Mutu 2
1Komatu zinachitika m’masiku amenewo kuti lamulo linakhazikitsidwa kuchokera kwa Kaisara Augusto, kuti kalembera achitike kwa onse okhala m’dzikomo. 2Kalemberayu poyamba anachitika pamene Kureniyo anali kazembe waku Suriya. 3Ndipo onse anapita kukalembetsa mu kaundula, aliyense ku mzinda wake: 4ndipo Yosefe nayenso anapita kuchokera ku Galileya mu mzinda wa Nazarete wa Yudeya, mu mzinda wa Davide, umene umatchedwa Betelehemu, chifukwa iye anali wanyumba ndi banja la Davide, 5kukalembedwa mu kaundula pamodzi ndi Mariya amene anatomeredwa ndi iye [monga] mkazi [wake], wokhala ndi pakati. 6Ndipo kunachitika, pamene anali kumeneko, masiku akubereka [mwana wake] anakwanira, 7ndipo iye anabereka mwana wake woyamba wamwamuna, ndipo anamkulunga iye mu nsalu nam’goneka modyera ng’ombe, pakuti munalibe malo m’nyumba ya alendo.
8Ndipo analiko abusa m’dzikolo akukhala kunja, akuyang’anira ziweto zawo usiku onse. 9Ndipo mngelo wa Ambuye anali nawo pamenepo, ndipo ulemelero wa Ambuye unawala pozungulira iwo, ndipo iwo anachita mantha [ndi] mantha akulu. 10Ndipo mngelo anati kwa iwo, musaope, pakuti taonani, ndilengeza kwa inu uthenga wabwino wa chimwemwe chachikulu, umene udzakhala kwa anthu onse; 11pakuti lero wakubadwirani inu mu mzinda wa Davide, amene ali Khristu Ambuye. 12Ndipo ichi ndi chizindikiro kwa inu: mudzapeza mwana wokulungidwa mu nsalu, atagona modyera ng’ombe. 13Ndipo mwadzidzidzi panali gulu la angelo akumwamba, akutamanda Mulungu1 nanena, 14Ulemelero kwa Mulungu2 m’mwambamwamba, ndi mtendere pansi pano, mwa anthu amene akondwera nawo. 15Ndipo kunachitika kuti, pamene angelo anachoka kwa iwo ndi kupita kumwamba, abusa anati kwa wina ndi mzake, Tiyeni tipitiretu tsopano ku Betelehemu, tikaone chinthu ichi chachitika, chimene Ambuye watidziwitsa ife. 16Ndipo iwo anabwera mwachangu, ndipo anawapeza onse Mariya ndi Yosefe, ndi mwana atagona modyera ng’ombe; 17ndipo pakuona [ichi] anadziwitsa za dziko limene kunachitika chinthuchi chimene chinanenedwa kwa iwo chokhudza mwanayu. 18Ndipo onse amene anamva [ichi] anadabwa pa zinthu zinanenedwa kwa iwo ndi abusa. 19Koma Mariya anasunga zinthu zonse [m’malingaliro mwake], nazisamala [izo] mu mtima mwake. 20Ndipo abusa anabwerera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu3 pa zinthu zonse zimene iwo anazimva ndi kuziona, monga zinanenedwera kwa iwo.
21Ndipo pamene masiku asanu ndi atatu anakwanira kuti adulidwe Iye, dzina lake linatchedwa Yesu, dzina limene linaperekedwa ndi mngelo asanalandiridwe m’mimba.
22Ndipo pamene masiku anakwanira akuyeretsedwa kwao molingana ndi lamulo la Mose, anam’bweretsa Iye ku Yerusalemu kudzampereka [Iye] kwa Ambuye 23(monga kunalembedwa mu lamulo la Ambuye: mwana wa mwamuna aliyense amene adzatsegulira mimba ya amake adzatchedwa woyera kwa Ambuye), 24ndipo pakupereka nsembe molingana ndi zimene zinanenedwa mu lamulo la Ambuye: nkhunda ziwiri, kapena njiwa zing’onozing’ono ziwiri.
25Ndipo taonani, panali munthu ku Yerusalemu amene dzina lake anali Simeoni; ndipo munthu ameneyu anali wolungama mtima ndi wopemphera, amene amadikilira matonthozedwe a Israyeli, ndipo Mzimu Woyera anali pa iye. 26Ndipo anauzidwa mwa umulungu ndi Mzimu woyera, kuti sadzaona imfa kufikira ataona Khristu wa Ambuye. 27Ndipo iye anabwera mu Mzimu m’kachisi; ndipo pamene makolo anabweretsa mwanayo Yesu kuti iwo achite naye monga mwa chikhalidwe cha lamulo, 28iye anamlandira m’manja mwake, nayamika Mulungu4, nanena, 29Ambuye, tsopano lolani kapolo wanu apite mu mtendere, molingana ndi mau anu; 30pakuti maso anga awona chipulumutso chanu, 31chimene inu mwandikonzera pamaso pa anthu onse; 32kuunika kwa vumbulutso la amitundu ndi ulemelero wa anthu a Israyeli. 33Ndipo atate wake ndi amake anadabwa ndi zinthu zonenedwazo zokhudza Iye. 34Ndipo Simeoni anawadalitsa iwo, ndipo anati kwa Mariya amake, Taona, [Mwana] uyu waikidwa akhale kugwa ndi kuuka kwa ambiri mu Israyeli, ndi chizindikiro cholankhula mowatsutsa; 35(ndipo ngakhale lupanga lidzapyoza moyo wako;) kotero kuti malingaliro akavumbulutsidwe kuchoka m’mitima yambiri.
36Ndipo kunali mneneri wamkazi, dzina lake Anna, mwana wamkazi wa Fanueli, wa fuko la Aseri, amene anali wokalamba zedi, nakhala ndi mwamuna wake zaka zisanu ndi ziwiri kuyambira pa unamwali wake, 37ndipo iye mwini anakhala wamasiye kufikira zaka makumi asanu ndi atatu kudza mphambu zinayi; amene sanachokeko ku kachisi, kutumikira usiku ndi usana ndi kusala kudya ndi mapemphero; 38ndipo iye pakufika ola lomwelo analemekeza Ambuye, ndipo analankhula za Iye kwa iwo onse amene amadikira chiombolo cha Yerusalemu.
39Ndipo pamene iwo anatsiriza zonse molingana ndi lamulo la Ambuye, anabwerera ku Galileya ku mzinda wawo omwe wa Nazarete. 40Ndipo Mwanayo anakula ndi kulimbika [mu mzimu], wodzazidwa ndi nzeru, ndipo chisomo cha Mulungu5 chinali pa Iye.
41Ndipo makolo ake amapita ku Yerusalemu chaka ndi chaka kuphwando la pasaka. 42Ndipo pamene Iye anakwanitsa zaka khumi ndi ziwiri, iwo anapita [ku Yerusalemu] molingana ndi mwambo wa phwando 43ndipo anamaliza masiku awo, koma pamene amabwerera, mnyamatayo Yesu anatsalira m’mbuyo ku Yerusalemu, ndipo makolo ake sanadziwe [za chimenechi]; 44koma, anaganiza kuti Iye ali nawo pamodzi pa ulendo, ndipo anayenda ulendo wa tsiku limodzi, ndipo anamuyang‘ana mwa achibale ndi anansi: 45ndipo pamene sanamupeze Iye anapita ku Yerusalemu kukamufuna. 46Ndipo kunachitika, patapita masiku atatu anampeza Iye mkachisi, atakhala pakati pa aphunzitsi ali kuwamvera iwo komanso kuwafunsa mafunso. 47Ndipo iwo onse amene anamumva Iye anali odabwa ndi chidziwitso chake komanso mafunso ake. 48Ndipo pamene iwo anamuona Iye anali odabwa: ndipo amayi wake anati kwa Iye, Mwana Iwe, chifukwa chiyani wachita ichi kwa ife? Taona, bambo ako ndi ine takhala tikukufunafuna Iwe mwa nkhawa. 49Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chiyani munali kundifunafuna Ine? Kodi simudziwa kuti Ine ndikuyenera [kukhala] mu zochitika za Atate wanga? 50Ndipo iwo sanamvetse kalikonse kamene Iye ananena kwa iwo. 51Ndipo Iye anapita nawo nafika ku Nazarete, ndipo Iye anawamvera iwo. Ndipo amayi wake anazisunga izi zonse mumtima mwawo. 52Ndipo Yesu anakulabe mu nzeru, ndi msinkhu, ndi m’kukonderedwa ndi Mulungu6 komanso anthu.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu