Mutu 18
1Mu nthawi yomweyo ophunzira anabwera kwa Yesu, nanena, Nanga ndi ndani amene ali wamkulu mu ufumu wakumwamba? 2Ndipo Yesu atadziyitanira kwa [Iye] mwana wamng’ono, anamuika pakati pawo, 3ndipo anati, Indetu ndinena kwa inu, Pokhapokha inuyo mutembenuke ndi kukhala ngati mwana wamng‘ono, simudzatha konse kulowa ufumu wakumwamba. 4Kotero aliyense amene adzichepetsa yekha ngati mwana wamng’ono uyu, iye ali wamkulu mu ufumu wakumwamba; 5ndipo aliyense amene adzalandira mwana wamng’ono chotere m’dzina langa, walandira Ine. 6Koma iye amene adzakhumudwitsa m’modzi wa ana ang’ono amene amakhulupirira mwa Ine, kukanakhala bwino kwa iye kumangidwa mwala wa mphero pakhosi pake ndipo aponyedwe pakuya m’nyanja. 7Tsoka padziko lapansi chifukwa cha zolakwika! Pakuti ndikofunikira ndithu kuti zolakwikazo zibwere; komabe tsoka lili kwa munthu amene amabweretsa zolakwikazo! 8Ndipo ngati dzanja lako kapena phazi lako likuchimwitsa iwe, ulidule ndi kulichotsa [ilo] kwa iwe; n’kwabwino kwa iwe kukalowa m’moyo wolumala kapena woduka chiwalo, [kusiyana] ndi kukhala ndi manja awiri kapena mapazi awiri ndi kuponyedwa m’moto wamuyaya. 9Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa iwe, likolowole ndi kulichotsa [ilo] kwa iwe; n’kwabwino kwa iwe kulowa m’moyo ndi diso limodzi, [kusiyana] ndi kukhala ndi maso awiri koma ndi kukaponyedwa m’gehena wa moto. 10Onetsetsani kuti simukunyoza m’modzi wa ana ang’ono awa; pakuti ndinena kwa inu kuti angelo awo kumwamba apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga amene ali kumwamba. 11Pakuti Mwana wa munthu wabwera kudzapulumutsa chimene chili chotayikacho. 12Kodi mukuganiza bwanji inu? Ngati munthu ali nazo nkhosa zana limodzi, ndipo imodzi mwa izo isochera, kodi iye, samasiya makumi asanu ndi anayi kudza mphambu zisanu ndi zinayi pa phiri, napita ndi kufunafuna imodzi yosocherayo? 13Ndipo zikachitika kuti iye waipeza, zoonadi ndinena kwa inu, amakondwera kwambiri chifukwa cha iyo koposa nkhosa makumi asanu ndi anayi kudza mphambu zisanu ndi zinayi zimene sizinasokerezo. 14Chotero sichifuniro cha Atate wanu amene ali kumwamba kuti m’modzi wa ana ang’ono awa akaonongeke.
15Komatu ngati m’bale wanu akuchimwirani, pitani, mlangizeni iye pakati pa inu awiri nokha. Ngati angakumvereni inu, mwam’bweza m’bale wanu. 16Koma ngati samvera [iye], tengani m’modzi kapena awiri pambali kuti akhale mboni, kuti kalikonse kakaimikike pa mau a mboni ziwiri kapena zitatu. 17Komabe ngati samvera iwo, uzani mpingo; ndiponso ngati samvera mpingowo, ameneyu kwa inu akhale ngati m’modzi wa amitundu ndi wokhometsa msonkho. 18Zoonadi ndinena kwa inu, Chilichonse chimene mudzamanga padziko lapansi chidzakhalanso chomangidwa kumwamba, ndipo chilichonse chimene mudzamasula padziko lapansi chidzamasulidwanso kumwamba. 19Ndinenanso kwa inu, kuti ngati awiri adzagwirizana padziko lapansi kanthu kalikonse, kalikonse kamene adzapempha, kadzapatsidwa kwa iwo kuchokera kwa Atate wanga amene ali kumwamba. 20Pakuti kumene awiri kapena atatu asonkhanira m’dzina langa, kumeneko Ine ndidzakhala pakati pawo.
21Pamenepo Petro anabwera kwa Iye nanena, Ambuye, kodi m’bale wanga andichimwire kochuluka bwanji kuti ine ndimkhululukire iye? Kasanu ndi kawiri? 22Yesu anati kwa iye, Sindinena kwa inu kuti kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi asanu ndi awiri kuchulukitsa kasanu ndi kawiri. 23Pachifukwa chimenechi ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inafuna kuwerengera ndi akapolo ake. 24Ndipo pakuyamba kuwerengera, wa ngongole wina ya matalente mazana khumi anabwera naye kwa iye. 25Koma atasowa chobwezera, mbuye [wake] anamulamula kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wake yemwe, ndi ana ake omwe, komanso kalikonse kamene anali nako kuli abweze ngongoleyo. 26Kotero kapoloyo pakugwada pansi ndi kumpembedza iye, analankhula, Ambuye, bandilezerani mtima ine ndipo ndikubwezerani zonse. 27Ndipo mbuye wa kapoloyo, pakukhudzika ndi chifundo, anam’masula iye ndipo anam’khululukira ngongole yake. 28Koma kapoloyu pakutuluka panja anampeza m’modzi wa kapolo mzake amene anamungongoza iye marupiya a theka zana limodzi. Ndipo atamugwira iye, anamkanyanga pakhosi, nati, Undilipire [ine] ngati uli nane ngongole iliyonse. 29Kenako kapolo mzakeyo pakugwada pansi [pa mawondo ake], anamudandaulira iye, nanena, Ubandilezera mtima, ndipo ine ndidzakubwezera. 30komatu iye sanatero, koma anachoka namponya iye m’nyumba ya ndende, kufikira atapereka zonse zimene anangongola. 31Koma akapolo amzake, ataona zimene zinachitikazi, anamva chisoni chachikulu, ndipo anapita namfotokozera mbuye wao zonse zimene zinachitika. 32Pamenepo mbuye wake, atamuitana, anati kwa iye, Kapolo woipa! Ine ndakukhululukira ngongole zonse chifukwa unandipempha ine; 33sukanatha nawenso kukhala ndi chifundo pa kapolo mzakoyu, monga ine ndinakhala ndi chifundo ndi iwe? 34Ndipo mbuye wake pakupsya naye mtima anampereka kwa anthu ozunza kufikira atabweza zonse zimene anamungongoza iye. 35Chimodzimodzinso Atate wanga wakumwamba adzachitira inu ngati simukhululukira aliyense wa abale anu m’mitima mwanu.