Mutu 20
1Ndipo kunachitika kuti tsiku lina, pamene Iye amaphunzitsa anthu m’kachisi, ndi kulalikira uthenga wabwino, ansembe akulu ndi alembi pamodzi ndi akulu anabwera, 2ndipo analankhula kwa Iye nanena, Tiuzeni mukuchita zinthu izi ndi ulamuliro wa ndani, kapena ndi ndani amene anakupatsani ulamuliro umenewu? 3Ndipo Iye poyankha anati kwa iwo, Inenso ndikufunseni chinthu [chimodzi], ndipo mundiuze: 4Ubatizo wa Yohane, unali wochokera kumwamba kapena wa anthu? 5Ndipo iwo anatsutsana mwa iwo okha, nanena, Ngati tinena kuti, Wakumwamba, Iye anena kuti, Chifukwa chiyani simunamkhulupirire iye? 6koma ngati tinena, Wa anthu anthu atigenda miyala, pakuti iwo anakopeka mtima kuti Yohane anali mneneri. 7Ndipo iwo anayankha, sakudziwa kumene uchokera. 8Ndipo Yesu anati kwa iwo, Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndimapangira zinthu zimenezi.
9Ndipo Iye anayamba kulankhula kwa anthu fanizo ili: Munthu analima munda wa mpesa ndipo anaubwereketsa kwa anthu olima m’munda, ndipo anachoka m’dzikolo kwa nthawi yaitali. 10Ndipo mu nyengo yake iye anatumiza kapolo kwa anthu olima m’munda aja, kuti akamupatse iye zipatso za mpesa; koma olima m’munda aja, anamumenya, nam’bweza [iye] wopanda kanthu. 11Anatumanso kapolo wina; koma iwo, atamumenyanso, anam‘nenera chipongwe, nam’bweza [iye] wopanda kanthu. 12Ndipo anatumanso wachitatu; ndipo iwo, anampwetekanso, namponya [iye] kunja. 13Ndipo mbuye mwini wa munda anati, Ndidzachita chiyani? Ndidzatumiza mwana wanga wokondedwa: kapena mwina akamuona adzampatsa [iye] ulemu. 14Koma pamene anthu olima m’munda aja anamuona anauzana pakati pawo, nanena, Uyu ndiye wolowa m’malo; [bwerani,] tiyeni timuphe iye, kuti cholowacho chikhale chathu. 15Ndipo anamutulutsa kunja kwa munda wa mpesa, namupha [iye]. Kodi mbuye wa munda wa mpesa adzachita chiyani kwa iwo? 16Iye adzabwera ndi kuwaononga olima m’mundawo, ndipo adzaupereka mundawo kwa ena. Ndipo pamene iwo anamva izi anati, Zisakhale choncho! 17Koma pamene anawayang’ana iwo anati, Kodi ndi chiyani ichi chimene chalembedwa, Mwala umene iwo omanga anaukana, umenewu wasanduka wa pangodya? 18Aliyense wakugwera pa mwala umenewu adzathyoka, koma amene mwalawu udzamgwera udzamupera ngati ufa.
19Ndipo alembi ndi ansembe akulu anafuna ola lomwelo kumgwira Iye, ndipo iwo anaopa anthu; pakuti iwo anadziwa kuti fanizoli amanena za iwo.
20Ndipo anamuyang’anira [iye], natumiza anthu omuzonda, nazizembaitsa ngati anthu achilungamo, kuti akamukole ndi mau otuluka mkamwa [mwake], cholinga kuti akamupereke ku mphamvu ndi ulamuliro wa kazembe. 21Ndipo anamufunsa Iye nanena, Mphunzitsi, ife timadziwa kuti mumalankhula ndi kuchita molondola, ndipo simusamala nkhope ya [munthu], koma mumaphunzitsa ndi choonadi njira ya Mulungu1: 22Kodi ndi koyenera kwa ife kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena ayi? 23Koma Iye pozindikira chinyengo chawo anati kwa iwo, Chifukwa chiyani mukundiyesa? 24Ndionetseni rupiya la theka. Chithunzithunzi ndi cholemba chake ndi zandani? Ndipo poyankha iwo anati, za Kaisara. 25Ndipo anati kwa iwo, Lipirani pamenepo za Kaisara kwa Kaisara ndi za Mulungu2 kwa Mulungu3. 26Ndipo iwo sanakwanitse kumugwira iye m’malankhulidwe [ake] pamaso pa anthu, ndipo podabwa ndi mayankhidwe ake, iwo anakhala chete.
27Ndipo ena mwa Asaduki, amene amakana kuti kulibe kuukitsidwa kwa akufa, anabwera [kwa iye], 28namfunsa Iye nanena, Mphunzitsi, Mose anatilembera kwa ife, ngati wina m’bale wake amwalira, amene anali naye mkazi, ndipo analibe mwana, m’bale wake amtenge mkaziyo namuwukitsire mbewu m’bale wakeyo. 29Analipo abale asanu ndi awiri: ndipo woyamba, atazitengera mkazi anamwalira wopanda mwana; 30ndipo wachiwiri [anamtenga mkaziyo, ndipo iye anamwalira wopanda mwana]; 31ndipo wachitatu anamutenga iye: ndiponso momwemo wachisanu ndi chiwiri anamwalira namsiya wopanda ana; 32ndipo kumapeto kwake mkaziyo anamwaliranso. 33M’kuuka pamenepo ndani mwa iwowa adzakhala mkazi wake, pakuti onsewa asanu ndi awiri anamutenga ngati mkazi wao? 34Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ana a padziko pano amakwatira ndi kukwatiwa, 35koma iwo amene amawerengedwa kukhala oyenera kukhala ndi gawo mu dziko lija, ndi kuuka kwa akufa, samakwatira kapena kukwatiwa; 36pakuti iwo samamwalira konse, pakuti afanana ndi angelo, ndipo ali ana a Mulungu4, kukhala ana a kuuka kwa akufa. 37Komatu kuti akufa adzauka, Mose anaonetsera mu [gawo la] chitsamba chija, pamene anamutchula Ambuye Mulungu5 wa Abrahamu ndi Mulungu6 wa Isake ndi Mulungu7 wa Yakobo; 38koma Iye si Mulungu8 wa akufa koma wa amoyo; pakuti anthu onse akhala moyo kwa Iye. 39Ndipo ena mwa alembi anamuyankha nati, Mphunzitsi, mwalankhula bwino. 40Pakuti iwo sanayeserenso kumufunsa kalikonse.
41Ndipo Iye anati kwa iwo, Amanena bwanji kuti Khristu ndi mwana wa Davide, 42ndipo Davide mwini anati m’buku la Masalmo, Ambuye anati kwa Ambuye wanga, Khala kudzanja langa lamanja 43kufikira nditayika adani ako [monga] chopondera cha mapazi ako? 44Davide pamenepo anamutchula Iye Ambuye, ndipo akhala bwanji mwana wake?
45Ndipo pamene anthu onse amavetsera, Iye anati kwa ophunzira ake, 46Chenjerani ndi alembi, amene amakonda kuyenda mu mikanjo italiitali, ndipo amakonda kulonjeredwa m’misika, ndipo amakhala mipando ya ulemu m’sunagoge, ndi mipando ya ulemu ku maphwando; 47amaononga nyumba za akazi a masiye, ndipo monyenga amapemphera mapemphero ataliatali. Amenewa adzalandira chilango choopsa.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu