Mutu 13
1Tsopano lisanafike phwando la pasaka, Yesu, podziwa kuti ola lake lafika kuti achoke padziko lapansili kupita kwa Atate, m’mene anawakonda ake omwe amene anali m’dziko lapansi, anawakonda iwo kufikira chimaliziro. 2Ndipo pa nthawi ya mgonero, mdierekezi anayikiratu mu mtima mwa Yudase [mwana] wa Simoni, Iskariote, kuti akampereke Iye, 3 [Yesu,] podziwa kuti Atate anampatsa Iye zinthu zonse m’manja mwake, ndipo kuti anachokera kwa Mulungu1, 4ananyamuka pa mgonero nachotsa zofunda zake, ndipo pamene anatenga chopukutira anachimanga m’chiuno mwake: 5kenako anathira madzi m’mbale yosambira m’manja, ndipo anayamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndipo anawapukuta iwo ndi chopukutira chimene anamanga m’chiuno chija. 6Iye anabwera kwa Simoni Petro; ndipo iye anati kwa Yesu, Ambuye, kodi Inu nkusambitsa mapazi anga? 7Yesu anayankha nati kwa iye, Chimene ndikuchita sungachidziwe pano, koma udzachidziwa mtsogolo. 8Petro anati kwa Iye, Inu simungasambitse mapazi anga. Yesu anamyankha iye, Pokhapokha ndikusambitse iwe, sudzakhala nalo gawo ndi Ine. 9Simoni Petro anati kwa Iye, Ambuye, osati mapazi anga okha, komanso manja anga ndi mutu wanga. 10Yesu anati kwa iye, Amene wasambitsidwa thupi lonse sakufunikanso kusamba koma mapazi okha, ndipo ndi woyeretsedwa; ndinutu oyera koma osati nonse ayi. 11Pakuti Iye anadziwa amene adzampereka: pa chifukwa chimenechi Iye anati, Simuli oyera nonse. 12Pamene Iye anawasambitsa mapazi awo, anatenga zofunda zake, nakhalanso pansi, nati kwa iwo, Kodi mukudziwa chimene ndapanga kwa inu? 13Inu mundiitana Ine Mphunzitsi ndi Ambuye, ndipo munena bwino, pakuti ndine amene. 14Pamenepo ngati Ine, Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, nanunso mukuyenera kusambitsana mapazi wina ndi mzake; 15pakuti ndakupatsani chitsanzo chimenechi, monga ndachitira kwa inu, muchitenso chimodzimodzi. 16Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu. Kapolo saposa mbuye wake, kapena wotumidwa saposa iye amene wamtumayo. 17Ngati inu mukudziwa zinthu zimenezi, odala muli inu ngati muchita zimenezi. 18Sindikulankhula za inu nonse. Ine ndikudziwa amene ndawasankha; koma kuti lemba likwanitsidwe, Iye amene akudya mkate ndi Ine watukulira dendene lake pa Ine. 19Ndikuuzani pano zisanachitike, kuti zikazachitika, mukakhulupilire kuti ndine amene. 20Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, Iye wolandira amene ndimtuma alandira Ine; ndipo amene alandira Ine alandira amene anandituma Ine.
21Atalankhula zinthu izi, Yesu anavutika mu mzimu, ndipo anachitira umboni nanena, Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, kuti m’modzi wa inu adzandipereka Ine. 22Pomwepo ophunzira anayang’anizana wina ndi mzake, podabwa kuti akunena ndani. 23Tsopano pa gome m’modzi wa ophunzira ake anatsamira pa chifuwa cha Yesu, ameneyu ndiye amene Yesu anamkonda. 24Simoni Petro anamkodola pamenepo namfunsa kuti akhoza kukhala ndani amene Iye akunenayo. 25Koma iye, pamene anatsamira pachifuwa cha Yesu, anati kwa Iye, Kodi ndi ndani? 26Yesu anayankha, Iye amene, ndikasusa nthongo yanga, ndi kumpatsa. Ndipo atasusa nthongo, anapereka kwa Yudase [mwana] wa Simoni, Isikariote. 27Ndipo, atalandira nthongo, pomwepo Satana analowa mwa iye. Pamenepo Yesu anati kwa iye, Chimene ukufuna kuchita, chita mwachangu. 28Koma palibe wakukhala pa gome amene anadziwa chifukwa chiyani analankhula izi kwa iye; 29pakuti ena anaganiza, chifukwa Yudase amasunga thumba, kuti Yesu analankhula kwa iye, Kagule zinthu zimene tikufunikira pa phwando; kapenanso kuti akapereke kenakake kwa osauka. 30Pamenepo atalandira nthongo, anatuluka nthawi yomweyo; ndipo unali usiku.
31Pamene iye anatuluka panja Yesu anati, Tsopano Mwana wa munthu walemekezedwa, ndipo Mulungu2 walemekezedwa mwa Iye. 32Ngati Mulungu3 walemekezedwa mwa Iye, Mulungu4 adzamulemekezanso Iye mwa Iye yekha, ndipo adzamlemekeza nthawi yomweyo. 33Ana inu, komabe katsala kanthawi kochepa pamene ndili ndi inu. Mudzandifunafuna; ndipo, monga ndinanena kwa Ayuda, Kumene Ine ndipita simungathe kubwerako, ndinenanso kwa inu tsopano. 34Lamulo latsopano ndikupatsani inu, kuti mukondane wina ndi mzake; monga Ine ndakukondani inu, kuti nanunso mukondane wina ndi mzake. 35Mwa ichi anthu onse azadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukhala ndi chikondi pakati panu. 36Simoni Petro anati kwa Iye, Ambuye, mukupita kuti? Yesu anamuyankha iye, Kumene ndipita sungathe kunditsatira pano, koma udzanditsatira bwino lake. 37Petro anati kwa iye, Ambuye, chifukwa chiyani sindingathe kukutsatirani pano? Ine ndidzataya moyo wanga chifukwa cha Inu. 38Yesu anayankha, Udzataya moyo wako chifukwa cha Ine! Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa iwe, Tambala asanalire udzandikana Ine katatu.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu