Mulungu12! Maweruzo ake ndi osasanthulika, ndi njira zake zosalondoleka!34Pakuti ndani amene wadziwa malingaliro a Ambuye, kapena ndani amene anakhalako mlangizi wake?35kapena ndani wapereka kwa Iye koyamba, ndipo chidzabwezeredwa kwa iye?36Pakuti ndi Iye, ndiponso mwa Iye, komanso kwa Iye zinthu zonse zichokera: kwa Iye kukhale ulemelero nthawi zonse. Amen.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu