Mutu

1Mkuluyo, kwa mkazi wosankhika ndi ana ake, amene ndamukonda m’choonadi, ndipo osati ine ndekha komanso onse amene adziwa choonadi, 2pachifukwa cha choonadi chimene chikhala mwa ife ndipo chidzakhala ndi ife kwamuyaya. 3Chisomo chidzakhala ndi inu, chifundo, mtendere zochokera kwa Mulungu1 Atate, ndi kwa Ambuye Yesu Khristu, Mwana wa Atate, m’choonadi ndi chikondi.

4Ndinakondwera kwambiri kuti ndapeza ana anu akuyenda m’choonadi, monga ife talandira lamulo kuchokera kwa Atate. 5Ndipo tsopano ndikupemphani, mkazi wosankhika inu, osati kukulemberani lamulo latsopano, koma kuti chimene ife tinali nacho kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mzake. 6Ndipo chimenechi ndicho chikondi, kuti tikayende molingana ndi malamulo ake. Limeneli ndi lamulo, molingana ndi m’mene munamvera kuyambira pachiyambi, kuti mukayende mu limenelo. 7Pakuti onyenga ambiri apita m’dziko lapansi, iwo amene savomereza Yesu Khristu kuti anabwera mthupi — ameneyu ndi wonyenga ndi wokana Khristu. 8Muzipenyere nokha, kuti tisataye chimene tachichita, koma tikalandire mphoto yonse. 9Yense wakupita chitsogolo koma osakhala m’chiphunzitso cha Khristu alibe Mulungu. Iye wakukhala m’chiphunzitso, ali naye Atate komanso Mwana. 10Ngati wina adza kwa inu ndipo sanabweretse chiphunzitso chimenechi, musamulandire mnyumba zanu, ndipo musamlonjere; 11pakuti iye amene amlonjera ayanjana nazo ntchito zake zoipa.

12Pokhala nazo zambiri zolembera kwa inu, Sinditero ndi kaIata ndi kapezi; koma ndiyembekezera kubwera kwa inu, ndi kulankhulana pakamwa ndi pakamwa, kuti chimwemwe chathu chikachulukire.

13Ana a mchemwali wanu wosankhika akukulonjerani.

1Elohimu