Mutu 4

1Tidzanena chiyani pamenepo kuti kholo lathu Abrahamu molingana ndi thupi anapeza chiyani? 2Pakuti ngati Abrahamu analungamitsidwa pa mfundo ya ntchito, pamenepo iye ali nacho chodzitamandira: koma osati pamaso pa Mulungu1; 3pakuti malembo anena kuti chiyani? Ndipo Abrahamu anakhulupilira Mulungu2, ndipo kunawerengedwa kwa iye ngati kulungama. 4Tsopano kwa iye amene agwira ntchito mphoto yake siiwerengedwa monga ngati chisomo, koma ya malipiro: 5koma kwa iye amene sagwira ntchito, koma akhulupilira pa Iye amene amalungamitsa ochimwa, chikhulupiliro chake chiwerengedwa ngati kulungama. 6Monga umo Davide analengezanso kudalitsika kwa munthu amene Mulungu3 amuyesa wolungama popanda kugwira ntchito: 7Odala [iwo] amene kusaweruzika kwao kwakhululukidwa, ndipo machimo awo akwiliridwa: 8wodala munthu amene Ambuye sadzamuwerengera konse uchimo.

9[Kodi] pamenepo mdalitso umenewu [utsamira] pa wodulidwa, kapenanso pa wosadulidwa? Pakuti timanena kuti chikhulupiliro chawerengedwa kwa Abrahamu monga kulungama. 10Nanga pamenepo chawerengedwa bwanji? Pamene iye anali mumdulidwe, kapena m’kusadulidwa? Osati mu mdulidwe, koma m’kusadulidwa. 11Ndipo iye analandira chizindikiro cha mdulidwe [ngati] chitsimikizo cha kulungama kwa chikhulupiliro chimene anali nacho mkusadulidwa, kuti akakhale kholo la iwo onse amene akhulupilira ali osadulidwa, kuti kulungama kukawerengedwe kwa iwonso; 12ndi kholo la odulidwa, osati kwa iwo amene anangochita mdulidwe, koma kwa iwonso amene ayenda m’mayendedwe a chikhulupiliro, munthawi ya kusadulidwa, kwa kholo lathu Abrahamu.

13Pakuti [sizinali] monga mwa lamulo kuti lonjezano linaperekedwa kwa Abrahamu, kapena ku mbeu yake, kuti akakhale olowa m’malo a dziko lapansi, koma mwa kulungama kwa chikhulupiliro. 14Pakuti ngati iwo amene ali a lamulo akhala olowa m’malo, chikhulupiliro chikhala chopanda pake, ndipo lonjezo likhala lopanda pake. 15Pakuti lamulo linabweretsa mkwiyo; komatu pamene palibe lamulo palibe kulakwa. 16Pamenepo mfundo ndi ya chikhulupiliro, kuti [zikakhale] molingana ndi chisomo, cholinga kuti lonjezano likhale lotsimikizika ku mbeu yonse, osati kwa okhawo amene ali a lamulo, komanso kwa amene ali ndi chikhulupiliro cha Abrahamu, amene ali kholo la tonse, 17(kulingana ndi momwe kunalembedwa, Ndakupanga iwe kukhala kholo la mitundu yambiri,) pamaso pa Mulungu4 amene iye anamkhulupilira, amene amaukitsa akufa, ndi kuitana zinthu zoti palibe monga zilipo; 18ameneyo motsutsana ndi chiyembekezo anakhulupilira m’chiyembekezo kukhala kholo la mitundu yambiri, molingana ndi chimene chinalankhulidwa, Kotero mbewu yako idzakhala: 19ndipo osati kukhala ofooka m’chikhulupiliro, sanaliyese thupi lake lomwe kukhala lakufa kale, pokhala ndi zaka pafupifupi zana limodzi, ndi kuumanso kwa mimba ya Sara, 20ndipo sanakayike ku lonjezano la Mulungu5 pokhala osakhulupilira; koma anapeza mphamvu m’chikhulupiliro, kupereka ulemelero kwa Mulungu6; 21ndipo atatsimikizika kwathunthu kuti zimene analonjeza ali nako kuthekeranso kuzichita; 22Pameneponso kunawerengedwa kwa iye monga kulungama. 23Tsopano sikunalembedwe chifukwa cha iye yekha kuti kunawerengedwa kwa iye, 24koma kwa ifenso, amene pokhulupilira pa Iye amene anaukitsidwa pakati pa akufa Yesu Ambuye wathu, 25amene anaperekedwa chifukwa cha machimo athu ndipo anaukitsidwa pa kulungamitsidwa kwathu, kumene kuwerengedwa.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu