Mutu 12
1Chabwino, zilibe phindu kwa ine kuzitamandira, pakuti ndizadza ku masomphenya ndi mavumbulutso a Ambuye. 2Ndidziwa munthu wa mwa Khristu, zaka khumi ndi zinayi zapitazo, (kaya m’thupi sindidziwa, kapena kunja kwa thupi sindidziwa, 1Mulungu adziwa;) amene anakwatulidwa kupita kumwamba kwachitatu. 3Ndipo ine ndimdziwa munthu wotereyu, (kaya mthupi kapena kunja kwa thupi sindidziwa konse, 2Mulungu adziwa;) 4kuti anakwatulidwa kupita ku paradizo, ndipo anamva zinthu zosasimbika zikunenedwa zimene siziyenera munthu kuzilankhula. 5Kwa wotereyu ine ndizazitamandira, koma za ine ndekha sindizazitamandira, pokhapokha m’zifooko zanga. 6Pakuti ngati ndidzafuna kuzitamandira, sindidzakhala wopusa; pakuti ndidzanena choonadi; koma ndiziletsa, kuti wina azaganiza kwa ine kukhala woposa chimene akuona mwa ine kukhala, kapena chilichonse chimene adzamva za ine. 7Ndipo kuti ndisakwezedwe ndi kuchuluka kwa kukula kwa mavumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga wa mthupi, mtumiki wa Satana kuti anditutunduze ine, kuti ndisakwezedwe koposa. 8Pakuti pa chimenechi katatu konse ndinafuna Ambuye kuti mungawu uchoke kwa ine. 9Ndipo Iye anati kwa ine, Chisomo changa chikukwanire iwe; pakuti mphamvu yanga ilimbika m’chifooko. Makamaka ndidzanyada pamenepo m’chifooko changa, kuti mphamvu ya Khristu ikakhale pa ine. 10Pamenepo ndikondwera ine m’chifooko, m’kunyozedwa, m’zikakamizo, m’masautso, m’zipsinjo, chifukwa cha Khristu: pakuti pamene ine ndifooka, pamenepo ndili ndi mphamvu.
11Ine ndasanduka wopusa; inuyo mwandichititsa ine kutero; pakuti ine ndinavomerezedwa ndi inu; pakuti ndakhala wopanda phindu kwa iwo amene anali atumwi opambana, ngatinso ine ndikhala wopanda pake. 12Zizindikirotu za mtumwi zinachitika pakati panu m’chipiliro chonse, m’zizindikiro, ndi m’zodabwitsa, ndi ntchito za mphamvu. 13Pakuti ndi chiyani chimene mwachepa nacho ku mipingo inayo, pokhapokha kuti inenso mwini sindinakhale waulesi kukusautsani inu? Ndikhululukireni chifukwa cha choipa ichi. 14Taonani, nyengo iyi yachitatu ndili wokonzeka kufika kwa inu, ndipo sindizakusautsani; pakuti ine sindifuna zinthu zanu, koma inu; pakuti ana safuna kuunjikira makolo, komatu makolo kuunjikira ana. 15Tsopano mokondwera ndidzagwiritsa ndi kupereka pa miyoyo yanu, ngakhale moonjeza kukukondani inu kuti ine ndikondedwe pang’ono.
16Koma zikhale momwemo. Ine sindinakulemetsani inu, koma pokhala wochenjera ndinakugwirani ndi chinyengo. 17Kodi ndinakuchitirani phindu lililonse pa iwo amene ndinawatuma kwa inu? 18Ndinamupempha Tito, ndi kumtumizira m’bale iye: kodi Tito anakulemetsani inu? Kodi sitinayende limodzi mu mzimu yemweyu? Kodi sitinayende m’mapazi omwewa?
19Inu mwakhala mukuganiza kwa nthawi kuti ife timawiringula kwa inu: tilankhula pamaso pa 3Mulungu mwa Khristu; ndi zinthu zonse, wokondedwa, kuti zikumangilireni. 20Pakuti ine ndichita mantha pamenepo kuti pakubwera ine ndisadzakupezeni monga ndiganiza, ndipo kuti ndisapezeke ine monga inu muganiza: kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mkwiyo, zilekanitso, kulankhula moipa, manong’onong’o, maugogodi, zisokonezo; 212kuti 4Mulungu wanga angandichepetse monga kwa inu pamene ndidzabweranso, ndi kuti ndingalilire ambiri amene anachimwa pachiyambi, ndipo sanalape monga mwa chidetso ndi chigololo ndi kukhumba zonyansa zimene anachita.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu