Mutu 10
1Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, Iye amene salowera pakhomo mkhola la nkhosa, koma alowera kwina, ameneyu ndi wakuba ndi wolanda; 2koma iye wakulowera pakhomo ndiye m’busa wa nkhosa. 3Kwa iyeyu wapakhomo amtsegulira; ndipo nkhosa zimamva mau ake; ndipo iye amaziyitana nkhosa zake ndi maina awo, ndipo amadzitsogolera. 4Pamene iye asonkhanitsa zake zomwe, azitsogolera, ndipo nkhosa zimtsatira iye, chifukwa zimadziwa mau ake. 5Koma izo sizitsatira mlendo, koma zimthawa iye, chifukwa sizidziwa mau a alendo. 6Fanizo ili Yesu analankhula kwa iwo, koma sanadziwe zimene Iye amalankhula kwa iwo.
7Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, Ine ndine khomo la nkhosa. 8Onse amene anabwera Ine ndisanabwere ndi akuba ndi olanda; koma nkhosa sizinawamve iwo. 9Ine ndine khomo: aliyense wolowa mwa Ine, adzapulumuka, ndipo adzalowa ndi kutuluka ndipo adzapeza msipu. 10Wakuba samabwera komatu kuti akabe, ndi kupha, ndi kuononga: Ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, ndipo akakhale nawo wochuluka. 11Ine ndine m’busa wabwino. M’busa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa: 12koma iye wotumikira chifukwa cha malipiro, ndipo kuti m’busa, amene nkhosazo sizake, akaona mbulu ukubwera, ndipo amasiya nkhosa ndi kuthawa; ndipo mbulu umamwaza nkhosazo. 13Iye amene amatumikira chifukwa cha malipiro, ndipo iye mwini sasamala za nkhosa. 14Ine ndine m’busa wabwino; ndipo Ine ndimawadziwa iwo amene ali anga, ndipo ndimadziwika mwa iwo amene ali anga, 15monga Atate andidziwa Ine ndi Ine ndidziwa Atate; ndipo ndipereka moyo wanga chifukwa cha nkhosa. 16Ndipo ndili nazo nkhosa zina zimene sizili za khola ili: zimenezo ndiyeneranso kuzitenga, ndipo zidzamva mau anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, m’busa m’modzi. 17Pachifukwa chimenechi Atate andikonda Ine, chifukwa ndataya moyo wanga kuti ndikautengenso. 18Palibe amene autenga kwa Ine, koma ndiupereka ndekha. Ine ndili nawo ulamuliro wakuutaya komanso ndili nawo ulamuliro wakuutenga. Ndalandira lamulo limeneli kwa Atate wanga. 19Panali kugawikana pakati pa Ayuda pokhudza mau amenewa; 20koma ambiri a iwo anati, Ali ndi chiwanda komanso misala; chifukwa chiyani mukumvera Iye? 21Ena anati, Malankhulidwe awa simalankhulidwe a munthu wogwidwa ndi chiwanda. Kodi chiwanda chikhoza kutsegula maso a anthu akhungu?
22Tsopano phwando la kukonzetsa limakondwereredwa ku Yerusalemu, ndipo inali nyengo yozizira. 23Ndipo Yesu anali kuyenda m’kachisi m’khumbi la Solomo. 24Pamenepo Ayuda anamzungulira Iye, ndipo anati kwa Iye, Kufikira liti mudzasunga moyo wathu m’malere? Kodi ndinu Khristu, nenani [ichi] kwa ife poyera. 25Yesu anawayankha iwo, Ndakuuzani inu, ndipo simukukhulupilira. Ntchito zimene ndichita m’dzina la Atate wanga, zimenezi zindichitira umboni wokhudza Ine: 26koma inu simukhulupilira, pakuti inu si nkhosa zanga, monga ndakuuzani. 27Nkhosa zanga zimva mau anga, ndipo ndimazidziwa, ndipo zimanditsatira Ine; 28ndipo ndimadzipatsa moyo wosatha; ndipo sizizaonongedwa, ndipo palibe angazilande kuchoka m’manja mwanga. 29Atate wanga amene wazipereka [izo] kwa Ine ndi wamkulu kuposa onse, ndipo palibe amene angazilande kuchoka m’manja mwa Atate wanga. 30Ine ndi Atate ndife amodzi.
31Pameneponso Ayuda anatenga miyala kuti amugende Iye. 32Yesu anawayankha iwo, Ntchito zabwino zambiri za Atate wanga ndakuonetserani inu; ndi ntchito iti imene mukundigendera Ine? 33Ayuda anamuyankha Iye, Chifukwa cha ntchito yabwino sitikugendani Inu, koma chifukwa cha mwano, ndipo chifukwa Inu, pokhala munthu, mukuzipanga nokha kukhala Mulungu1. 34Yesu anawayankha iwo, Kodi sizinalembedwe mu lamulo lanu, Ine ndinena, ndinu milungu2? 35Ngati Iye anawatchula iwo milungu3 kwa Iye amene mau a Mulungu4 anachokera (ndipo malemba sangathe kuphwanyidwa), 36kodi mukhoza kunena za Iye amene Atate anampatula ndi kumtumiza m’dziko lapansi, Ndiwe wa mwano, chifukwa Ine ndinati, Ndine Mwana wa Mulungu5? 37Ngati Ine sindichita ntchito za Atate wanga, musandikhulupilire; 38koma ngati ndichita, ngakhale kuti simundikhulupilira Ine, khulupilirani ntchitozo, kuti mukadziwe [ndi kukhulupilira] kuti Atate ali mwa Ine ndipo Ine ndili mwa Iye. 39Iwo anafunanso kumgwira Iye; ndipo Iye anawachokera m’dzanja lawo 40ndipo anapitanso kutsidya la Yordano kumalo kumene Yohane amabatiza poyamba: ndipo Iye anakhala kumeneko. 41Ndipo ambiri anabwera kwa Iye, nanena, Yohane sanachite chizindikiro; koma zinthu zonse zimene Yohane analankhula za [munthu] uyu zinali zoona. 42Ndipo ambiri kumeneko anakhulupilira pa Iye.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu