Mutu 23
1Pamenepo Yesu analankhula kwa makamu ndi ophunzira ake, 2nanena, Alembi ndi Afarisi anaziika okha pa mpando wa Mose: 3kotero zinthu zonse, zimene iwo angakuuzeni inu, chitani ndi kuzisunga. Koma musachite ntchito zao, pakuti iwo amalankhula koma samachita ayi, 4komatu amamangilira katundu wolemetsa ndi wovuta kunyamula, ndipo amaikiza pa mapewa a anthu, koma iwo sangakwanitse kumusuntha ndi chala chao. 5Ndipo ntchito zao zonse iwo amachita kuti aonekere kwa anthu: pakuti amatalikitsa njirisi zao ndi kukulitsa mothera [zovala zao], 6ndipo amakonda malo a ulemu m’maphwando ndi malo oyambilira m’masunagoge, 7ndi kulonjeredwa m’misika, ndi kuitanidwa ndi anthu, Mphunzitsi, Mphunzitsi. 8Koma inu, musamatchulidwa Mphunzitsi; pakuti mlangizi wanu ndi m’modzi, ndipo inu nonse ndinu abale. 9Ndipo musamatchule [wina aliyense] atate wanu padziko lapansi; pakuti Atate wanu ndi m’modzi, Iye amene ali kumwamba. 10Kapenanso kutchulidwa Mlangizi, pakuti pali mlangizi m’modzi, ndiye Khristu. 11Koma wamkulu pakati panu akhale mtumiki wanu. 12Ndipo iye amene adzazikweza yekha adzachepetsedwa, ndipo amene adzazichepetsa yekha adzakwezedwa.
13Koma tsoka kwa inu, alembi ndi Afarisi, achinyengo, pakuti mumatsekera ufumu wakumwamba kwa anthu; pakuti inu simulowamo, kapena mumalepheretsa iwo amene akulowa kuti asalowemo. 15Tsoka kwa inu, alembi ndi Afarisi, achinyengo, pakuti mumayendayenda kunyanja ndi [kumtunda] kumpangitsa wina mtembenuki, ndipo iye akachita [chomwechi], mumampangitsa kawiri konse kukhala mwana wa gehena kuposa inu eni. 16Tsoka kwa inu, atsogoleri akhungu, amene mumati, Iye amene adzalumbira potchula kachisi, palibe kanthu; koma iye amene adzalumbira potchula golide wa mkachisi, iye ali nawo mangawa. 17Opusa ndi akhungu inu, pakuti choposa ndi chiti, golide, kapena kachisi amene amayeretsa golideyo? 18Ndipo, amene adzalumbira potchula guwa, palibe kanthu; koma iye amene adzalumbira pa mtulo woikidwa pamwambapo ali nawo mangawa. 19[Opusa ndi] akhungu inu, pakuti choposa ndi chiti, mtulo, kapena guwa limene limayeretsa mtulowo? 20Chomwecho iye amene amalumbira potchula guwa alumbira pa ilo ndi zonse zopezeka pa guwapo. 21Ndipo Iye wakulumbira potchula kachisi alumbira pa ameneyu ndi iye wakukhala m’menemo. 22Ndipo iye wakulumbira potchula kumwamba alumbira pa mpando wa Mulungu1 ndi Iye wakukhala pamenepo. 23Tsoka kwa inu, alembi ndi Afarisi, achinyengo, pakuti mumapereka chakhumi cha timbeu tonunkhira, ndi tsabola ndi chitowe, koma musiya pambali zinthu zolemera za chilamulo, chiweruzo, ndi chifundo ndi chikhulupiliro: zimenezi munayenera kuchita ndipo simunayenere kuzisiya izo pambali. 24Atsogoleri akhungu inu, amene mumakutumula udzudzu koma mumamwera ngamila. 25Tsoka kwa inu, alembi ndi Afarisi, achinyengo, pakuti mumatsuka kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma mkati mwake mwadzadza ndi kulanda ndi kusadziletsa. 26Mfalisi wakhungu iwe, uyambe watsuka koyamba mkati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera. 27Tsoka kwa inu, alembi ndi Afarisi, achinyengo, pakuti muli ngati manda opaka njereza, amene amaoneka okongola kunja kwake, koma mkati mwadzala ndi mafupa ndi zonyansa zonse. 28Chimodzimodzinso inu, kunja mumaoneka anthu olungama, koma mkati mwadzala ndi chinyengo ndi kusaweruzika. 29Tsoka kwa inu, alembi ndi Afarisi, achinyengo, pakuti mumamanga ziliza za aneneri ndi kulemekeza manda a anthu olungama, 30ndipo mumanena kuti, Tikanakhala ife kuti tinali m’masiku a makolo athu sitikanatenga mbali ndi iwo m’mwazi wa aneneri. 31Kotero inu mumachitira umboni kuti muli ana a iwo amene anapha aneneri: 32ndipo inu, munadzadza mlingo wa makolo anu. 33Njoka inu, mbewu ya mamba, kodi mudzathawa bwanji chiweruzo cha gehena? 34Chomwecho, taonani, Ine ndakutumizirani inu aneneri, ndi anthu a nzeru, ndi alembi; ndipo [ena] mwa iwo mudzawapha ndi kuwapachika, ndipo [ena] mwa iwo mudzawakwapula m’masunagoge anu, ndipo mudzawazunza kuchokera mzinda umodzi kufikira mzinda wina; 35kotero kuti mwazi wonse wolungama wokhetsedwa padziko lapansi udzakhala pa inu, kuyambira mwazi wolungama wa Abele kufikira mwazi wa mwana wa Zakaliya, Barakiya, amene inu munamupha pakati pa kachisi ndi guwa la nsembe. 36Zoonadi ndinena ndi inu, Zinthu zonse izi zidzafikira pa mbadwo umenewu. 37Yerusalemu, Yerusalemu, [mzinda] umene umapha aneneri ndi kugenda iwo amene atumidwa kwa iye, kodi ndi kangati kamene ndasonkhanitsa ana ako monga thadzi lisonkhanitsa ana ake pansi pa mapiko ake, ndipo sumafuna ayi! 38Taonani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja; 39Pakuti ndinena kwa inu, Simudzandionanso Ine kufikira mudzati, wodala iye wakudza m’dzina la Ambuye.
1Elohimu